Watchtower LAIBULALE YA PA INTANETI
Watchtower
LAIBULALE YA PA INTANETI
Chichewa
  • BAIBULO
  • MABUKU
  • MISONKHANO
  • km 12/05 tsamba 7
  • Zilengezo

Palibe Vidiyo.

Pepani vidiyoyi ikukanika kutsegula.

  • Zilengezo
  • Utumiki Wathu wa Ufumu—2005
Utumiki Wathu wa Ufumu—2005
km 12/05 tsamba 7

Zilengezo

◼ Mabuku ogawira mu December: Gawirani buku la Munthu Wamkulu Koposa Onse Amene Anakhalako. January: Gawirani bulosha la Dikirani! February: Gawirani buku la Yandikirani kwa Yehova. March: Gawirani buku latsopano la Kodi Baibulo Limaphunzitsa Chiyani Kwenikweni? Yetsetsani kuyambitsa maphunziro a Baibulo.

◼ Popeza kuti Timapepala Toitanira Anthu ku Chikumbutso SITIDZATUMIZIDWA kuchokera ku ofesi ya nthambi, mipingo iyambe kuitanitsa timapepala ta 2006 pa oda yawo ya mabuku ya January. Timapepalati tidzakhalapo m’Chichewa, Chingelezi, Chiswahili, ndi m’Chitumbuka. Muyenera kuitanitsa m’mipukutu ya timapepala 100 m’chinenero chilichonse. Chonde itanitsani mosamala popeza kuti anapangira anthu achidwi okha basi, osati kugawira chisawawa.

◼ Dziwani kuti Chikumbutso cha chaka cha 2007 chidzakhala pa Lolemba, pa April 2, dzuwa litalowa. Taneneratu zimenezi kuti abale apezeretu malo ena ngati mipingo ingapo imagwiritsa ntchito Nyumba ya Ufumu imodzi ndipo pakufunika kupeza malo ena. Akapeza malo ena, akulu ayenera kugwirizana ndi eni malowo n’kutsimikizira kuti mwambowu usadzadodometsedwe ndi zochitika zina pamalowo kuti Chikumbutsocho chidzachitike bwinobwino ndi mwadongosolo.

◼ Popeza Chikumbutso ndi mwambo wapadera, bungwe la akulu posankha wokamba nkhani liyenera kusankha mkulu yemwe alidi woyenerera, osati kungosinthana kapena kuti chaka chilichonse azingokamba mbale mmodzimodzi yemweyo. Ngati pali wodzozedwa amene ndi mkulu komanso angathe kukamba nkhaniyo asankhe ameneyo.

◼ Mipingo ingakhale italandira kapena ilandira timapepala toitanira anthu. Tingagwiritse ntchito timapepalati kuitanira anthu ku misonkhano. Pa timapepalati mumalembapo nthawi za misonkhano, malo kapena adiresi ya Nyumba ya Ufumu. Ngakhale kuti mpingo uliwonse ulandira timapepala timeneti, m’tsogolo muno mpingo uzioda wokha timapepalati pogwiritsa ntchito Fomu Yofunsira Mabuku (S-14). Chizindikiro cha kapepalaka ndi sf.

    Mabuku a Chichewa (1974-2025)
    Tulukani
    Lowani
    • Chichewa
    • Tumizirani Ena
    • Zimene Mumakonda
    • Copyright © 2025 Watch Tower Bible and Tract Society of Pennsylvania
    • Zoyenera Kutsatira
    • Nkhani Yosunga Chinsinsi
    • Privacy Settings
    • JW.ORG
    • Lowani
    Tumizirani Ena