Zilengezo
◼ Mabuku ogaŵira mu October: Gaŵirani magazini a Nsanja ya Olonda ndi Galamukani! Mukapeza anthu achidwi, gaŵirani bulosha la Mulungu Amafunanji, ndipo yesetsani kuyambitsa maphunziro a Baibulo. November: Gaŵirani buku la Chidziŵitso kapena bulosha la Mulungu Amafunanji. Ngati anthu ali nalo kale buku ndi bulosha limeneli, mungagaŵire bulosha lina lililonse lakale. December: Munthu Wamkulu Woposa Onse Amene Anakhalako. Ngati mulibe, mungagaŵire Baibulo—Kodi Ndilo Mawu a Mulungu Kapena a Munthu? ndi Bukhu Langa la Nkhani za Baibulo January: Chinsinsi cha Chimwemwe cha Banja.
◼ Mphatika imene ili mu Utumiki Wathu wa Ufumu uno ndi “Ndandanda ya Sukulu ya Utumiki wa Mulungu ya 2004.” Isungeni kuti mudzaigwiritse ntchito chaka chonse cha 2004.
◼ Mipingo posachedwapa iyamba kulandira zipepala za lemba la chaka limodzi ndi mabuku amene imalandira nthaŵi zonse. Ngakhale kuti timakutumizirani zipepala za lemba la chaka zimenezi popanda kukuuzani mtengo wake, zimapangidwa ndi kampani yakunja ndipo ofesi ya nthambi imalipira. Tisaiwale kuti ndi mwayi wathu komanso udindo wathu kupereka mooloŵa manja pothandiza ntchito ya Ufumu mwa kupereka zopereka zaufulu zoti zithandize kulipira mtengo wa zipepalazi. Ngati zingatheke, zingakhale bwino kuti mipingo idzakhome zipepala za lemba la chaka zatsopanozi pofika pa January 1, 2004.
◼ Tikukumbutsa alembi onse a mipingo kuti azionetsetsa kuti alemba nambala ya mpingo yolondola akamatumiza fomu yofunsira mabuku ya mwezi ndi mwezi (S-14). Ngati mulemba nambala yolakwika, mabuku anu angatumizidwe ku mpingo wina. Mungapeze nambala yolondola pa sitetimenti ya mwezi ndi mwezi imene timatumiza ku mpingo wanu. Kuwonjezera pa fomu ya S-14, mukamatumiza makalata kapena mafomu ku ofesi ya nthambi amene akufunika kuti mulembepo nambala ya mpingo, nthaŵi zonse muyenera kulemba nambala yolondola.