Kodi Mboni za Yehova Zimaona Motani Nkhani Yovota?
1. Kodi Akristu amaona motani kuvota?
1 M’Baibulo muli mfundo zofotokozedwa bwino zimene zimapangitsa atumiki a Mulungu kukhala ndi malingaliro oyenera pa nkhani imeneyi. Komabe, zikuoneka kuti palibe mfundo imene imaletsa kuvota kwenikweniko. Mwachitsanzo, palibe chifukwa chimene bungwe la oyang’anira siliyenera kuchitira voti posankha mfundo za gulu lawo. Nthaŵi zambiri mipingo ya Mboni za Yehova imasankha nthaŵi ya misonkhano ndi kagwiritsidwe ntchito ka ndalama za mpingo mwa kuvota pokweza manja.
2. Kodi ndi mfundo za m’Malemba ziti zimene zimakhudza kuvota pachisankho cha ndale?
2 Komabe, bwanji za kuvota pachisankho cha ndale? N’zoona kuti m’mayiko ena a demokalase, pafupifupi theka la anthu a m’mayikowo sapita kukavota patsiku la chisankho. Ponena za Mboni za Yehova, izo sizisokoneza ufulu wa ena woponya voti; komanso mwa njira iliyonse siziuza anthu kuti asavote pazisankho za ndale. Zimalemekeza ndi kugwirizana ndi akuluakulu a boma amene asankhidwa moyenerera pa zisankho zimenezi. (Aroma 13:1-7) Pankhani yakuti kaya iwo akavotera winawake amene waima nawo pa chisankho, aliyense wa Mboni za Yehova amasankha yekha chochita malinga ndi chikumbumtima chake chophunzitsidwa ndi Baibulo komanso mmene amaonera udindo wake kwa Mulungu ndi Boma. (Mat. 22:21; 1 Pet. 3:16) Posankha chochita pankhaniyi, yomwe aliyense amadzisankhira yekha, Mboni zimalingalira mfundo zingapo.
3. Kodi mawu a Yesu opezeka m’buku la Yohane angatithandize motani?
3 Yoyamba, Yesu Kristu ponena za otsatira ake anati: “Sakhala a dziko lapansi, monga Ine sindikhala wa dziko lapansi.” (Yoh. 17:14) Mboni za Yehova sizipeputsa mfundo imeneyi. Popeza kuti ‘sizili za dziko lapansi,’ siziloŵerera m’zochitika za ndale za dziko.—Yoh. 18:36.
4. Kodi mfundo yakuti Akristu ali ngati akazembe imakhudza motani zochita zawo?
4 Yachiŵiri, mtumwi Paulo anadzitcha kukhala “mtumiki” woimira Kristu kwa anthu a m’tsiku lake. (Aef. 6:20; 2 Akor. 5:20) Mboni za Yehova zimakhulupirira kuti Kristu Yesu tsopano ndi Mfumu yoikidwa ya Ufumu wa Mulungu wakumwamba, ndipo monga atumiki kapena kuti akazembe, ziyenera kulengeza zimenezi ku mitundu ya anthu. (Mat. 24:14; Chiv. 11:15) Akazembe safunika kuloŵerera m’zochitika za m’mayiko amene iwo atumizidwako. Monga oimira Ufumu wa Mulungu wakumwamba, Mboni za Yehova zimaona kuti zili ndi udindo wofananawo wosaloŵerera m’ndale za m’mayiko amene zikukhala.
5. Kodi ndi mlandu wotani umene ungakhalepo chifukwa chovota?
5 Mfundo yachitatu yofunika kuilingalira ndiyo yakuti awo amene amavotera nawo munthu pa udindo angakhale ndi mlandu wa zimene munthu am’sankhayo azichita. Pa 1 Timoteo 5:22, Baibulo limati: “Usafulumira kuika manja pa munthu aliyense, kapena usayanjana nazo zoipa za eni; udzisunge wekha woyera mtima.” Akristu ayenera kulingalira mofatsa ngati akufuna kukhala ndi mlandu umenewu.
6. Kodi kuvota pachisankho cha ndale kungakhudze motani umodzi wathu?
6 Yachinayi, Mboni za Yehova zimaona umodzi wawo wachikristu kukhala wamtengo wapatali kwambiri. (Akol. 3:14) Pamene zipembedzo ziloŵa m’ndale, kaŵirikaŵiri zotsatira zake zimakhala kugaŵanika kwa Akristu awo. Motsanzira Yesu Kristu, Mboni za Yehova zimapeŵa kuloŵa m’ndale motero zimasunga umodzi wawo wachikristu.—Mat. 12:25; Yoh. 6:15; 18:36, 37.
7. Kodi kusaloŵerera m’ndale kumatithandiza motani polalikira kwa ena?
7 Mfundo yachisanu komanso yomaliza, ndiyo yakuti kusaloŵa m’ndale kumapatsa Mboni za Yehova mwayi wokhala olimbika kapena kuti ufulu wolankhula za uthenga wofunika wa Ufumu ndi anthu a zipani zonse.—Aheb. 10:35.
8. Kodi Mboni za Yehova m’mayiko ambiri zimasankha kutani?
8 Mwa kulingalira mfundo za m’Malemba zimene zafotokozedwazi, Mboni za Yehova m’mayiko ambiri zimasankha aliyense payekha kusaponya voti pazisankho za ndale, ndipo malamulo a m’mayikowo amalimbikitsa ufulu umenewo.
9. Kodi n’chiyani chingatithandize kuti tikhalebe osaloŵerera m’zochitika za dziko monga Akristu ndiponso kuti tikhalebe ndi ufulu wa kulankhula?
9 Zosankha zaumwini zilizonse zimene Mboni za Yehova zimapanga m’zochitika zosiyanasiyana, zimachita mwanzeru kuti zisaloŵerere m’zochitika za dziko monga Akristu komanso kuti zikhalebe ndi ufulu wa kulankhula. M’zinthu zonse, zimadalira Yehova Mulungu kuti azilimbitse, azipatse nzeru, ndi kuzithandiza kuti zisataye chikhulupiriro chawo mwa njira ina iliyonse. Chotero zimasonyeza chikhulupiriro m’mawu a wamasalmo akuti: “Inu ndinu thanthwe langa ndi linga langa; ndipo chifukwa cha dzina lanu ndiyendetseni bwino, ndipo nditsogolereni.”—Sal. 31:3.