Bokosi la Mafunso
◼ Kodi ndi bwino kusonkhanitsa mfundo zomwe zidzagwiritsidwe ntchito mu Sukulu ya Utumiki wa Mulungu n’kuzigawira kwa anthu ena?
N’zololeka kuchita zimenezi kuti mupatse anthu a m’banja mwanu ndi anzanu ochepa. Komabe, mfundo zimenezi siziyenera kugawiridwa kwa anthu mwachisawawa kapena kugulitsidwa, chifukwa kuchita zimenezo kungakhale kuphwanya malamulo ofalitsira mabuku.—Aroma 13:1.
Pa nkhani zina zoti zikambidwe mu Sukulu ya Utumiki wa Mulungu, amangoikapo mutu wokha basi, popanda kusonyeza komwe nkhaniyo yachokera. Kodi zingakhale zothandiza kuti munthu wina alembe m’ndandanda wa mabuku amene mukupezeka nkhaniyo kapena kusonkhanitsa mfundo zimene anthu amene apatsidwa nkhaniyo angagwiritse ntchito? Ayi. Ndiponso sizingakhale zoyenera kusonkhanitsa mayankho a mafunso a Kubwereza kwa m’Sukulu ya Utumiki wa Mulungu n’kupatsa anthu ena, chifukwa kuchita zimenezi sikungawathandize kukumbukira mfundo zofunika. Anthu a m’sukulu ayenera kufufuza okha zinthu. Imeneyi ndi mbali yofunika ya maphunziro amene Yehova amapereka kudzera m’sukuluyi kuti atithandize kulankhula ndi “lilime la ophunzira.”—Yes. 50:4.