Watchtower LAIBULALE YA PA INTANETI
Watchtower
LAIBULALE YA PA INTANETI
Chichewa
  • BAIBULO
  • MABUKU
  • MISONKHANO
  • km 4/04 tsamba 6
  • Kubwereza za M’sukulu ya Utumiki Wa Mulungu

Palibe Vidiyo.

Pepani vidiyoyi ikukanika kutsegula.

  • Kubwereza za M’sukulu ya Utumiki Wa Mulungu
  • Utumiki Wathu wa Ufumu—2004
Utumiki Wathu wa Ufumu—2004
km 4/04 tsamba 6

Kubwereza za M’sukulu ya Utumiki Wa Mulungu

Mafunso otsatiraŵa mudzawakambirana pa Sukulu ya Utumiki wa Mulungu ya mlungu woyambira April 26, 2004. Woyang’anira sukulu adzatsogolera kubwereza nkhani zomwe zakambidwa m’kati mwa milungu ya March 1 mpaka April 26, 2004. Kubwerezaku kudzakhala kwa mphindi 30. [Dziŵani izi: Pa funso lomwe kumapeto kwake silikusonyeza buku lililonse lomwe mwatengedwa nkhaniyo, ndiye kuti muyenera mufufuze nokha kuti mupeze mayankho ake.—Onani Sukulu ya Utumiki, mas. 36-7.]

LUSO LA KULANKHULA

1. Tikamakamba nkhani, n’chifukwa chiyani ndi bwino kugwiritsa ntchito autilaini polankhula kusiyana ndi kuŵerenga nkhani yochita kulemba? [be-CN tsa. 166 ndime 3]

2. Tikamakonzekera ulaliki wakumunda, kodi tingakonze bwanji maganizo athu kuti akhale autilaini ya m’maganizo? [be-CN tsa. 167 ndime 2]

3. Mwakugwiritsa ntchito Machitidwe 13:16-41 ndi Machitidwe 17:2, 3, fotokozani mmene Paulo ‘anawatsimikizira kuti Yesu ndi Kristu.’ (Mac. 9:22) [be-CN tsa. 170 ndime 2]

4. Kodi mapindu ena okamba nkhani kuchokera mu mtima ndi otani? [be-CN tsa. 175 ndime 2-5]

5. Kodi mbuna zina zimene zimabwera chifukwa cholankhula kuchokera mu mtima n’ziti, ndipo n’chiyani chingatithandize kuzipeŵa? [be-CN tsa. 175 ndime 6–tsa. 176 ndime 3]

NKHANI NA. 1

6. Malinga ndi nkhani imene ili pa Genesis 32:24-32, kodi Yakobo, amene panthaŵiyo anali ndi zaka 97, anachita chiyani kuti alandire madalitso a Yehova, ndipo kodi zimenezi zikutiphunzitsa chiyani? [w02-CN 8/1 mas. 29-31]

7. (a) Kodi “kulingalira” n’kutani, ndipo kodi kungatithandize bwanji kupeŵa kusasamala ndiponso kuipidwa monkitsa? (Miy. 1:4) [w02-CN 8/15 mas. 21-22]

8. Kodi okamba nkhani angatani kuti Malemba akhale maziko a nkhani zawo? [be-CN tsa. 52 ndime 6–tsa. 53 ndime 5]

9. Posintha autilaini ya mafupa okhaokha kukhala mnofu wa malongosoledwe a Malemba, kodi wokamba nkhani ayenera kusankha chiyani? [be-CN tsa. 54 ndime 2-4]

10. Kodi n’chifukwa chiyani Yehova anadyetsa Aisrayeli mana mlungu ndi mlungu, mwezi ndi mwezi m’chipululu, ndipo kodi tingaphunzire chiyani kuchokera pa nkhani imeneyi? (Deut. 8:16) [w02-CN 9/1 tsa. 30 ndime 3-4]

KUŴERENGA BAIBULO KWA MLUNGU NDI MLUNGU

11. Monga mmene lemba la Genesis 37:12-17 likusonyezera, kodi pali kufanana kotani pakati pa moyo wa Yosefe ndi wa Yesu? [w87-CN 5/1 tsa. 12 ndime 12]

12. Monga mmene tingaonere mu nkhani imene ili pa Genesis 42:25-35, kodi Yosefe anasonyeza bwanji chifundo chofanana ndi chimene Yesu amasonyeza? [w87-CN 5/1 tsa. 18 ndime 10; tsa. 19 ndime 17]

13. Kodi zimene gulu la kapolo limatipatsa masiku ano zikufanana bwanji ndi kugawa tirigu kumene kunachitika mu nthaŵi ya Yosefe? (Gen. 47:21-25)

14. Pamene Yehova ananena kuti “Ine ndine yemwe ndili ine,” kodi amasonyeza chiyani chokhudza dzina lake?

15. Kodi ndi maupandu obadwa nawo aŵiri ati a kudandaula amene tikuwaona pa Eksodo 16:2, 3? [w93-CN 3/15 tsa. 21]

    Mabuku a Chichewa (1974-2025)
    Tulukani
    Lowani
    • Chichewa
    • Tumizirani Ena
    • Zimene Mumakonda
    • Copyright © 2025 Watch Tower Bible and Tract Society of Pennsylvania
    • Zoyenera Kutsatira
    • Nkhani Yosunga Chinsinsi
    • Privacy Settings
    • JW.ORG
    • Lowani
    Tumizirani Ena