Watchtower LAIBULALE YA PA INTANETI
Watchtower
LAIBULALE YA PA INTANETI
Chichewa
  • BAIBULO
  • MABUKU
  • MISONKHANO
  • km 4/04 tsamba 1
  • Achinyamata—Ŵerengani Mawu a Mulungu!

Palibe Vidiyo.

Pepani vidiyoyi ikukanika kutsegula.

  • Achinyamata—Ŵerengani Mawu a Mulungu!
  • Utumiki Wathu wa Ufumu—2004
  • Nkhani Yofanana
  • Kodi Mumasankha Bwanji Zochita?
    Nsanja ya Olonda Yolengeza Ufumu wa Yehova (Yophunzira)—2016
  • Achinyamata, Kodi Mukuyesetsa Kukwaniritsa Zolinga Zauzimu?
    Nsanja ya Olonda Yolengeza Ufumu wa Yehova (Yophunzira)—2018
  • Muzikhulupirira Yehova Kuti Muzisankha Zochita Mwanzeru
    Nsanja ya Olonda Yolengeza Ufumu wa Yehova (Yophunzira)—2017
  • Zosankha Zanu Zizilemekeza Mulungu
    Nsanja ya Olonda—2011
Onani Zambiri
Utumiki Wathu wa Ufumu—2004
km 4/04 tsamba 1

Achinyamata—Ŵerengani Mawu a Mulungu!

1 Paunyamata ndi nthaŵi yovuta komanso yofunika kusankha zochita pankhani zazikulu. Ambiri mwa Akristu achinyamatanu tsiku lililonse mumakakamizidwa kuphwanya miyezo ya Mulungu ya makhalidwe abwino. Pamene mukuyamba kusankha zochita pankhani ya maphunziro, ntchito, ndiponso ukwati, muzikhala muli kale ndi zolinga zauzimu. Mukatero m’pamene mungasankhe zochita zina zimene zingakupindulitseni kwa moyo wanu wonse. Zolinga zauzimu zenizeni zidzakuthandizani kuchita mwanzeru ndiponso kukometsa njira yanu. Kuŵerenga ndi kusinkhasinkha Mawu a Mulungu nthaŵi zonse, kudzakulimbikitsani kutsatira uphungu wake wouziridwa pamoyo wanu, ndipo zofuna zanu zoyenera zidzakuyenderani bwino.—Yos. 1:8; Sal. 1:2, 3.

2 Kodi Adzakupindulitsani Bwanji? Dziko la Satana lili ndi zokopa zambiri zimene zingatipangitse kuchita zoipa. (1 Yoh. 2:15, 16) Mwina mukudziŵa anzanu a m’kalasi kapena ena a zaka zangati zanu amene apeza mavuto chifukwa chochita zinthu motengera anzawo. Kutsatira uphungu wa m’Baibulo kudzakuthandizani kukhala wolimba pamakhalidwe abwino ndiponso mwauzimu kuti mukane kuchita zoipa. Komanso, uphungu wa m’Mawu a Mulungu ungakuthandizeni kupeŵa misampha yosaoneka bwinobwino ya Satana. (2 Akor. 2:11; Aheb. 5:14) Kuyenda m’njira za Mulungu kudzakupatsani chimwemwe chenicheni—mudzasangalala ndi zochita zanu pamoyo wanu.—Sal. 119:1, 9, 11.

3 Mfundo za m’Mawu a Mulungu zimene n’zosasintha zimaposa nzeru za anthu. (Sal. 119:98-100) Kudziŵa bwino mfundo za m’Baibulo, kusinkhasinkha zolinga za Yehova zimene waulula pamodzi ndi pemphero la pansi pamtima, zingakuthandizeni kupanga ubwenzi wolimba ndi Yehova Mulungu, yemwe ndi Mlembi wanzeru koposa wa Baibulo. Iye akulonjeza kuti: “Ine ndidzakulangiza ndi kuphunzitsa iwe za njira ukayendayo; ndidzakupangira ndi diso langa lakuyang’ana iwe.”—Sal. 32:8.

4 Patulani Nthaŵi Yowaŵerenga: Mtsikana wina wachikristu anatsimikiza mtima kuŵerenga Baibulo lonse, ndipo analimaliza kuŵerenga m’chaka chimodzi. Kodi anapindula chiyani? Akuti: “Ndinaphunzira zambiri za Yehova—zinthu zimene zandithandiza kumuyandikira kwambiri ndiponso kufuna kumuopa kwa moyo wanga wonse.” (Yak. 4:8) Kodi munaŵerengako Baibulo lonse? Ngati simunaŵerenge, bwanji osakhala ndi cholinga chochita zimenezo? Ndithudi Yehova adzadalitsa khama lanu, ndipo mudzapindula kwambiri.

    Mabuku a Chichewa (1974-2025)
    Tulukani
    Lowani
    • Chichewa
    • Tumizirani Ena
    • Zimene Mumakonda
    • Copyright © 2025 Watch Tower Bible and Tract Society of Pennsylvania
    • Zoyenera Kutsatira
    • Nkhani Yosunga Chinsinsi
    • Privacy Settings
    • JW.ORG
    • Lowani
    Tumizirani Ena