Watchtower LAIBULALE YA PA INTANETI
Watchtower
LAIBULALE YA PA INTANETI
Chichewa
  • BAIBULO
  • MABUKU
  • MISONKHANO
  • km 5/04 tsamba 2
  • Ndandanda ya Misonkhano ya Utumiki

Palibe Vidiyo.

Pepani vidiyoyi ikukanika kutsegula.

  • Ndandanda ya Misonkhano ya Utumiki
  • Utumiki Wathu wa Ufumu—2004
  • Timitu
  • Mlungu Woyambira May 10
  • Mlungu Woyambira May 17
  • Mlungu Woyambira May 24
  • Mlungu Woyambira May 31
  • Mlungu Woyambira June 7
Utumiki Wathu wa Ufumu—2004
km 5/04 tsamba 2

Ndandanda ya Misonkhano ya Utumiki

Mlungu Woyambira May 10

Nyimbo Na. 193

Mph. 10: Zilengezo za pampingo. Zilengezo zina musankhe mu Utumiki Wathu wa Ufumu uno. Ngati mfundo zimene zili pa tsamba 4 zingathandize m’gawo la mpingo wanu, zigwiritseni ntchito posonyeza chitsanzo cha mmene tingagaŵire Nsanja ya Olonda ya May 15 ndi Galamukani! ya June 8. Mungathe kugwiritsanso ntchito maulaliki ena. Mu ulaliki uliwonse, sonyezani njira zosiyana za mmene tingayankhire munthu amene sakufuna kuti tikambirane naye ponena kuti “Ndili ndi chipembedzo changa.”—Onani buku la Kukambitsirana, masamba 18-19. (Ngati magazini ameneŵa sanafike pampingopo, gwiritsani ntchito chitsanzo cha ulaliki cha mu Utumiki Wathu wa Ufumu wa mwezi watha.)

Mph. 15: Zosoŵa za pampingo.

Mph. 20: “‘Kulitsani’ Chikondi.” Kambani mawu oyamba osakwana mphindi imodzi, ndiyeno kambiranani mwa mafunso ndi mayankho. Phatikizanipo ndemanga za m’buku la Lambirani Mulungu, tsamba 150, ndime 14.

Nyimbo Na. 18 ndi pemphero lomaliza.

Mlungu Woyambira May 17

Nyimbo Na. 188

Mph. 10: Zilengezo za pampingo.

Mph. 15: “Sonyezani Kuyamikira Kwanu.” Kambani mawu oyamba osakwana mphindi imodzi, ndiyeno kambiranani mwa mafunso ndi mayankho. Ngati nthaŵi ilipo, pemphani omverawo kupereka ndemanga pa malemba amene sanagwidwe mawu. Pokambirana ndime 3, pemphani munthu mmodzi kapena aŵiri amene achita upainiya wothandiza posachedwapa kufotokoza madalitso amene apeza pochita zimenezo.

Mph. 20: Timaganizirana. (1 Akor. 12:25, 26) Nkhani ndi kukambirana ndi omvera pogwiritsa ntchito buku la Utumiki Wathu, masamba 157-159, pa mutu waung’ono wakuti “Kuderana Nkhaŵa.” Ngakhale kuti anthu a Yehova timakhala m’mbali zonse za dziko lapansi, ndife ogwirizana kwambiri. Tonsefe tiyenera kupempherera abale athu tsiku ndi tsiku. Timafulumiranso kuthandiza abale athu powapatsa zinthu zofunika pamoyo pakagwa zadzidzidzi. Ŵerengani ndi kukambirana malemba amene ali ndi mfundo zazikulu, ndipo phatikizanipo nkhani imodzi kapena ziŵiri za m’mabuku athu zosonyeza kuti timathandizana.

Nyimbo Na. 100 ndi pemphero lomaliza.

Mlungu Woyambira May 24

Nyimbo Na. 128

Mph. 12: Zilengezo za pampingo. Lipoti la maakaunti. Sonyezani chitsanzo cha mmene tingagaŵire Nsanja ya Olonda ya June 1 ndi Galamukani! ya June 8. Akonzeni maulalikiŵa kuti akhale ogwira mtima kwa munthu amene ali m’chipembedzo chinachake cha m’deralo. (Ngati magazini ameneŵa sanafike pampingopo, gwiritsani ntchito chitsanzo cha ulaliki cha mu Utumiki Wathu wa Ufumu wa mwezi watha.)

