Ndandanda ya Misonkhano ya Utumiki
Mlungu Woyambira November 14
Mph. 10: Zilengezo za pampingo. Zilengezo zina musankhe mu Utumiki Wathu wa Ufumu uno. Gwiritsani ntchito mfundo zimene zili patsamba 4 (ngati zingakhale zothandiza m’gawo lanu) kuchitira chitsanzo chosonyeza mmene tingagawire Nsanja ya Olonda ya November 15 ndi Galamukani! ya December 8. Mungagwiritsenso ntchito zitsanzo zina zothandiza. Pachitsanzo chilichonse, sonyezani njira zosiyanasiyana za mmene mungachitire ndi anthu olepheretsa kukambirana amene anganene kuti “Sindili wokondwera ndi chipembedzo.”—Onani buku la Kukambitsirana, mas. 16 ndi 17. (Ngati magazini amenewa sanafike pampingopo, gwiritsani ntchito chitsanzo cha ulaliki cha mu Utumiki Wathu wa Ufumu wa mwezi watha.)
Mph. 15: Zopereka Zimene Zimakondweretsa Mulungu. Nkhani yokambidwa ndi mkulu kuchokera mu Nsanja ya Olonda ya November 1, 2005, masamba 26 mpaka 30.
Mph. 20: “Lengezani Ulemerero wa Yehova.” Kambani mawu oyamba osakwana mphindi imodzi, ndiyeno kambiranani mwa mafunso ndi mayankho. Mukafika pa ndime 4, pemphani omvera kuti afotokoze zokumana nazo zachidule zosonyeza mmene khalidwe labwino lingatsegulire njira yolalikira.
Nyimbo Na. 24 ndi pemphero lomaliza.
Mlungu Woyambira November 21
Mph. 10: Zilengezo za pampingo.
Mph. 20: Zimene Mungachite Kuti Yehova Akhale Mulungu Wanu. Nkhani yokambidwa ndi mkulu kuchokera mu Nsanja ya Olonda ya April 1, 2005, masamba 25 mpaka 28. Fotokozani mmene tingagwiritsire ntchito zitsanzo za Abrahamu, Davide, ndi Eliya m’moyo wathu.
Mph. 15: “Sonyezani Ena Chidwi mwa Kuyang’anitsitsa Zinthu.” Kambani mawu oyamba osakwana mphindi imodzi, ndiyeno kambiranani mwa mafunso ndi mayankho. Chitani chitsanzo chosonyeza wofalitsa akuyang’anitsitsa zinthu zimene zikum’thandiza kuzindikira zimene mwininyumba amakonda ndiyeno alankhule mogwirizana ndi zimene waonazo.
Nyimbo Na. 67 ndi pemphero lomaliza.
Mlungu Woyambira November 28
Mph. 12: Zilengezo za pampingo. Werengani lipoti la maakaunti ndi makalata oyamikira zopereka ochokera ku nthambi. Kumbutsani ofalitsa kupereka malipoti a utumiki wa kumunda a mwezi wa November. Gwiritsani ntchito mfundo zimene zili patsamba 4 (ngati zingakhale zothandiza m’gawo lanu) kuchitira chitsanzo chosonyeza mmene tingagawire Nsanja ya Olonda ya December 1 ndi Galamukani! ya December 8. Mungagwiritsenso ntchito zitsanzo zina zothandiza. Tchulanipo za dongosolo la zopereka. (Ngati magazini amenewa sanafike pampingopo, gwiritsani ntchito chitsanzo cha ulaliki cha mu Utumiki Wathu wa Ufumu wa mwezi watha.)
Mph. 15: “Kodi Tingathandize Motani?” Nkhani. Fotokozani zitsanzo zingapo za kuyesetsa kwa atumiki a Yehova kupereka thandizo kwa okhulupirira anzawo amene anafunikira thandizo. (Onani Galamukani! ya August 8, 2003, masamba 10 mpaka 15; December 8, 2002, masamba 13 mpaka 18; ndi yachingelezi ya October 22, 2001, masamba 23 mpaka 27. Mungagwiritsenso ntchito zofalitsa zina.) Ndiyeno kambiranani mfundo zazikulu za mu Utumiki Wathu wa Ufumu uno m’nkhani imene ili patsamba 3. Tsindikani mfundo yakuti ngati aliyense akufuna kupereka ndalama zothandizira anthu amene akuvutika, ndi bwino kupereka ndalamazo ku thumba la ntchito ya padziko lonse.
Mph. 18: Kulalikira Uthenga Wabwino mu December. Nkhani ndi kukambirana ndi omvera. Kuyamba ndi nkhani ya mphindi zisanu, fotokozani mwachidule mfundo zotsatirazi zochokera mu nkhani yakuti “Mmene Tingagwiritsire Ntchito Zitsanzo za Maulaliki,” yopezeka patsamba 8 mu Utumiki Wathu wa Ufumu wa January 2005: (1) Tingakhale ogwira mtima kwambiri ngati pogwiritsa ntchito zitsanzo za maulaliki, tilankhula m’mawu athuathu. (2) Tiyenera kugwiritsa ntchito luntha lathu kuti tisinthe ulaliki wathu mogwirizana ndi zimene zili zoyenera kudera kwathu. (3) Tiyenera kuganizira za chikhalidwe ndi kaganizidwe ka anthu a m’dera lathu. (4) Tiyenera kuwerenga bwinobwino mutu umene tikufuna kukagwiritsa ntchito ndi kupezamo mfundo zimene zingapatse anthu chidwi. (5) Palibe lamulo lakuti tizigwiritsa ntchito zitsanzo zokhazo zomwe tapatsidwa. Ndiyeno kambiranani ndi omvera za momwe mungagwiritsire ntchito mfundo zimenezi pofalitsa mabuku ogawira mu December. Mungagwiritse ntchito zitsanzo za m’mphatika ya Utumiki Wathu wa Ufumu wa January 2005 kapena kalalikidwe kena kalikonse kamene kangakhale kogwira mtima kwanuko. Chitani chitsanzo chimodzi kapena ziwiri.
Nyimbo Na. 123 ndi pemphero lomaliza.
Mlungu Woyambira December 5
Mph. 10: Zilengezo za pampingo.
Mph. 15: Zosowa za pampingo.
Mph. 20: “Zimene Utumiki Wathu Umakwaniritsa.” Kambani mawu oyamba osakwana mphindi imodzi, ndiyeno kambiranani mwa mafunso ndi mayankho. Mukafika pa ndime 5, phatikizanipo mfundo za mu Nsanja ya Olonda ya February 15, 2004, tsamba 32.
Nyimbo Na. 26 ndi pemphero lomaliza.