Zilengezo
◼ Mabuku ogaŵira mu April ndi May: Gaŵirani magazini a Nsanja ya Olonda ndi Galamukani! Popanga maulendo obwereza kwa anthu achidwi, omwe ena mwa iwo angakhale amene anapezeka pa Chikumbutso kapena pa zochitika zina zauzimu koma sasonkhana ndi mpingo mokhazikika, yesetsani kugaŵira buku la Lambirani Mulungu. Tidzachite zotheka kuyambitsa phunziro la Baibulo lapanyumba, makamaka ngati ena anamaliza kale kuphunzira buku la Chidziŵitso ndi bulosha la Mulungu Amafunanji. June: Phunzirani kwa Mphunzitsi Waluso. Ngati anthu anena kuti alibe ana, gaŵirani bulosha la Mulungu Amafunanji. Pogwiritsa ntchito buloshali, yesetsani kuyambitsa maphunziro a Baibulo apanyumba. July ndi August: Mabulosha alionse amene mpingo uli nawo.
◼ Kuyambira mu April, tidzatumiza mabaji a msonkhano wachigawo wa 2004 pamodzi ndi mabuku. Simukufunika kuitanitsa mabajiwa. Mabaji adzaikidwa m’mipukutu ya mabaji 20 mpukutu uliwonse, malinga ndi kukula kwa mpingo uliwonse. Ngati mpingo ukufuna mabaji ena, itanitsani pa Fomu Yofunsira Mabuku (S-14). Ngati pampingopo pali amene akufuna mapulasitiki oikamo baji, mungawaitanitsire.
◼ N’kofunika kuti ofesi ya nthambi ikhale ndi maadiresi ndi manambala a telefoni amene akugwira ntchito panopo a oyang’anira otsogolera ndi alembi onse m’kaundula wake. Zimenezi zikangosintha nthaŵi ina iliyonse, Komiti ya Utumiki ya Mpingo izilemba ndi kusaina fomu ya Kusintha Adiresi ya Woyang’anira Wotsogolera/Mlembi (S-29) ndi kuitumiza mwamsanga ku ofesi ya nthambi.
◼ Alembi a mipingo azisunga mafomu okwanira a Chofunsirapo Utumiki wa Upainiya Wokhazikika (S-205) ndi Chofunsirapo Utumiki wa Upainiya Wothandiza (S-205b). Angaitanitse mafomuŵa pa Fomu Yofunsira Mabuku (S-14). Sungani mafomu okwanira pafupifupi chaka chimodzi. Pendani mafomu onse a anthu amene afunsira upainiya wokhazikika kuti mutsimikizire kuti ayankha mafunso onse ndiponso pali tsiku limene anabatizidwa. Ngati wofunsirayo sakukumbukira tsiku limene anabatizidwa, angoyerekeza tsikulo ndiyeno asunge limenelo.