Ndandanda ya Misonkhano ya Utumiki
Mlungu Woyambira April 12
Mph. 10: Zilengezo za pampingo. Zilengezo zina muzisankhe mu Utumiki Wathu wa Ufumu uno. Mwa kugwiritsa ntchito mfundo za patsamba 8, sonyezani zitsanzo za momwe tingagaŵire Nsanja ya Olonda ya April 15 ndi Galamukani! ya May 8. M’zitsanzo zonse ziŵirizo, agaŵire magazini onse aŵiri pamodzi ngakhale kuti agwiritsa ntchito magazini imodzi pokambirana. M’zitsanzo zonsezi, sonyezani njira zosiyana za mmene tingayankhire munthu amene akufuna kuti tisakambirane naye ponena kuti “Ndili wotanganidwa.”—Onani buku la Kukambitsirana, tsamba 19 ndi 20. (Ngati magazini ameneŵa sanafike pampingopo, gwiritsani ntchito chitsanzo cha ulaliki cha mu Utumiki Wathu wa Ufumu wa mwezi watha.)
Mph. 15: “Kum’patsa Yehova Zabwino Koposa.” Kambani mawu oyamba osakwana mphindi imodzi ndiyeno kambiranani mwa mafunso ndi mayankho. Pokambirana ndime 4, pemphani omvera kunena njira zenizeni zimene tingasonyezere kuti timakonda anthu pochita utumiki wathu.
Mph. 20: “Kodi Mboni za Yehova Zimaona Motani Nkhani Yovota?” Ikambidwe ndi mkulu woyenerera. Kambani mawu oyamba osakwana mphindi imodzi ndiyeno kambiranani mwa mafunso ndi mayankho. Gwiritsani ntchito mafunso amene aperekedwawo. Ŵerengani ndi kukambirana malemba ofunika kwambiri. Mbale amene akukamba nkhaniyi atsatire kwambiri mfundo za m’Baibulo pankhaniyi ndipo apeŵe kuikapo maganizo.
Nyimbo Na. 91 ndi pemphero lomaliza.
Mlungu Woyambira April 19
Mph. 8: Zilengezo za pampingo.
Mph. 17: “Tsanzirani Mtima wa Yesu.” Kambani mawu oyamba osakwana mphindi imodzi ndiyeno kambiranani mwa mafunso ndi mayankho. Gwiritsani ntchito mafunso amene aperekedwawo. Pokambirana ndime 4, pemphani apainiya othandiza kunena madalitso amene apeza chifukwa chochita upainiyawo.
Mph. 20: “Msonkhano Wachigawo wa 2004 Wakuti ‘Yendani ndi Mulungu.’” Kambani mawu oyamba osakwana mphindi imodzi ndiyeno kambiranani mwa mafunso ndi mayankho. Ikambidwe ndi mlembi wa mpingo. Limbikitsani onse kuti akonzekere msonkhanowu mofulumira.
Nyimbo Na. 80 ndi pemphero lomaliza.
Mlungu Woyambira April 26
Mph. 12: Zilengezo za pampingo. Lipoti la maakaunti. Kumbutsani ofalitsa kupereka malipoti awo a utumiki wakumunda a April. Tchulani mabuku ogaŵira mu May. Mwa kugwiritsa ntchito mfundo za patsamba 8, sonyezani zitsanzo za momwe tingagaŵire Nsanja ya Olonda ya May 1 ndi Galamukani! ya May 8. M’zitsanzo zonse ziŵirizo, agaŵire magazini onse aŵiri pamodzi ngakhale kuti agwiritsa ntchito magazini imodzi pokambirana. Chitsanzo chimodzi pa zitsanzozi, chikhale cholalikira kwa mnzathu wa kuntchito kapena wa kusukulu. (Ngati magazini ameneŵa sanafike pampingopo, gwiritsani ntchito chitsanzo cha ulaliki cha mu Utumiki Wathu wa Ufumu wa mwezi watha.)
Mph. 15: Zosoŵa za pampingo.
Mph. 18: “Kupereka Malipoti a Utumiki Wathu wa Kumunda Mwamsanga Ndiponso Molondola.” Kambani mawu oyamba osakwana mphindi imodzi ndiyeno kambiranani mwa mafunso ndi mayankho. Gwiritsani ntchito mafunso amene aperekedwawo. Ikambidwe ndi woyang’anira utumiki.
Nyimbo Na. 38 ndi pemphero lomaliza.
Mlungu Woyambira May 3
Mph. 10: Zilengezo za pampingo. Nenani mwachidule zochitika zimene zimakonda kukonzedwa m’miyezi ikubwerayi; kupezeka pa msonkhano wachigawo, kuchita upainiya wothandiza, kukonza panyumba, ndiponso mwina kupita kokasangalala. Ngati mpingo uli ndi gawo limene sulalikiramo kaŵirikaŵiri, lengezani zimene zikukonzedwa zokafola gawo lonselo. Khama ndiponso kukonzekera n’zofunika kuti tisalephere kuchita phunziro la banja, misonkhano yampingo, ndi utumiki wakumunda ngati ulendo kapena zochitika zina zidodometsa zimene timachita nthaŵi zonse. (Miy. 21:5) Kumbutsani onse kupereka malipoti awo a utumiki wakumunda, kaya ali panyumba kapena achoka.
Mph. 15: “Achinyamata—Ŵerengani Mawu a Mulungu!” Kambani mawu oyamba osakwana mphindi imodzi ndiyeno kambiranani mwa mafunso ndi mayankho. Konzeranitu kuti wachinyamata mmodzi kapena aŵiri anene za pulogalamu yawo yoŵerenga Baibulo ndiponso mmene akupindulira nayo. Limbikitsani achinyamata kuti chikhale cholinga chawo kuŵerenga Baibulo lonse. Phatikizanipo ndemanga za m’buku la Sukulu ya Utumiki, tsamba 10, ndime 4.
Mph. 20: Kodi Kulambira Yehova Kumapindulitsa Bwanji Miyoyo Yathu? Kukambirana ndi omvera. Kulambira koona ndicho chinsinsi cha moyo wosangalala ndi watanthauzo. (1) Kumatithandiza kulimbana ndi mavuto ndi nkhaŵa za pamoyo. (Afil. 4:6, 7) (2) Kumatilimbikitsa kukulitsa makhalidwe ofanana ndi a Mulungu. (2 Pet. 1:5-8) (3) Kumatithandiza kugwiritsa ntchito nthaŵi yathu ndi zinthu zathu m’njira yopindulitsa kwambiri. (1 Tim. 6:17-19) (4) Kumatipatsa chiyembekezo chodalirika cha m’tsogolo. (2 Pet. 3:13) (5) Kumatithandiza kupanga ubwenzi wolimba ndi Yehova. (Yak. 4:8) Siyanitsani mmene zinthu zimenezi zilili zosoŵa kwa anthu amene sadziŵa kapena satumikira Yehova.
Nyimbo Na. 164 ndi pemphero lomaliza.