Watchtower LAIBULALE YA PA INTANETI
Watchtower
LAIBULALE YA PA INTANETI
Chichewa
  • BAIBULO
  • MABUKU
  • MISONKHANO
  • km 12/05 tsamba 6
  • Kubwereza za M’sukulu ya Utumiki wa Mulungu

Palibe Vidiyo.

Pepani vidiyoyi ikukanika kutsegula.

  • Kubwereza za M’sukulu ya Utumiki wa Mulungu
  • Utumiki Wathu wa Ufumu—2005
Utumiki Wathu wa Ufumu—2005
km 12/05 tsamba 6

Kubwereza za M’sukulu ya Utumiki wa Mulungu

Mafunso otsatirawa mudzawakambirana pa Sukulu ya Utumiki wa Mulungu ya mlungu woyambira December 26, 2005. Woyang’anira sukulu adzatsogolera kubwereza nkhani zomwe zakambidwa m’kati mwa milungu ya November 7 mpaka December 26, 2005. Kubwerezaku kudzakhala kwa mphindi 30. [Dziwani izi: Pa funso lomwe kumapeto kwake silikusonyeza buku lililonse lomwe mwatengedwa nkhaniyo, ndiye kuti muyenera mufufuze nokha kuti mupeze mayankho ake.—Onani buku la Sukulu ya Utumiki, mas. 36-7.]

LUSO LA KULANKHULA

1. Kodi tingatani kuti tizilimbikitsa ena “mwa chikondi”? (Filem. 9) [be-CN tsa. 266]

2. Kodi tingalimbikitse ena ndi ‘chiphunzitso cholamitsa’ m’njira ziti? (Tito 1:9) [be-CN tsa. 267 ndime 1-2]

3. N’chifukwa chiyani kuli kofunika kuti nkhani zathu zizikhala zolimbikitsa, ndipo tingachite zimenezi motani? [be-CN tsa. 268 ndime 1-3, bokosi]

4. Potsanzira Mose, kodi kuthandiza ena kukumbukira zimene Yehova wachitira anthu ake kumawalimbikitsa motani? (Deut. 3:28; 31:1-8) [be-CN tsa. 268 ndime 5–tsa. 269 ndime 2]

5. N’chifukwa chiyani kulankhula moyamikira zimene Yehova akuchita pakali pano ndiponso zimene adzachite m’tsogolo kumalimbikitsa omvera athu? [be-CN mas. 270-271]

NKHANI NA. 1

6. Kodi mfungulo zimene Yesu anapatsa Petro zinali chiyani ndipo anazigwiritsa ntchito bwanji? [gt-CN tsa. 59]

7. N’chifukwa chiyani masomphenya a kusandulika kwa Yesu ali olimbikitsa kwambiri kwa ophunzira ake? [gt-CN tsa. 60]

8. Kodi chikhulupiriro chingakhale champhamvu mpaka pati? [gt-CN tsa. 61]

9. Kodi tikuphunzirapo chiyani pa Mateyu 18:1-5? [gt-CN tsa. 62]

10. Kodi nkhani ya kukhumudwitsa wamng’ono n’njaikulu bwanji? [gt-CN tsa. 63]

KUWERENGA BAIBULO KWA MLUNGU NDI MLUNGU

11. Pakuti Yehova sanalole kuti Davide am’mangire kachisi, kodi zimenezi zikutanthauza kuti sanasangalale ndi nkhondo zimene Davide anamenya? (1 Mbiri 22:6-10)

12. M’pemphero lake lopereka kachisi kwa Yehova, kodi Solomo anazindikira bwanji kuti Yehova sangosamala zosowa za atumiki ake monga gulu, koma amasamalanso za vuto lililonse la munthu aliyense amene amamuopa? (2 Mbiri 6:29, 30)

13. Kodi “ziwanda” zotchulidwa pa 2 Mbiri 11:15 zinali chiyani?

14. Popeza kuti ulamuliro wa Basa unayamba ‘m’chaka chachitatu cha Asa’ ndipo analamulira zaka 24 zokha, zikutheka bwanji kuti Basa “anakwera kulimbana ndi Yuda” mu “chaka cha makumi atatu mphambu zisanu ndi chimodzi cha Asa”? (1 Maf. 15:33; 2 Mbiri 16:1)

15. Kodi lemba la 2 Mbiri 20:22, 23 limamveketsa bwino motani zimene zichitikire dziko la Satana posachedwapa?

    Mabuku a Chichewa (1974-2025)
    Tulukani
    Lowani
    • Chichewa
    • Tumizirani Ena
    • Zimene Mumakonda
    • Copyright © 2025 Watch Tower Bible and Tract Society of Pennsylvania
    • Zoyenera Kutsatira
    • Nkhani Yosunga Chinsinsi
    • Privacy Settings
    • JW.ORG
    • Lowani
    Tumizirani Ena