Ndandanda ya Misonkhano ya Utumiki
Mlungu Woyambira October 13
Mph. 8: Zilengezo za pampingo. Zilengezo zina musankhe mu Utumiki Wathu wa Ufumu uno. Limbikitsani onse kuti agwiritse ntchito mafunso amene ali pa tsamba 1 poonanso notsi zawo, kuti akonzekere kudzakambirana nkhani za Msonkhano Wachigawo wakuti “Patsani Mulungu Ulemerero” pa Msonkhano wa Utumiki mlungu wamaŵa.
Mph. 20: “Tumikirani Yehova Mokondwera.” Kambani mawu oyamba osakwana mphindi imodzi ndiyeno kambiranani mwa mafunso ndi mayankho. (Onse akhale ndi mphatika ya Utumiki Wathu wa Ufumu wa January 2002 pokambirana nkhani ino.) Mukatha kukambirana ndime 4, tchulani zoti mu November tidzagaŵira bulosha la Mulungu Amafunanji ndi buku la Chidziŵitso. Mwachidule kambiranani ulaliki umodzi umene uli mu mphatika ya Utumiki Wathu wa Ufumu wa January 2002. Ndiyeno sonyezani chitsanzo cha mmene anthu angagwiritsire ntchito ulaliki umenewo. Limbikitsani onse kuti azikonzekera bwino akamapita mu utumiki.
Mph. 17: Kuchititsa Maphunziro a Baibulo Kumabweretsa Madalitso. Nkhani ndi kukambirana ndi omvetsera. Tchulani zokumana nazo zingapo zimene zili m’mabuku athu zokhudza maphunziro a Baibulo opita patsogolo. (w00-CN 3/1 tsa. 6) Pemphani omvetsera kuti afotokozepo zimene tikuphunzira pa zokumana nazo zimenezi, ndi mmene timapindulira chifukwa chochititsa maphunziro a Baibulo.
Nyimbo Na. 172 ndi pemphero lomaliza.
Mlungu Woyambira October 20
Mph. 5: Zilengezo za pampingo.
Mph. 40: “Misonkhano Yachigawo Yatilimbikitsa Kupatsa Mulungu Ulemerero!” Ikambidwe ndi mkulu. Mufotokoze mawu oyamba kwa mphindi imodzi kapena kucheperapo, ndiyeno mukambirane ndi omvetsera pulogalamu ya msonkhano wachigawo pogwiritsa ntchito mafunso amene alembedwa mu nkhaniyi. Mugaŵe nthaŵi yanu m’njira yoti muthe kukambirana mafunso onse, ndipo mwina mungafunikire kungomva yankho limodzi lokha pa mafunso ena. Simungathe kuŵerenga malemba onse amene alembedwa mu nkhaniyi panthaŵi imene mwapatsidwa. Malemba ameneŵa alembedwa kuti anthu apeze mayankho mosavuta. Ndemanga zizikhala makamaka zofotokoza phindu logwiritsa ntchito zinthu zimene tinaphunzira.
Nyimbo Na. 112 ndi pemphero lomaliza.
Mlungu Woyambira October 27
Mph. 12: Zilengezo za pampingo. Lipoti la maakaunti. Kumbutsani ofalitsa kuti apereke malipoti a October. Limbikitsani onse kuti akaŵerengenso notsi zawo za pulogalamu ya tsiku la msonkhano wapadera wa chaka chautumiki chapita pokonzekera Msonkhano wa Utumiki wa mlungu wamaŵa. Mwakugwiritsa ntchito mfundo zimene zili patsamba 8, khalani ndi zitsanzo ziŵiri zosonyeza zomwe zingachitikedi pogaŵira Nsanja ya Olonda ya October 15 ndi Galamukani! ya October 8. M’zitsanzo ziŵiri zonsezo, agaŵire magazini onse aŵiri ngakhale kuti adzachitira chitsanzo magazini imodzi. M’chitsanzo chimodzi, asonyeze mmene angachitire ulendo wobwereza kwa munthu amene amam’patsa magazini mwezi uliwonse. Amuchititse mwininyumbayo kuyembekezera mwachidwi ulendo wotsatira mwa kumuonetsa bokosi lakuti “M’kope Lathu Lotsatira.”—Onani Utumiki Wathu wa Ufumu wa October 1998, tsamba 8, ndime 7 mpaka 8.
