Kupereka Malipoti a Utumiki Wathu wa Kumunda Mwamsanga Ndiponso Molondola
1. Kodi timamva bwanji tikalandira malipoti olimbikitsa a ntchito ya utumiki wa kumunda?
1 Tonsefe timasangalala tikamva za zinthu zabwino zimene zikuchitika polalikira uthenga wa Ufumu. (Onani Miyambo 25:25.) Petro atatha kukamba nkhani yolimbikitsa patsiku la Pentekoste, ‘anawonjezereka anthu ngati zikwi zitatu.’ (Mac. 2:41) Patapita nthaŵi pang’ono, anthu ameneŵa anachuluka kufika “ngati zikwi zisanu.” (Mac. 4:4) Akristu a m’zaka 100 zoyambirira ayenera kuti anasangalala kwambiri ndi malipoti amenewo! Masiku anonso timasangalala kumva malipoti olimbikitsa.
2. Kodi chimafunika n’chiyani kuti malipoti akhale olondola?
2 Timasangalala kumva kuti ntchito yolalikira uthenga wabwino padziko lonse ikuwayendera bwino abale athu. Popeza kuwonkhetsa malipoti ameneŵa kumatenga nthaŵi yambiri ndiponso ndi ntchito yaikulu, n’kofunika kuti wofalitsa Ufumu aliyense athandize nawo ntchitoyi. Kodi mumayesetsa kupereka mwamsanga malipoti anu mwezi uliwonse?
3. Kodi malipoti olondola ndi othandiza bwanji kwa ifeyo ndiponso gulu la Yehova?
3 Timasangalala kwambiri ndi malipoti onena za kuwonjezereka pantchito yauzimu. Komanso, malipoti amathandiza gulu kudziŵa mmene ntchito yapadziko lonse ikuyendera. Gulu limafuna kuona kumene kukufunika thandizo lochuluka kapena mabuku amene akufunika kusindikiza ndiponso kuchuluka kwake. Malipoti a utumiki wa kumunda amathandiza akulu mumpingo uliwonse kudziŵa mbali zofunika kuwongolera. Malipoti abwino amalimbikitsa, ndipo amatithandiza tonsefe kupenda utumiki wathu ndikuona pofunika kuwongolera.
4. Kodi wofalitsa aliyense payekha ndiponso akulu angachite zotani mu mpingo kuti atsimikizire kuti malipoti a utumiki wa kumunda olondola atumizidwa ku ofesi ya nthambi mwezi uliwonse?
4 Ofalitsa onse afunika kuzindikira kuti ndi udindo wawo kupereka mwamsanga malipoti a utumiki wa kumunda mwezi uliwonse. Wofalitsa aliyense payekha angaike malipoti ake m’bokosi la ku Nyumba ya Ufumu ngati akufuna kutero kapena ngati walephera kupereka kwa woyang’anira phunziro lake la buku. Mlembi azichotsa malipoti m’bokosi la malipoti mwezi uliwonse. Woyang’anira phunziro la buku azionetsetsa kuti malipoti a gulu lake amene walandira aperekedwa mwamsanga kwa mlembi kuti awonkhetse. Zimenezi ziyenera kuchitika pasanafike pa 6 mwezi uliwonse. Wofalitsa wampingo aliyense ndiponso mpainiya ayenera kuyesetsa kupereka malipoti ake panthaŵi yake pamapeto a mwezi uliwonse. Popeza kuti oyang’anira Phunziro la Buku la Mpingo amakhalanso tcheru kuthandiza anthu amene zimawavuta kuchita utumiki wa kumunda mokhazikika, paphunziro la buku lomaliza mwezi uliwonse kapena panthaŵi ina yoyenera iwo angakumbutse anthu kuti apereke malipoti.
5. Kodi wofalitsa aliyense payekha angathandize bwanji kuti lipoti lizikhala lolondola, ndipo kodi pepala lolembapo Lipoti la Utumiki Wakumunda (S-4) lingatithandize bwanji pankhani imeneyi?
