Ndandanda ya Misonkhano ya Utumiki
Mlungu Woyambira September 11
Mph. 10: Zilengezo za pampingo. Zilengezo zina musankhe mu Utumiki Wathu wa Ufumu uno. Chitani chitsanzo chosonyeza momwe tingagawire Nsanja ya Olonda ya September 15 ndi Galamukani! ya September pogwiritsa ntchito mfundo zimene zili pa tsamba 4 kapena ulaliki wina uliwonse umene ungakhale wothandiza m’gawo lanu. M’chitsanzo chimodzi, sonyezani mmene tingayankhire munthu amene akufuna kuti tisakambirane naye ponena kuti “Ndili ndi chipembedzo changa.”—Onani buku la Kukambitsirana tsamba 18 mpaka 19. (Ngati mpingo wanu sunalandire magazini tatchulawa gwiritsirani ntchito zitsanzo zimene zinatchulidwa mu Utumiki Wathu wa Ufumu wa mwezi watha.)
Mph. 20: Kupindula ndi Msonkhano wa Utumiki ndi Sukulu ya Utumiki wa Mulungu. Nkhani ndi kukambirana ndi omvera yotengedwa m’buku la Gulu Lochita Chifuniro cha Yehova, kuchokera pa kamutu ka pa tsamba 64 mpaka pa kamutu ka pa tsamba 69.
Mph. 15: Kalata Yochokera ku Nthambi. Nkhani ndi kukambirana ndi omvera kuchokera pa kalata yomwe ili pa tsamba loyamba la Utumiki Wathu wa Ufumu uno. Funsani mafunso aliyense wa mu mpingo wanu amene anathandiza nawo pa ntchito yomanga Nyumba ya Ufumu.
Nyimbo Na. 126 ndi pemphero lomaliza.
Mlungu Woyambira September 18
Nyimbo 213
Mph. 5: Zilengezo za pampingo.
Mph. 15: Kodi Tinachita Zotani Chaka Chatha? Woyang’anira utumiki atchule zinthu zimene zinachitika chaka chautumiki chapitachi, makamaka zinthu zolimbikitsa zomwe zinachitika mu utumiki. Ayamikire abale pamene pakufunika kuyamikira. Tchulani mbali imodzi kapena ziwiri zomwe zikufunika kugwirirapo ntchito chaka chikubwerachi. Tchulani za ntchito ya apainiya, ndipo ayamikireni chifukwa cha ntchito yawo yabwino. Tchulani zotsatirapo zabwino zomwe zinalipo chifukwa choyesetsa kuthandiza anthu osalalikira.
Mph. 25: “Tidzakhala ndi Ntchito Yapadera Kuyambira pa October 16 Mpaka pa November 12!” Nkhaniyi ikambidwe ndi mkulu mwaumoyo kwambiri. Mukawerenga chilengezo chomwe chili m’kalata yopita kwa mabungwe a akulu ya pa June 6, 2006, patsani munthu aliyense amene alipo kapepala kamodzi ka Uthenga wa Ufumu Na. 37. Kenaka pitirizani kukambirana nkhaniyi mwa mafunso ndi mayankho. Fotokozani zomwe zakonzedwa mu mpingo wanu kuti muthe kulalikira gawo lanu lonse. Limbikitsani ofalitsa onse kuti achite nawo mokwanira ntchito yapaderayi. Khalani ndi chitsanzo chachidule.
Nyimbo Na. 50 ndi pemphero lomaliza.
Mlungu Woyambira September 25
Mph. 15: Zilengezo za pampingo. Werengani lipoti la maakaunti ndi mawu oyamikira zopereka olembedwa pa sitetimenti. Kumbutsani ofalitsa kupereka malipoti awo a utumiki wa kumunda a mwezi wa September. Pogwiritsa ntchito mfundo zimene zili pa tsamba 4 kapena ulaliki wina uliwonse umene ungakhale wothandiza m’gawo lanu, chitani chitsanzo chosonyeza momwe tingagawire Nsanja ya Olonda ya October 1 ndi Galamukani! ya October mu ulaliki wa mumsewu. (Ngati mpingo wanu sunalandire magazini tatchulawa gwiritsirani ntchito zitsanzo zimene zinatchulidwa mu Utumiki Wathu wa Ufumu wa mwezi watha.)
Mph. 20: “Pitirizani Kulimbikitsana”a Werengani ndi kuthirira ndemanga malemba onse otchulidwa. Funsani omvera kuti anenepo momwe athandizidwira ndi kukoma mtima kwa ena.
Mph. 10: Zokumana nazo. Pemphani omvera kuti afotokoze zomwe akumana nazo pogawira magazini yapadera ya Galamukani! kapena poyambitsa maphunziro a Baibulo pa ulendo woyamba m’buku la Baibulo Limaphunzitsa Chiyani. Mungachite chitsanzo chimodzi kapena ziwiri zosonyeza zokumana nazo zabwino kwambiri.
Nyimbo Na. 183 ndi pemphero lomaliza.
Mlungu Woyambira October 2
Mph. 10: Zilengezo za pampingo. Kambiranani mwachidule Bokosi la Mafunso.
Mph. 15: Zosowa za pampingo.
Mph 20: “Kulalikira ku Nyumba ndi Nyumba.”b Ngati muli ndi nthawi, pemphani omvera kuti aperekepo ndemanga pa malemba amene atchulidwa.
Nyimbo Na. 127 ndi pemphero lomaliza.
[Mawu a M’munsi]
a Kambani mawu oyamba osakwana mphindi imodzi, ndiyeno kambiranani mwa mafunso ndi mayankho.
b Kambani mawu oyamba osakwana mphindi imodzi, ndiyeno kambiranani mwa mafunso ndi mayankho.