Ndandanda ya Misonkhano ya Utumiki
Dziwani Izi: M’miyezi ikubwerayi Utumiki Wathu wa Ufumu udzakhala ndi ndandanda ya Misonkhano ya Utumiki ya mlungu uliwonse. Mipingo ingasinthe moyenera kuti ikapezeke pa Msonkhano Wachigawo wakuti “Kumvera Mulungu.” Ngati n’koyenera, gwiritsani ntchito mphindi 15 pa Msonkhano wa Utumiki womaliza musanapite ku msonkhano wachigawo kuti muonenso malangizo oyenera ndi zikumbutso za mu mphatika ya Utumiki Wathu wa Ufumu uno amene akukhudza mpingo wanuwo. Pakadutsa mwezi umodzi kapena iwiri utatha msonkhano wachigawo, gwiritsani ntchito mphindi 15 mpaka 20 za mu Msonkhano wa Utumiki (mwina mungagwiritse ntchito chigawo cha zosowa za pampingo) kuti mubwereze mfundo zazikulu za msonkhano wachigawo zimene ofalitsa aziona kukhala zothandiza mu utumiki wa kumunda. Pokonzekera kukambiranako, tonse tikalembe notsi zofunika kumsonkhano wachigawo, komanso mfundo zapadera zimene tikufuna kuzigwiritsa ntchito mu utumiki wa kumunda. Mbali yapadera ya mu Msonkhano wa Utumiki imeneyi idzatipatsa mwayi wofotokoza mmene tikugwiritsira ntchito mfundo zimene tinaziphunzira kumsonkhano ndiponso kufotokoza mmene mfundozo zathandizira utumiki wathu kukhala wogwira mtima. Zidzakhala zolimbikitsa kumva mmene ena agwiritsira bwino ntchito malangizo amene tinalandira kumsonkhano ndiponso zidzalimbikitsa ena kuti agwiritse ntchito uphungu ndi mfundo zimene zinaperekedwa pa pulogalamu ya msonkhano wachigawo.
Mlungu Woyambira July 11
Mph. 10: Zilengezo za pampingo. Zilengezo zina musankhe mu Utumiki Wathu wa Ufumu uno. Gwiritsani ntchito mfundo zimene zili patsamba 8 (ngati zingakhale zothandiza m’gawo lanu) kuchitira chitsanzo choonetsa mmene tingagawire Nsanja ya Olonda ya July 15 ndi Galamukani! ya August 8. Mungathe kugwiritsanso ntchito maulaliki ena amene angakhale othandiza. M’chitsanzo chilichonse, sonyezani njira zosiyana za mmene tingayankhire munthu wofuna kuimitsa kukambirana ponena kuti “Ndili wotanganitsidwa.”—Onani buku la Kukambitsirana, tsa. 19 ndi 20. (Ngati magazini amenewa sanafike pampingopo, gwiritsani ntchito chitsanzo cha ulaliki cha mu Utumiki Wathu wa Ufumu wa mwezi watha.)
Mph. 15: “Kodi Mwapemphapo Wina Aliyense Kuti Muziphunzira Naye Baibulo?” Nkhani ndi kukambirana ndi omvera. Ikambidwe ndi woyang’anira utumiki. Mukamaliza kukambirana ndime 4, pemphani wofalitsa kuchita chitsanzo cha mmene tingayambitsire phunziro la Baibulo pogwiritsa ntchito ulaliki wotchulidwa m’ndimeyo.
Mph. 20: “Kufikira Anthu Ambiri Mmene Tingathere.” Kambani mawu oyamba osakwana mphindi imodzi, ndiyeno kambiranani mwa mafunso ndi mayankho. Pokambirana ndime 5, kambani mfundo zomwe mukuona kuti zikhoza kugwira ntchito m’gawo lanu zimene zili mu Utumiki Wathu wa Ufumu wa June 2005, tsamba 8.
Nyimbo Na. 88 ndi pemphero lomaliza.
Mlungu Woyambira July 18
Mph. 7: Zilengezo za pampingo. Kambani mwachidule mfundo zochokera mu Nsanja ya Olonda ya August 15, 2000, tsamba 32. Fotokozani phindu lotsatira pulogalamu yowerenga Baibulo tsiku ndi tsiku, ngakhale pa nthawi imene tili pa tchuthi ndiponso pa nthawi imene sitikuchita ntchito yathu ya masiku onse.
