Watchtower LAIBULALE YA PA INTANETI
Watchtower
LAIBULALE YA PA INTANETI
Chichewa
  • BAIBULO
  • MABUKU
  • MISONKHANO
  • km 8/04 tsamba 2
  • Ndandanda ya Misonkhano ya Utumiki

Palibe Vidiyo.

Pepani vidiyoyi ikukanika kutsegula.

  • Ndandanda ya Misonkhano ya Utumiki
  • Utumiki Wathu wa Ufumu—2004
  • Timitu
  • Mlungu Woyambira August 9
  • Mlungu Woyambira August 16
  • Mlungu Woyambira August 23
  • Mlungu Woyambira August 30
  • Mlungu Woyambira September 6
Utumiki Wathu wa Ufumu—2004
km 8/04 tsamba 2

Ndandanda ya Misonkhano ya Utumiki

Mlungu Woyambira August 9

Nyimbo Na. 57

Mph. 10: Zilengezo za pampingo ndi zilengezo zina zosankhidwa mu Utumiki Wathu wa Ufumu uno. Ngati mfundo zimene zili patsamba 8 zingathandize m’gawo la mpingo wanu, zigwiritseni ntchito posonyeza chitsanzo cha mmene tingagaŵire Nsanja ya Olonda ya August 15 ndi Galamukani! ya September 8. Mungathe kugwiritsanso ntchito maulaliki ena. Tchulani makonzedwe a zopereka zaufulu. Kumbutsani omvera kuti adzabweretse bulosha la Mulungu Amafunanji mlungu wa maŵa. (Ngati magazini ameneŵa sanafike pampingopo, gwiritsani ntchito chitsanzo cha ulaliki cha mu Utumiki Wathu wa Ufumu wa mwezi watha.)

Mph. 15: “Kupirira Kuli ndi Mphoto Yake.” Kambani mawu oyamba osakwana mphindi imodzi, ndiyeno kambiranani mwa mafunso ndi mayankho. Phatikizanipo ndemanga zachidule kuchokera mu Nsanja ya Olanda ya December 15, 2000, masamba 22 ndi 23, ndime 15 mpaka 18.

Mph. 20: Kugwiritsa Ntchito Mathirakiti Kuyambitsira Maphunziro a Baibulo. Nkhani ndi kukambirana ndi omvera yochokera mu Utumiki Wathu wa Ufumu wa November 2001 masamba 3 ndi 4. Fotokozani kuti ndife okonzeka kusintha mogwirizana ndi wophunzira aliyense payekha, monga mmene afotokozera m’ndime 5. Sonyezani chitsanzo chimodzi kapena ziŵiri zachidule kuchokera m’ndime 8 mpaka 10. Ngati pali ulaliki wina wogwira mtima kwanuko, ufotokozeni ndipo chitirani chitsanzo umenewo m’malo mwa umene uli m’ndimezo. Pemphani omvera kuti afotokoze zokumana nazo zimene apeza pogwiritsa ntchito thirakiti lakuti Kodi Mukufuna Kudziŵa Zambiri za Baibulo?

Nyimbo Na. 74 ndi pemphero lomaliza.

Mlungu Woyambira August 16

Nyimbo Na. 189

Mph. 10: Zilengezo za pampingo.

Mph. 15: Khomerezani Choonadi mwa Ana Anu. Nkhani yochokera m’buku la Chimwemwe cha Banja, masamba 55 mpaka 59. Fotokozani njira zinayi za mmene makolo angathandizire ana awo kupanga ubwenzi wolimba ndi Yehova mwa kuchita zimene nkhaniyo ikunena.

Mph. 20: “Kuchititsa Maphunziro a Baibulo Opita Patsogolo​—Gawo 2.” Kambani mawu oyamba osakwana mphindi imodzi, ndiyeno kambiranani mwa mafunso ndi mayankho. Phatikizanipo chitsanzo cha mphindi zisanu. Wofalitsa akufunsa mkulu mmene angathandizire wophunzira kupita patsogolo. Mkuluyo akufotokoza kuti vuto lofala kwambiri ndilo kutenga nthaŵi yaitali paphunziro ukufotokoza mfundo zimene zili zosafunika kwenikweni. Mwa kugwiritsa ntchito bulosha la Mulungu Amafunanji, phunziro 9, asonyeze wofalitsayo mmene (1) angatsindikire mfundo zazikulu za m’nkhaniyo, (2) mmene angagwiritsire ntchito malemba osagwidwa mawu mogwira mtima, ndi (3) mmene angagwirizanitsire phunzirolo ndi zosowa za wophunzirayo. Afotokozenso kuti m’pofunika kukonzekera bwino nthaŵi iliyonse pamene akukachititsa phunziro.

Nyimbo Na. 85 ndi pemphero lomaliza.

