Zilengezo
◼ Mabuku ogawira mu February: Gawirani buku la Yandikirani kwa Yehova. Ngati mulibe buku limeneli, mungagawire mabuku ena akale omwe mpingo wanu uli nawo ambiri. March: Gawirani buku la Baibulo Limaphunzitsa Chiyani ndipo yesetsani kuyambitsa maphunziro a Baibulo. April ndi May: Tidzagawira magazini a Nsanja ya Olonda ndi Galamukani! Mukamachita maulendo obwereza kwa anthu achidwi, ngakhalenso amene anafika pa Chikumbutso kapenanso pa misonkhano ina koma safika pa misonkhano ya mpingo nthawi zonse, yesetsani kuwagawira buku la Baibulo Limaphunzitsa Chiyani, ndi cholinga choyambitsa phunziro la Baibulo.
◼ Mlembi ndi woyang’anira utumiki ayenera kuonanso ntchito ya apainiya okhazikika. Ngati ena zikuwavuta kukwanitsa maola awo, akulu ayenera kukonza zokumana nawo kuti awathandize. Kuti mupeze mfundo zina, werenganinso kalata ya pachaka ya S-201.
◼ Nkhani ya onse yapadera ya nyengo ya Chikumbutso ya 2007 ili ndi mutu wakuti “Mukhoza Kukhala Otetezeka M’dziko la Mavutoli.” Onani zilengezo zofanana ndi zimenezi mu Utumiki Wathu wa Ufumu wa October 2006.
◼ Alembi a Mipingo Adziwe Izi: Mukalandira mabuku kapena magazini a zinenero zimene simunaitanitse, muwabweze ku ofesi ya nthambi mukaona kuti simungathe kuwagwiritsira ntchito bwinobwino m’gawo la mpingo wanu. Zikatero, lembani kalata ku nthambi mwamsanga, n’kutchula mabuku amene munaitanitsawo, omwe sanatumizidwe m’chinenero chimene mumafuna. Mwachitsanzo, lembani kalata mwamsanga ngati mwalandira magazini a Nsanja ya Olonda angapo m’chinenero chimene simunaitanitse, ndipo mukuona kuti zimenezi zingathe kuchititsa kuti anthu a mumpingo wanu aperewedwe magazini a chinenero chanu pa phunziro la Nsanja ya Olonda. Komanso ngati zinthu zina zimene munaitanitsa sizinabwere, komano zasonyezedwa kuti zili pa mpambo wa mabuku amene mwalandira, lembani kalata ku ofesi ya nthambi n’kutchula zinthu zimene sizinatumizidwezo, osaiwalanso kutchula chinenero chake.
◼ Kuyambira magazini a July 2007, tisiya kutulutsa Nsanja ya Olonda ndi Galamukani! pakaseti m’Chingelezi. Maoda onse amene anatumizidwa kale adzatha mwezi umenewu. Onani tsamba la cha kumayambiriro kwa magaziniwa kuti muone mitundu yosiyanasiyana ya ma CD a magaziniwa amene munthu angaitanitse kudzera ku mpingo. Tikufuna tikukumbutseninso kuti m’tsogolomuno zikuoneka kuti tidzasiya kutulutsa zinthu zambiri pa makaseti a wailesi ndi makaseti a vidiyo, ndipo m’malo mwake zizidzakhala pa CD-ROM ndi pa DVD.
◼ Ma DVD atsopano amene alipo:
Tsopano vidiyo ya Young People Ask—What Will I Do With My Life? ili m’zinenero ziwiri: Chingelezi ndi Chifalansa, pa DVD imodzi (dvyf-DVA)