Watchtower LAIBULALE YA PA INTANETI
Watchtower
LAIBULALE YA PA INTANETI
Chichewa
  • BAIBULO
  • MABUKU
  • MISONKHANO
  • km 2/07 tsamba 7
  • Kubwereza za M’sukulu ya Utumiki wa Mulungu

Palibe Vidiyo.

Pepani vidiyoyi ikukanika kutsegula.

  • Kubwereza za M’sukulu ya Utumiki wa Mulungu
  • Utumiki Wathu wa Ufumu—2007
Utumiki Wathu wa Ufumu—2007
km 2/07 tsamba 7

Kubwereza za M’sukulu ya Utumiki wa Mulungu

Mafunso otsatirawa mudzakambirana pa Sukulu ya Utumiki wa Mulungu ya mlungu woyambira February 26, 2007. Woyang’anira sukulu adzatsogolera kubwereza nkhani zomwe zakambidwa m’kati mwa milungu ya January 1 mpaka February 26, 2007. Kubwerezaku kudzakhala kwa mphindi 30. [Dziwani izi: Pa funso lomwe kumapeto kwake silikusonyeza buku lililonse lomwe mwatengedwa nkhaniyo, ndiye kuti muyenera mufufuze nokha kuti mupeze mayankho ake.—Onani buku la Sukulu ya Utumiki, mas. 36-7.]

LUSO LA KULANKHULA

1. Pokamba nkhani, kodi ndi nthawi iti imene tiyenera kusonyeza mmene mfundo za m’nkhaniyo zimagwirira ntchito, ndipo tiyenera kuchita zimenezi motani? [Jan. 1 be-CN tsa. 158 ndime 1-3]

2. N’chifukwa chiyani kuli kofunika kuthandiza ena kuona mmene nkhani yathu ikuwakhudzira, ndipo tingachite motani zimenezi? [be-CN tsa. 159 ndime 3-4]

3. N’chifukwa chiyani kusankha bwino mawu kuli kofunika? [be-CN tsa. 160]

4. Kodi chingatithandize n’chiyani kuti tizigwiritsa ntchito mawu osiyanasiyana molondola? [be-CN tsa. 161 ndime 5-6; tsa. 162 ndime 1, 4]

5. Kodi kulankhula mochokera pa autilaini, kaya ya m’maganizo kapena yolemba, kuli ndi phindu lotani? [be-CN tsa. 166 ndime 1-3]

NKHANI NA. 1

6. Kodi tingakonzekere motani nkhani yowerenga? [be-CN tsa. 43 ndime 4]

7. Kodi chofunika n’chiyani kuti tizikonda chabwino ndi kudana n’choipa? (Aheb. 5:14) [w05-CN 1/1 tsa. 9 ndime 11]

8. Kodi tiyenera kukumbukira chiyani ngati titawerenga nkhani inayake m’Baibulo, imene ikutichititsa kukayikira ngati Mulungu anachita zinthu moyenerera kapena mwachilungamo? [w05-CN 2/1 tsa. 24 ndime 7]

9. Kodi tidzachita chiyani ngati malamulo a anthu akutsutsana ndi malamulo a Mulungu? [w05-CN 4/15 tsa. 12 ndime 9] Ngati timakonda Mawu a Mulungu, tidzakhalabe okhulupirika kwa Yehova. (Sal. 119:​18, 20, 24) Mofanana ndi atumwi a Yesu Khristu amene anali kuzunzidwa, tidzanena kuti: “Tiyenera kumvera Mulungu monga wolamulira, osati anthu.” (Mac. 5:⁠29)

10. N’chifukwa chiyani makolo ayenera kuona kuti ana awo ndi amtengo wapatali? [w05-CN 4/1 tsa. 8 ndime 5, 6]

KUWERENGA BAIBULO KWA MLUNGU NDI MLUNGU

11. Kodi “chophimba” ndi “nsalu yokuta” zotchulidwa pa Yesaya 25:7 n’chiyani?

12. Kodi anthu ‘angamuone’ ndi ‘kumumva’ Yehova motani? (Yes. 30:20, 21)

13. Zoona kapena Zonama: Pemphero la Hezekiya lolembedwa pa Yesaya 38:3, analipereka chifukwa choti ankafunitsitsa kukhala ndi moyo wautali.

14. Kodi Aisiraeli akanatumikira motani monga mboni za Yehova, ndipo ifeyo tingawatsanzire motani? (Yes. 43:10)

15. Mogwirizana ndi mawu aulosi amene ali pa lemba la Yesaya 52:11, 12, kodi chofunika n’chiyani kuti munthu ‘anyamule zotengera za Yehova’?

    Mabuku a Chichewa (1974-2025)
    Tulukani
    Lowani
    • Chichewa
    • Tumizirani Ena
    • Zimene Mumakonda
    • Copyright © 2025 Watch Tower Bible and Tract Society of Pennsylvania
    • Zoyenera Kutsatira
    • Nkhani Yosunga Chinsinsi
    • Privacy Settings
    • JW.ORG
    • Lowani
    Tumizirani Ena