Watchtower LAIBULALE YA PA INTANETI
Watchtower
LAIBULALE YA PA INTANETI
Chichewa
  • BAIBULO
  • MABUKU
  • MISONKHANO
  • km 11/06 tsamba 2
  • Ndandanda ya Misonkhano ya Utumiki

Palibe Vidiyo.

Pepani vidiyoyi ikukanika kutsegula.

  • Ndandanda ya Misonkhano ya Utumiki
  • Utumiki Wathu wa Ufumu—2006
  • Timitu
  • Mlungu Woyambira November 13
  • Mlungu Woyambira November 20
  • Mlungu Woyambira November 27
  • Mlungu Woyambira December 4
Utumiki Wathu wa Ufumu—2006
km 11/06 tsamba 2

Ndandanda ya Misonkhano ya Utumiki

Mlungu Woyambira November 13

Nyimbo Na. 152

Mph.10: Zilengezo za pampingo. Pogwiritsa ntchito mfundo zimene zili patsamba 8 kapena ulaliki wina uliwonse umene ungakhale wothandiza m’gawo lanu, chitani zitsanzo zosonyeza momwe tingagawire Nsanja ya Olonda ya November 15 ndi Galamukani! ya November. M’chitsanzo chimodzi, sonyezani zimene tingachite munthu atafuna kuimitsa kukambirana ponena kuti, “Ndili Wozolowerana Kale ndi Ntchito Yanu.”—Onani m’buku la Kukambitsirana, tsamba 20. (Ngati mpingo wanu sunalandire magazini tatchulawa gwiritsirani ntchito zitsanzo za mu Utumiki Wathu wa Ufumu wa mwezi watha.)

Mph.20: Atumiki a Uthenga Wabwino. Nkhani ndi kukambirana ndi omvera kuchokera m’buku la Gulu Lochita Chifuniro cha Yehova, tsamba 77 mpaka pakamutu ka patsamba 83.

Mph.15: “Olimba Mtima, Koma Amtendere.”a Perekani ndemanga kuchokera m’buku la Sukulu ya Utumiki, tsamba 252 ndi 253, pansi pa kamutu kakuti “Pamene Muyenera Kulolera.”

Nyimbo Na. 39 ndi pemphero lomaliza.

Mlungu Woyambira November 20

Nyimbo Na. 132

Mph.10: Zilengezo za pampingo. Zilengezo zina musankhe mu Utumiki Wathu wa Ufumu uno.

Mph.15: Zosowa za pampingo.

Mph.20: Kugawira buku la Munthu Wamkulu mwezi wa December. Kukambirana ndi omvera. Pemphani omvera kuti afotokoze chifukwa chake amakonda buku la Munthu Wamkulu ndipo afotokozenso zokumana nazo zosangalatsa zimene apeza pogawira bukuli m’mbuyomu. Onaninso zitsanzo za ulaliki mu mphatika ya mu Utumiki Wathu wa Ufumu wa January 2005. Chitani chitsanzo chosonyeza mmene mungagawire bukuli pogwiritsa ntchito ulaliki umodzi wa mu mphatikayi kapena ulaliki wina uliwonse umene ungakhale wogwira mtima kwanuko.

Nyimbo Na. 203 ndi pemphero lomaliza.

Mlungu Woyambira November 27

Nyimbo Na. 111

Mph.5: Zilengezo za pampingo. Werengani lipoti la maakaunti ndi mawu oyamikira zopereka olembedwa pa sitetimenti.

Mph.10: Kumanga Mogwirizana N’cholinga Chotamanda Mulungu. Nkhani ndi kukambirana ndi omvera yotengedwa mu Nsanja ya Olonda ya November 1, 2006, masamba 17 mpaka 21.

Mph.15: “Mmene Mungakonzekerere Kugawira Magazini.”b Phatikizanipo chitsanzo cha mphindi zitatu chokhala ndi ofalitsa awiri, mwina mwamuna ndi mkazi wake, akusankha ulaliki woti agwiritse ntchito womwe uli patsamba 8 wogawira magazini a December. Asonyeze mmene angaufotokozere m’mawu awoawo. Ndiyeno, pogwiritsa ntchito mfundo za m’nkhani imene angokambirana kumeneyo, akonzekere ndi kuchita chitsanzo cha mmene angakafotokozere m’gawo lawo nkhani inanso ya m’magazini yomweyo imene ingakhale ya panthawi yake.

Mph.15: “Kodi Ndimaiona Bwanji Nkhani Yokhudza Tizigawo ta Magazi ndi Njira Zachipatala Zogwiritsa Ntchito Magazi Anga Omwe?” Nkhani yokambirana mwa mafunso ndi mayankho yokhalanso ndi chitsanzo.

Nyimbo Na. 120 ndi pemphero lomaliza.

Mlungu Woyambira December 4

Nyimbo Na. 155

Mph.5: Zilengezo za pampingo. Kumbutsani ofalitsa kuti apereke malipoti a utumiki wa kumunda a mwezi wa November.

Mph.20: “Kodi Mizimu Yoipa Ingakuvulazeni?”c Limbikitsani mpingo kuti ugwiritsire ntchito bwino timabukuti. Pamapeto pa phunziro lililonse, muyenera kubwereza phunzirolo pogwiritsira ntchito Baibulo.

Mph.20: Gwiritsani Ntchito Baibulo Poyankha Mafunso. Nkhani yokambirana ndi omvera yotengedwa mu Nsanja ya Olonda ya August 15, 2002, tsamba 17 ndi 18 pansi pa kamutu kakuti, “Kukonda Choonadi Chimene Timaphunzitsa.” Pemphani omvera kuyankha funso lililonse. Chitani chitsanzo chosonyeza wofalitsa akugwiritsa ntchito buku la Kukambitsirana poyankha funso la munthu wogwira naye ntchito, amene akufunsa kuti, “N’chifukwa chiyani simukondwerera Khirisimasi?”

Nyimbo Na. 168 ndi pemphero lomaliza.

[Mawu a M’munsi]

a Kambani mawu oyamba osakwana mphindi imodzi, ndiyeno kambiranani mwa mafunso ndi mayankho.

b Kambani mawu oyamba osakwana mphindi imodzi, ndiyeno kambiranani mwa mafunso ndi mayankho.

c Kambani mawu oyamba osakwana mphindi imodzi, ndiyeno kambiranani mwa mafunso ndi mayankho.

    Mabuku a Chichewa (1974-2025)
    Tulukani
    Lowani
    • Chichewa
    • Tumizirani Ena
    • Zimene Mumakonda
    • Copyright © 2025 Watch Tower Bible and Tract Society of Pennsylvania
    • Zoyenera Kutsatira
    • Nkhani Yosunga Chinsinsi
    • Privacy Settings
    • JW.ORG
    • Lowani
    Tumizirani Ena