Mlungu Woyambira August 23

Nyimbo Na. 33

Mph. 15: Zilengezo za pampingo. Lipoti la maakaunti. Sonyezani chitsanzo cha mmene tingagaŵire Nsanja ya Olonda ya September 1 ndi Galamukani! ya September 8. M’chitsanzo chimodzi, sonyezani mmene tingalalikire mphunzitsi kusukulu. (Ngati magazini ameneŵa sanafike pampingopo, gwiritsani ntchito chitsanzo cha ulaliki cha mu Utumiki Wathu wa Ufumu wa mwezi watha.)

Mph. 10: “Njira Yatsopano Yobwerezera Zophunziridwa pa Misonkhano Yadera.” Nkhani ndi kukambirana ndi omvera kuchokera pa nkhani ya patsamba 4. Tchulani madeti a msonkhano wadera ndi tsiku la msonkhano wapadera ngati aperekedwa. Amene akufuna kubatizidwa ayenera kudziŵitsa woyang’anira wotsogolera madetiŵa asanafike.

Mph. 20: “Nzeru Yochokera Kumwamba Ndi Yololera.” (Yak. 3:17, NW) Kambani mawu oyamba osakwana mphindi ziŵiri okhudza ndime ziŵiri zoyambirira, ndiyeno kambiranani mwa mafunso ndi mayankho. Gwiritsani ntchito mafunso otsatiraŵa pokambirana ndime 3 mpaka 7: Kodi kukhala wololera kumatanthauza chiyani? N’chifukwa chiyani khalidwe limeneli lili lofunika mu utumiki? Kodi chitsanzo cha mtumwi Paulo chikutiphunzitsa chiyani? Kodi ofalitsa angachite chiyani posonyeza kuganizira moyo wa anthu a m’gawolo? Kodi tingawathandize motani ophunzira Baibulo kukhala ololera? Konzani pasadakhale zoti munthu mmodzi kapena aŵiri adzasimbe zokumana nazo zawo zosonyeza phindu la kuchita zinthu mololera.

Nyimbo Na. 220 ndi pemphero lomaliza.

Mlungu Woyambira August 30

Nyimbo Na. 90

Mph. 10: Zilengezo za pampingo. Kumbutsani ofalitsa kupereka malipoti a utumiki wa kumunda a August.

Mph. 15: “Sukulu Yophunzitsa Utumiki—Khomo Lalikulu Loloŵera M’ntchito Yochuluka.” Nkhani ndi kukambirana ndi omvera. Tchulani za msonkhano wa amene akufuna kuloŵa Sukulu Yophunzitsa Utumiki umene umakhalapo pamsonkhano wadera. Limbikitsani amene ali oyenerera kuti akapezeke pamsonkhano umenewu.

Mph. 20: Kodi Munapindula? Kukambirana ndi omvera. Bwerezani mfundo zotsatirazi zimene zinatuluka mu Utumiki Wathu wa Ufumu m’chaka chautumiki chapitachi: Lembani mawu oyamba a ulaliki wanu pa kapepala. (km-CN 10/03 tsa. 8) Yamikirani munthu payekha, molunjika, ndiponso kuchokera pansi pa mtima. (km-CN 11/03 tsa. 1) Lalikirani nthaŵi imene anthu amakonda kupezeka panyumba. (km-CN 12/03 tsa. 1) Khalani ndi nthaŵi yeniyeni yoŵerenga Baibulo, yokonzekera misonkhano, ndiponso ya utumiki wa kumunda. (km-CN 1/04 tsa. 4) Gwiritsani ntchito bulosha la “Onani Dziko Lokoma” pamene mukuchita phunziro laumwini ndi pamene mukuŵerenga Baibulo. (km-CN 3/04 tsa. 2) Khalani ndi cholinga choŵerenga Baibulo lonse lathunthu. (km-CN 4/04 tsa. 1) Kulalikira m’gawo la malonda. (km-CN 7/04 tsa. 4) Gwiritsani ntchito mathirakiti kuyambitsira maphunziro a Baibulo. (km-CN 8/04 tsa. 2) Pemphani omvera afotokoze phindu limene apeza mwa kugwiritsa ntchito mfundo zimenezi.

Nyimbo Na. 145 ndi pemphero lomaliza.

Mlungu Woyambira September 6

Nyimbo Na. 197

Mph. 5: Zilengezo za pampingo.

Mph. 15: Zosoŵa za pampingo.

Mph. 25: “Onetsani Mzimu wa Upainiya.” Kambani mawu oyamba osakwana mphindi imodzi, ndiyeno kambiranani mwa mafunso ndi mayankho. Mwachidule funsani mpainiya mmodzi kapena aŵiri. Auzeni afotokoze mmene zitsanzo za makolo awo, akulu, ndi za anthu ena zawalimbikitsira kuti achite utumiki wa nthaŵi zonse.

Nyimbo Na. 142 ndi pemphero lomaliza.

    Mabuku a Chichewa (1974-2025)
    Tulukani
    Lowani
    • Chichewa
    • Tumizirani Ena
    • Zimene Mumakonda
    • Copyright © 2025 Watch Tower Bible and Tract Society of Pennsylvania
    • Zoyenera Kutsatira
    • Nkhani Yosunga Chinsinsi
    • Privacy Settings
    • JW.ORG
    • Lowani
    Tumizirani Ena