Mph. 8: Bokosi la Mafunso. Nkhani yokambidwa ndi woyang’anira wotsogolera.
Mph. 30: “Yamikani Yehova mu Msonkhano Waukulu.” Yokambidwa ndi mlembi wa mpingo. Tchulani msonkhano wachigawo umene mpingo wanu wapemphedwa kudzapita. Kambiranani ndimezo mofanana ndi mmene timachitira Phunziro la Nsanja ya Olonda. Uzani wina kuti aziwerenga ndimezo. Tchulani mfundo zili m’bokosi lakuti “Zikumbutso za Msonkhano Wachigawo.”
Nyimbo Na. 10 ndi pemphero lomaliza.
Mlungu Woyambira July 25
Mph. 15: Zilengezo za pampingo. Werengani lipoti la maakaunti ndi makalata oyamikira zopereka ochokera ku nthambi. Mwa kugwiritsa ntchito mfundo zimene zili patsamba 8 (ngati zingakhale zothandiza m’gawo lanu), sonyezani chitsanzo choonetsa mmene tingagawire Nsanja ya Olonda ya August 1 ndi Galamukani! ya August 8. Mungathe kugwiritsanso ntchito maulaliki ena amene angakhale othandiza. M’chitsanzo chimodzi, sonyezani akugawira magazini mu ulaliki wa mwamwayi kumsika kapena malo ena alionse amene kumapezeka anthu ambiri. (Ngati magazini amenewa sanafike pampingopo, gwiritsani ntchito chitsanzo cha ulaliki cha mu Utumiki Wathu wa Ufumu wa mwezi watha.)
Mph. 10: Khomerezani Choonadi mu Mtima mwa Ana Anu. (Deut. 6:7) Nkhani yokambidwa ndi mkulu kuchokera mu Nsanja ya Olonda ya August 15, 2002, tsamba 30 ndi 31. Tchulani mfundo za m’Malemba zimene zingathandize kholo lachikristu mmene lingaphunzitsire mwana wake ngati kholo linalo si Mboni.
Mph. 20: “Ngongole Imene Tili Nayo kwa Ena.” Kambani mawu oyamba osakwana mphindi imodzi, ndiyeno kambiranani mwa mafunso ndi mayankho. Phatikizanipo ndemanga zochokera mu Nsanja ya Olonda ya July 1, 2000, tsamba 11, ndime 13.
Nyimbo Na. 82 ndi pemphero lomaliza.
Mlungu Woyambira August 1
Mph. 10: Zilengezo za pampingo. Kumbutsani ofalitsa kupereka malipoti a utumiki wa kumunda a mwezi wa July. Pemphani omvera kutsegula pa tsamba 70 m’buku la Sukulu ya Utumiki, ndipo mwa kukambirana ndi omvera, pendani ndime 1 ndi 2 komanso bokosi lakuti “Mmene Mungayankhire pa Misonkhano.”
Mph. 15: “Thandizani Ana Anu Kupita Patsogolo mu Utumiki.” Nkhani ndi kukambirana ndi omvera. Phatikizanipo chitsanzo chosonyeza kholo ndi mwana akuchita ulaliki wosavuta. Pomaliza, khololo lifotokoze mwachidule za dongosolo la zopereka.
Mph. 20: “Kuchititsa Maphunziro a Baibulo Opita Patsogolo—Gawo 10.” Kambani mawu oyamba osakwana mphindi imodzi, ndiyeno kambiranani mwa mafunso ndi mayankho. Phatikizanipo chitsanzo chosonyeza anthu akuyeserera ulaliki. Chikhale choti achiyamba kale ndipo akupitiriza. Pamene wophunzira akuyeserera ulalikiwo, wochititsa phunziroyo, amene wakhala mbali ya mwininyumba, akane monga mmene ambiri amakanira mukawapeza mu utumiki. Wophunzirayo asonyeze kuti akusowa chonena, ndiyeno wochititsa phunziroyo amufotokozere mmene angachitire zikakhala choncho. Kuphatikiza pamenepo, konzani pasadakhale zoti munthu mmodzi kapena awiri adzafotokoze mmene anaphunzirira pamene anayamba kupita mu utumiki wa nyumba ndi nyumba.
Nyimbo Na. 218 ndi pemphero lomaliza.