Kodi Mizimu Yoipa Ingakuvulazeni?
1 Timabuku takuti Mizimu ya Akufa—Kodi Ingakuthandizeni Kapena Kukuvulazani? Kodi Iyo Ilikodi? ndi Njira ya ku Moyo Wosatha—Kodi Mwaipeza? tinalembedwera anthu a ku Africa kuno. Kuphunzira timabuku timeneti pa Phunziro la Buku la Mpingo kuyambira mlungu woyambira January 8, 2007, kudzatithandiza kumvetsa mmene Yehova amaonera nkhani yokhulupirira mizimu.
2 Anthu okhulupirira mizimu amaganiza kuti munthu akafa, mzimu wake umakhalapobe ndipo umatha kulankhula ndi anthu amoyo, nthawi zambiri kudzera kwa amkhalapakati. Ena a amkhalapakati amenewa amachiritsa anthu ndipo amatchedwa kuti asing’anga. Anthu ambiri amakhulupirira kuti matenda amabwera osati chifukwa cha tizilombo toyambitsa matenda koma chifukwa chokwiyitsa mizimu ya anthu amene anafa. Kuti achire, anthu ambiri amakatenga mankhwala azitsamba kapena zithumwa kwa asing’anga. Ambiri mwa asing’anga amenewa amakhala amizimu.—Deut. 18:10-12.
3 Kodi kukapempha mankhwala kapena chitetezo kwa anthu okhulupirira mizimu n’kulakwa? Kukhulupirira mizimu kumaikidwa m’gulu limodzi ndi ntchito zathupi. (Agal. 5:19-21) Kupempha chithandizo kwa anthu okhulupirira mizimu kumasonyeza kuti munthu akukhulupirira bodza la Satana lakuti anthu samafa. Kuli ngati kupempha malangizo kuchokera kwa anthu amene amagwiritsa ntchito mphamvu za Satana ndi ziwanda zake.
4 Kodi n’zotheka kuti Mkhristu alodzedwe ndi anthu amene amagwiritsa ntchito mphamvu za mizimu kapena asing’anga? Kabuku ka Mizimu ya Akufa, patsamba 24, kamati anthu ankhaninkhani amaopa matemberero, malaulo, njirisi ndi zithumwa. Koma atumiki a Mulungu sakhala akapolo a chilichonse cha zinthu zimenezi. Yehova ndi wamphamvu kwambiri kuposa Satana. Ngati mumatumikira Yehova, adzakutetezani ku ziwanda. (Yak. 4:7) Palibe angakulodzeni.
5 Munthu aliyense amene walodzedwa ndiye kuti alibe chitetezo cha Mulungu. Munthu ameneyo ndiye kuti sanasiyiretu chilichonse chokhudzana ndi kukhulupirira mizimu kapena kulambira ziwanda. Atha kunena kuti ndi Mkhristu weniweni, koma zoona zake n’zakuti sanadzipereke kotheratu ku ulamuliro wa Yehova mwa kumvera malamulo Ake. Kodi n’chiyani chimene munthu ameneyo afunikira kuchita kuti Yehova azimuteteza? Ayenera kufufuza panyumba pake ndi katundu wake yense ndiponso aone ngati ana ake avala njirisi pamikono pawo kapena pena paliponse m’thupi mwawo. Kodi pali chilichonse chimene anachikumbira m’nyumba mwake kapena pakhomo pake chimene anapatsidwa ndi wachibale kapena mnzake amene amakhulupirira mizimu? Kapena kodi ali ndi kanthu kena komwe anapatsidwa ndi munthu wokhulupirira mizimu?
6 Yehova sangateteze munthu amene amapita kwa asing’anga amene amadziwika kuti ndi amizimu n’cholinga chokatenga mankhwala oti amuteteze. Ngati mumakondadi Mulungu, kanani miyambo iliyonse yokhudzana ndi mizimu ndipo musamvere ngakhale pang’ono malangizo alionse amene amati ndi “oteteza” ochokera kwa mizimu.
7 Tikavala zida zauzimu ndi kukana chilichonse chokhudzana ndi ziwanda, sitidzakhala ndi mantha alionse ndipo tidzakhala ndi moyo wosangalala. Choncho, pamene tikuphunzira timabukuti, tiyeni tizikonzekereratu n’kukhala ndi nthawi yosinkhasinkha za mmene tingapewere chilichonse chimene chingachititse kuti Yehova aleke kutiteteza.