Mph. 20: Gwiritsani Ntchito Lupanga la Mzimu. (Aef. 6:17) Kukambirana ndi omvetsera. Mfundo zake muzitenge m’buku la Sukulu ya Utumiki, masamba 143 mpaka 144. Pemphani anthu kuti ayankhe mafunso aŵa: (1) Kodi n’chifukwa chiyani timagwiritsa ntchito Baibulo poyankha mafunso? (2) Kodi dzina lakuti Mboni za Yehova limasonyeza chiyani za ife? (3) Kodi Yesu anatisiyira chitsanzo chotani, ndipo kodi tingamutsanzire bwanji? (4) M’gawo lathu, kodi njira zina zabwino zimene tingagwiritse ntchito n’ziti pofuna kuyamba kukambirana ndi anthu zinthu za m’Baibulo? (5) Kodi n’chifukwa chiyani ndi bwino kuŵerenga Baibulo mwachindunji pamene tingathe kutero? (6) Kodi akulu angalimbikitse bwanji ena kuti azigwiritsa ntchito bwino Baibulo? Khalani ndi chitsanzo chimene achikonzekera bwino chotengedwa pa zochita zimene zili pa tsamba 144, chosonyeza wofalitsa wodziŵa bwino kulalikira akugwiritsa ntchito lemba limodzi kapena kuposa apo poyankha funso. Limbikitsani onse kuti akhale n’cholinga chogwiritsa ntchito Baibulo nthaŵi iliyonse imene akuchitira umboni.
Mph. 13: Zokumana nazo. Pemphani omvetsera kuti afotokoze zokumana nazo zimene anakhala nazo panthaŵi ya msonkhano wachigawo kapena pamene amalalikira mwamwayi ku ntchito, ku sukulu, kapena kwina kulikonse.
Nyimbo Na. 52 ndi pemphero lomaliza.
Mlungu Woyambira November 3
Mph. 8: Zilengezo za pampingo. Mwakugwiritsa ntchito mfundo zimene zili patsamba 8, khalani ndi zitsanzo ziŵiri zosonyeza zomwe mungachite pogaŵira Nsanja ya Olonda ya November 1 ndi Galamukani! ya October 8. M’zitsanzo ziŵiri zonsezo, agaŵire magazini onse aŵiri ngakhale kuti adzachitira chitsanzo magazini imodzi. M’chitsanzo chimodzi, asonyeze zimene angachite atakumana ndi munthu amene sakufuna kuti tikambirane naye ponena mawu akuti, “Sindiri wokondwerera.”—Onani buku la Kukambitsirana, tsa. 16
Mph. 12: Zosoŵa za pampingo.
Mph. 25: Khalani Ochuluka mu Ntchito Zabwino. (1 Tim. 6:18) Mwakugwiritsa ntchito mafunso amene alembedwa m’munsiŵa, mkulu akambirane ndi omvetsera pulogalamu ya tsiku la msonkhano wapadera ya chaka cha utumiki chapita. Pemphani omvetsera kuti afotokoze mmene agwiritsira ntchito zimene anaphunzira. (Mukhoza kuwapatsiratu anthu mbali zimenezi.) Tsindikani mbali zotsatirazi za pulogalamuyo: (1) “Ntchito Zabwino Zimapindulitsa Kwambiri.” (Mlal. 2:11) Kodi n’chifukwa chiyani atumiki a Mulungu amachita ntchito zabwino zimene Mawu a Mulungu amafotokoza mmalo mochita ntchito zachabe za m’dzikoli? (2) “Khalani Olemera kwa Mulungu.” (Mat. 6:20) Kodi ena ‘adzikundikira okha chuma m’Mwamba’ motani, ndipo kodi apindula bwanji? (3) “Chititsani Utumiki Wanu Kukhala Wosangalatsa Kwambiri mwa Kuchititsa Phunziro la Baibulo.” (om tsa. 91) Kodi n’chiyani chingatithandize kuyambitsa ndi kuchititsa phunziro la Baibulo? (4) “Ntchito Zabwino M’nthaŵi Ino Yotuta.” (Mat. 13:37-39) Kodi Akristu oyambirira anasonyeza chitsanzo chotani cha ntchito zabwino, ndipo kodi ntchito ya Ufumu yawonjezeka motani masiku ano? (5) “Ntchito Zanu Zabwino Zilemekeze Yehova.” (Mat. 5:14-16) Kodi ena ‘awalitsa kuunika kwawo’ motani? (6) “Kuyamikira Achinyamata Chifukwa cha Ntchito Zabwino Polemekeza Yehova.” (Sal. 148:12, 13) Kodi achinyamata achikristu m’dera lathu lino akulemekeza bwanji Yehova? (7) “Pitirizani Kuchita Ntchito Zabwino Kuti Yehova Akudalitseni.” (Miy. 10:22) Pamene tikupitiriza kukhala otanganidwa pochita ntchito zabwino, kodi tingapeze madalitso otani monga munthu payekha, monga banja, monga mpingo, ndiponso monga gulu la padziko lonse?
Nyimbo Na. 180 ndi pemphero lomaliza.