Mph. 15: “Nyimbo Zimene Zimatsitsimula.” Nkhani ndi kukambirana ndi omvera. Phatikizanipo ndemanga za mu Nsanja ya Olonda ya February 1, 1997, tsamba 27, ndime 1-2.

Mph. 18: Konzekerani Kulalikira Mwamwayi. Nkhani ndi kukambirana ndi omvera pogwiritsa ntchito Utumiki Wathu wa Ufumu wa June 2003, tsamba 3. Konzeranitu kuti anthu angapo asimbe zimene anakumana nazo polalikira mwamwayi. Sonyezani mwachidule mmene tingagwiritsire ntchito thirakiti lakuti Kodi Mukufuna Kudziŵa Zambiri za Baibulo? polalikira mwamwayi.

Nyimbo Na. 211 ndi pemphero lomaliza.

Mlungu Woyambira May 31

Nyimbo Na. 26

Mph. 8: Zilengezo za pampingo. Kumbutsani ofalitsa kupereka malipoti a utumiki wa kumunda a May.

Mph. 17: Moyo ndi Mphatso Imene Tiyenera Kuisamalira. Kukambirana ndi omvera pogwiritsa ntchito buku la Kukambitsirana, masamba 210-211. Kodi mungafotokoze bwanji mmene Yehova amaonera nkhani ya kutaya mimba kwa munthu amene amaganiza kuti mzimayi ali ndi ufulu wosankha zochita pa nkhani zimene zikukhudza thupi lake? Simbani chokumana nacho chimene chili mu Nsanja ya Olonda ya January 1, 2000, tsamba 4, ndime 4-5.

Mph. 20: “Kugaŵira Buku la Phunzirani kwa Mphunzitsi Waluso.” M’mwezi wa June tidzakhala tikugaŵira buku limeneli. Tchulani zinthu zimene azifotokoza pa tsamba 7, ndime 1-3, m’bukuli. Pemphani omvera kupereka ndemanga zofotokoza zimene amakonda m’bukuli. Pendani maulaliki amene aperekedwawo. Sonyezani mmene tingagwiritsire ntchito zithunzizo pogaŵira bukuli. Konzani zoti wachinyamata achitire chitsanzo ulaliki woyambawo, ndipo wachikulire achitire chitsanzo ulaliki umodzi mwa maulaliki enawo. Ngati ulaliki wina wosiyana ndi maulaliki ameneŵa ungathandize kwambiri m’dera lanulo, mungakambirane zimenezo ndipo sonyezani chitsanzo cha ulaliki woterowo m’malo mwa umodzi mwa maulaliki omalizirawo.

Nyimbo Na. 24 ndi pemphero lomaliza.

Mlungu Woyambira June 7

Nyimbo Na. 136

Mph. 5: Zilengezo za pampingo.

Mph. 20: Kodi Mwalankhula ndi Abwana Anu? Nkhani ndi kukambirana ndi omvera ndipo ikambidwe ndi mkulu. Gwiritsani ntchito nkhani yakuti “Kodi Mudzapezekapo?” Phatikizanipo ndemanga za m’buku la Sukulu ya Utumiki patsamba 67.

Mph. 20: Gwiritsani Ntchito Mafanizo Ogwira Mtima Pophunzitsa. Nkhani ndi kukambirana ndi omvera pogwiritsa ntchito Nsanja ya Olonda ya September 1, 2002, masamba 22-24. Kodi ndi zinthu zinayi ziti zimene zimachititsa fanizo kukhala logwira mtima? N’chifukwa chiyani zimathandiza fanizolo likakhala losavuta? Kodi tingapeze kuti mafanizo abwino? Pendani zina mwa zitsanzo zimene zili m’bokosi patsamba 23, ndipo kambiranani chifukwa chake mafanizo onsewo ndi ogwira mtima.

Nyimbo Na. 133 ndi pemphero lomaliza.

    Mabuku a Chichewa (1974-2025)
    Tulukani
    Lowani
    • Chichewa
    • Tumizirani Ena
    • Zimene Mumakonda
    • Copyright © 2025 Watch Tower Bible and Tract Society of Pennsylvania
    • Zoyenera Kutsatira
    • Nkhani Yosunga Chinsinsi
    • Privacy Settings
    • JW.ORG
    • Lowani
    Tumizirani Ena