Watchtower LAIBULALE YA PA INTANETI
Watchtower
LAIBULALE YA PA INTANETI
Chichewa
  • BAIBULO
  • MABUKU
  • MISONKHANO
  • km 10/03 tsamba 7
  • Kubwereza za M’sukulu ya Utumiki wa Mulungu

Palibe Vidiyo.

Pepani vidiyoyi ikukanika kutsegula.

  • Kubwereza za M’sukulu ya Utumiki wa Mulungu
  • Utumiki Wathu wa Ufumu—2003
Utumiki Wathu wa Ufumu—2003
km 10/03 tsamba 7

Kubwereza za M’sukulu ya Utumiki wa Mulungu

Mafunso otsatiraŵa mudzawakambirana pa Sukulu ya Utumiki wa Mulungu ya mlungu woyambira October 27, 2003. Woyang’anira sukulu adzatsogolera kubwereza nkhani zomwe zakambidwa m’kati mwa milungu ya September 1 mpaka October 27, 2003. Kubwerezaku kudzakhala kwa mphindi 30. [Dziŵani izi: Pa funso lomwe kumapeto kwake silikusonyeza buku lililonse lomwe mwatengedwa nkhaniyo, ndiye kuti muyenera mufufuze nokha kuti mupeze mayankho ake.—Onani Sukulu ya Utumiki, mas. 36-7.]

LUSO LA KULANKHULA

1. Kodi uphungu umene uli pa 1 Timoteo 2:9 wakuti munthu adziveke “chovala choyenera” umatanthauza chiyani, ndipo kodi zimenezi zingakhudze bwanji ulaliki wathu pa pulatifomu kapena mu utumiki wakumunda? [be-CN tsa. 132 ndime 4-5]

2. Kodi mfundo za m’Baibulo zimene zili pa 1 Yohane 2:15-17, Aefeso 2:2, ndi Aroma 15:3 ziyenera kukhudza bwanji kaonekedwe kathu? [be-CN tsa. 133 ndime 2-4]

3. Kodi n’chifukwa chiyani kudekha kuli kofunika, ndipo kodi tingaphunzire bwanji kudekha tikamakamba nkhani pa pulatifomu kapena tikamalalikira mu utumiki? [be-CN tsa. 135 bokosi; tsa. 136 ndime 5, bokosi]

4. Monga “mboni yokhulupirika ndi yoona,” kodi Yesu anasonyeza bwanji chitsanzo cha kugwiritsa ntchito Baibulo mu utumiki? (Chiv. 3:14) [be-CN tsa. 143 ndime 2-3]

5. Kodi tingakulitse bwanji luso lathu logwiritsa ntchito Baibulo? (Tito 1:9) [be-CN tsa. 144 ndime 1, bokosi]

NKHANI NA. 1

6. Kodi kuphunzira kumaphatikizapo chiyani, ndipo kodi ena mwa mapindu ophunzira Mawu a Mulungu mokhazikika ndi otani? [be-CN tsa. 27 ndime 3; tsa. 32 ndime 4]

7. Mogwirizana ndi zimene Yakobo 1:5, 6 amanena, kodi tiyenera kuchita chiyani ngati pali zinthu zofunika kwambiri zimene tiyenera kusankha? [w01-CN 9/1 tsa. 28 ndime 4]

8. Kodi “wonena ugogodi” amakhala chitsiru motani? (Miy. 10:18) [w01-CN 9/15 tsa. 25 ndime 3]

9. Lemba la Miyambo 10:15 limati: “Chuma cha wolemera ndi mudzi wake wolimba; koma umphawi wawo uwononga osauka.” Kodi zimenezi zimakhala zoona m’njira yotani? [w01-CN 9/15, tsa. 24]

KUŴERENGA BAIBULO KWA MLUNGU NDI MLUNGU

10. Zoona kapena Zonama: Pa 1 Akorinto 2:9, mtumwi Paulo akulankhula za cholowa chimene Yehova wakonzera anthu ake okhulupirika. Fotokozani. [ip-2-CN tsa. 366 bokosi]

11. Kodi anthu ena a ku Korinto ankadya zizindikiro ‘mosayenera’ m’njira yotani akakumana kuti achite Chikumbutso cha imfa ya Kristu? (1 Akor. 11:27) [w90-CN 2/15 tsa. 19 ndime 17]

12. Kodi mawu amene analembedwa pa 1 Akorinto 10:13 akukhudza ziyeso za mtundu wanji, ndipo kodi Yehova amaika “populumukirapo” motani? [w91-CN 10/1 tsa. 10-11 ndime 11-14]

13. Kodi chitsanzo cha Yesu cha kupatsa chimawakhudza bwanji Akristu? (2 Akor. 8:9) [w92-CN 1/15 tsa. 16 ndime 10]

14. Kodi Chilamulo chinakhala bwanji “namkungwi . . . wakutifikitsa kwa Kristu”? (Agal. 3:24) [w02-CN 6/1 tsa. 15 ndime 11]

15. Kodi “zoyamba za dziko lapansi” zimene tiyenera kuzipeŵa kuti tisasocheretsedwe n’chiyani? (Akol. 2:8)

    Mabuku a Chichewa (1974-2025)
    Tulukani
    Lowani
    • Chichewa
    • Tumizirani Ena
    • Zimene Mumakonda
    • Copyright © 2025 Watch Tower Bible and Tract Society of Pennsylvania
    • Zoyenera Kutsatira
    • Nkhani Yosunga Chinsinsi
    • Privacy Settings
    • JW.ORG
    • Lowani
    Tumizirani Ena