Ndandanda ya Misonkhano ya Utumiki
Mlungu Woyambira December 8
Mph. 8: Zilengezo za pampingo. Zilengezo zina musankhe mu Utumiki Wathu wa Ufumu uno.
Mph. 20: “Umodzi Weniweni Wachikristu—Kodi Umatheka Motani?” Kambani mawu oyamba osakwana mphindi imodzi ndiyeno kambiranani mwa mafunso ndi mayankho. Pokambirana ndime 5, pemphani omvera kunena zimene iwo anaona pa misonkhano yachigawo, pogwira ntchito zomangamanga za Ufumu, kapena ntchito yopereka thandizo kumene kunagwa tsoka zosonyeza umodzi wathu wachikristu.
Mph. 17: “Sukulu ya Utumiki wa Mulungu ya 2004.” Ikambidwe ndi woyang’anira sukulu. Phatikizanipo mfundo za mu mphatika ya Utumiki Wathu wa Ufumu wa October 2003.
Nyimbo Na. 108 ndi pemphero lomaliza.
Mlungu Woyambira December 15
Mph. 10: Zilengezo za pampingo. Kambiranani bokosi lakuti “Pitaniko Mwamsanga.” Fotokozani makonzedwe apadera a utumiki wa kumunda pa December 25 ndi pa January 1.
Mph. 15: Phunziro la Umwini—Mbali ya Kulambira. Nkhani yochokera mu Nsanja ya Olonda ya October 1, 2000, masamba 14-15, ndime 6-10.
Mph. 20: “Thandizani Anthu Amaganizo Abwino.” Kambani mawu oyamba osakwana mphindi imodzi ndiyeno kambiranani mwa mafunso ndi mayankho. Gwiritsani ntchito mafunso amene aperekedwawo. Onaninso mfundo za momwe tingachitire maulendo obwereza zotchulidwa m’bokosi patsamba 3 mu Utumiki Wathu wa Ufumu wa May 1997.
Nyimbo Na. 42 ndi pemphero lomaliza.
Mlungu Woyambira December 22
Mph. 12: Zilengezo za pampingo. Lipoti la maakaunti. Mwa kugwiritsa ntchito mfundo za patsamba 8, sonyezani zitsanzo za momwe tingagaŵire Nsanja ya Olonda ya December 15 ndi Galamukani! ya December 8. M’zitsanzo zonse ziŵirizo, agaŵire magazini onse aŵiri pamodzi ngakhale kuti agwiritsa ntchito magazini imodzi pokambirana. Kumbutsani onse za Msonkhano wa Utumiki wapadera wa mlungu wamaŵa, womwe tidzakambirana ndi kugaŵa makadi a Chidziŵitso kwa Madokotala/Chowamasula ku Mlandu.
Mph. 15: Zosoŵa za pampingo.
Mph. 18: “Kufunafuna Anthu Oyenerera.” Kambani mawu oyamba osakwana mphindi imodzi ndiyeno kambiranani mwa mafunso ndi mayankho. Ikambeni mogwirizana ndi zochitika kwanuko. Ndi nthaŵi iti imene mosakayikira tingapeze anthu panyumba? Kodi papezeka zotani chifukwa cholalikira dzuŵa litapendeka? Kodi ndi njira ziti zimene tingagwiritse ntchito kuti tilankhule ndi anthu amene sapezekapezeka panyumba?
Nyimbo Na. 209 ndi pemphero lomaliza.
Mlungu Woyambira December 29
Mph. 10: Zilengezo za pampingo. Limbikitsani ofalitsa onse kupereka malipoti awo a utumiki wa kumunda a December. Tchulani mabuku ofunika kugaŵira mu January. Mwa kugwiritsa ntchito mfundo za patsamba 8, sonyezani zitsanzo za momwe tingagaŵire Nsanja ya Olonda ya January 1 ndi Galamukani! ya December 8.
Mph. 15: “Kuimba Kwathu Kutamande Yehova.” Nkhani ndi kukambirana ndi omvetsera. Yamikirani mpingowo chifukwa choyesetsa kuimbira Yehova zitamando ndi mtima wonse.
Mph. 20: Kuthana ndi Mavuto Azamankhwala Popanda Kukayikira Chilichonse. Nkhaniyi ikambidwe ndi mkulu woyenerera, pogwiritsa ntchito autilaini yochokera ku ofesi ya nthambi. Onaninso mfundo zazikulu m’bokosi lakuti “Zinthu Zotithandiza Kuti Tipeŵe Magazi.” Gaŵirani ofalitsa obatizidwa ndi ana awo makadi a Chidziŵitso kwa Madokotala/Chowamasula ku Mlandu ndi Makadi a Ana.
Nyimbo Na. 182 ndi pemphero lomaliza.
Mlungu Woyambira January 5
Mph. 5: Zilengezo za pampingo.
Mph. 15: Ntchito Yanu Sili Chabe. (1 Akor. 15:58) Kukambirana ndi omvetsera. Konzeranitu kuti ofalitsa amene akhala achangu kwa zaka zambiri anene mmene ntchito yolalikira inali kuyendera masiku oyambirira. Ndi anthu angati amene anali kusonkhana ndi mpingo uno? Kodi mpingo unali ndi gawo lalikulu bwanji? Kodi anthu anali kuchita motani akamva uthenga wa Ufumu? Kodi munali kukumana ndi chitsutso chotani? Kodi ntchito ya Ufumu yapita patsogolo motani m’deralo m’zaka zonsezi?
Mph. 25: “Kuphunzira Pakati pa Anthu a Mulungu.” Nkhani yokambidwa ndi mkulu komanso kukambirana ndi omvetsera. Kambirananinso bokosi lakuti “Malangizo Ophunzitsira Anthu Achikulire Kuŵerenga ndi Kulemba.”
Nyimbo Na. 7 ndi pemphero lomaliza.