5 Kodi Ofalitsa Angathandize Bwanji Kuti Lipoti Likhale Lolondola? Kuti malipoti akhale olondola, tizichitira lipoti maola athunthu okha ku mpingo. Wofalitsa ngati ali ndi nthaŵi yosakwana ola limodzi azisunga n’kudzaiphatikiza pa lipoti lake la mwezi wotsatira. Nthaŵi iliyonse imene tapita mu utumiki wa kumunda, ndi bwino kulemba nthaŵi imene takhala mu ulaliki, magazini amene tagaŵira, ndiponso maulendo obwereza amene tapanga. Ndiyeno pamapeto pa mwezi tingawonkhetse pamodzi zimene tinalembazo, osati kungoganizira kuti tachita mwakuti ayi. Pepala lolembapo Lipoti la Utumiki Wakumunda (S-4) limene mpingo umapereka limathandiza kuti kusunga zimenezi kukhale kosavuta.
6. (a)Kodi ndi nthaŵi iti imene tingaŵerengere ulendo wobwereza? (b) Mpingo ukakhala ndi mapepala olembapo Lipoti la Phunziro (S-3), kodi ofalitsa ayenera kukumbukira kuti pali kugwirizana kotani pakati pepala lolembapo Lipoti la Phunziro (S-3), ndi pepala lolembapo Lipoti la Utumiki Wakumunda (S-4)? (c) Ngati mpingo ulibe mapepala olembapo Lipoti la Phunziro, kodi n’kofunika kuti ofalitsa aziperekabe Lipoti la Utumiki Wakumunda (S-4) mwezi uliwonse, ndipo n’chifukwa chiyani ayenera kuchita zimenezo?
6 Kodi ndi Nthaŵi Iti Imene Tingaŵerengere Ulendo Wobwereza? Kuti tiŵerengere ulendo wobwereza, tiyenera kulankhula ndi munthu yemwe tinam’lalikirapo. Tingaŵerengere maulendo obwereza komanso nthaŵi imene takhala mu utumiki wa kumunda pamene tikukapereka magazini kwa anthu amene timakawapatsa magazini, polalikira kachiŵiri kwa munthu yemwe tinalankhula naye kale patelefoni, kapena polemba kalata kwa munthu amene tinam’lalikirapo kale. Nthaŵi iliyonse tikachititsa phunziro la Baibulo lapanyumba tingaŵerengerenso ulendo wobwereza. Ngati mpingo unaitanitsa mapepala olembapo Lipoti la Phunziro (S-3), pamapeto a mwezi muzilemba pepala limeneli bwinobwino ndiponso molondola za phunziro la Baibulo lililonse limene munachititsa n’kuperekera kumodzi ndi pepala lanu lolembapo Lipoti la Utumiki Wakumunda (S-4). Chiŵerengero cha maphunziro osiyanasiyana a Baibulo amene munachititsa m’mwezi umenewo chiyenera kulembedwa m’bokosi loyenerera limene lili kumanja, m’munsi mwa pepala lolembapo Lipoti la Utumiki Wakumunda (S-4). Ngati mpingo ulibe mapepala a S-3, chonde lembani pepala lolembapo Lipoti (S-4) ndi kupereka monga mwa nthaŵi zonse, kuti ofesi ya nthambi idzalandire lipoti lolondola la ntchito ya mwezi umenewo ya mpingo wanu.
7. Kodi timapindulanji chifukwa chotsatira mofunitsitsa zimene gulu linakonza?
7 Wofalitsa aliyense amene amatsatira mofunitsitsa zimene tafotokozazi, zomwe n’zimene gulu linakonza angasangalale kudziŵa kuti amathandiza kwambiri kuti lipoti la ntchito ya padziko lonse ya Mboni za Yehova lizikhala lolondola. (Yerekezerani ndi Ezekieli 9:11.) Tiyeni tonsefe tizipereka malipoti a utumiki wa kumunda olondola ndiponso panthaŵi yake!