Ndandanda ya Misonkhano ya Utumiki
Mlungu Woyambira February 12
Mph.10: Zilengezo za pampingo. Gwiritsani ntchito mfundo zimene zili pa tsamba 8, kapena ulaliki wina uliwonse umene ungakhale wothandiza m’gawo lanu, kusonyeza chitsanzo cha mmene tingachitire pogawira Nsanja ya Olonda ya February 15 ndi Galamukani! ya February. M’chitsanzo chimodzi, sonyezani mmene mungachitire ndi munthu yemwe sakufuna kukambirana naye, amene akunena kuti “sindili okondwera ndi chipembedzo.”—Onani buku la Kukambitsirana, masamba 16 mpaka 17. (Ngati mpingo wanu sunalandire magazini tatchulawa gwiritsirani ntchito zitsanzo za mu Utumiki Wathu wa Ufumu wa mwezi watha.)
Mph 35: “Lengezani Ulemerero wa Yehova.”a Nkhani yokambidwa ndi woyang’anira utumiki. Pamene pali mfundo zoyenerera, lengezani nthawi ndi malo omwe kukachitikire Chikumbutso, lengezani za misonkhano yomwe mwawonjezera yokonzekera utumiki wa kumunda, ndiponso lengezani cholinga cha mpingo choti ukhale ndi apainiya okwana mwakutimwakuti m’mwezi wa April. Mukamaliza kukambirana ndime yachitatu, chitani chitsanzo chachidule chosonyeza wofalitsa akuitanira munthu ku Chikumbutso paulendo wobwereza.
Nyimbo Na. 147 ndi pemphero lomaliza.
Mlungu Woyambira February 19
Mph.10: Zilengezo za pampingo. Kambiranani “Pulogalamu Yatsopano ya Msonkhano Wadera” ndipo lengezani tsiku la msonkhanowo ngati mukulidziwa.
Mph.20: “Tsanzirani Mphunzitsi Waluso Pogwiritsa Ntchito Buku la Baibulo Limaphunzitsa Chiyani.”b Pokambirana ndime 6, chitani chitsanzo chachidule chosonyeza wofalitsa akubwereza zimene waphunzira ndi wophunzira wake pogwiritsa ntchito bokosi lomwe lili kumapeto kwa mutu 6 wa buku la Baibulo Limaphunzitsa chiyani.
Mph.15: Kodi Mungayambitse Phunziro la Baibulo M’mwezi wa March? Kukambirana ndi omvetsera. Kuyambira pa March 1 mpaka kufika pa 15, tizidzagawira buku la Baibulo Limaphunzitsa Chiyani n’cholinga choyambitsa maphunziro a Baibulo. Onaninso mfundo zomwe zili mu mphatika ya Utumiki Wathu wa Ufumu wa January 2006, masamba 3 mpaka 6. Pogwiritsa ntchito imodzi mwa mfundo zomwe zili pa tsamba 6 kapena chitsanzo china chilichonse chomwe chingakhale chothandiza m’gawo lanu, sonyezani mmene mungayambitsire phunziro la Baibulo paulendo woyamba. Pemphani omvetsera kuti anene nkhani zolimbikitsa zofotokoza zimene anakumana nazo pamene anali kugwiritsa ntchito bukuli, makamaka poyambitsa maphunziro a Baibulo.
Nyimbo Na. 220 ndi pemphero lomaliza.
Mlungu Woyambira February 26
Mph.10: Zilengezo za pampingo. Werengani lipoti la maakaunti ndi ndalama zimene zalembedwa pa sitetimenti. Gwiritsani ntchito mfundo zimene zili pa tsamba 8, kapena ulaliki wina uliwonse umene ungakhale wothandiza m’gawo lanu, kusonyeza chitsanzo cha mmene tingachitire pogawira Nsanja ya Olonda ya March 1 ndi Galamukani! ya March. M’chitsanzo chimodzi, sonyezani wofalitsa akulalikira m’gawo la malonda. (Ngati mpingo wanu sunalandire magazini tatchulawa gwiritsirani ntchito zitsanzo za mu Utumiki Wathu wa Ufumu wa mwezi watha.)
Mph.15: “Musaiwale Ofooka.”c Fotokozaninso zitsanzo zomwe zili mu Nsanja ya Olonda ya May 1, 2004, masamba 21 mpaka 22, ndime 13 mpaka 16.
Mph.20: “Tsanzirani Khristu Pochita Utumiki.”d Ngati nthawi ilipo, pemphani omvetsera kuti awerenge ndi kupereka ndemanga pa malemba osonyezedwa m’nkhaniyi.
Nyimbo Na. 18 ndi pemphero lomaliza.
Mlungu Woyambira March 5
Mph.15: Zilengezo za pampingo. Musankhe zilengezo zina mu Utumiki Wathu wa Ufumu. Perekani kwa omvetsera aliyense kapepala kapadera kamodzi koitanira anthu ku Chikumbutso, ndipo kambiranani zimene mwakonza kwanuko zogawira timapepalati m’gawo lanu. Limbikitsani aliyense kudzachita nawo ntchitoyi mokwanira. Khalani ndi chitsanzo chosonyeza mmene mungagwiritsire ntchito timapepalati.
Mph.15: Kulalikira Uthenga Wabwino M’njira Yolongosoka. Nkhani ndi kukambirana ndi omvetsera yochokera m’buku la Gulu Lochita Chifuniro cha Yehova, kuchokera pa mutu waung’ono womwe uli pa tsamba 102 mpaka kumapeto kwa chaputala chonsecho.
Mph.15: “Tapatsidwa Chuma Choti Tisamalire.”e Ngati muli ndi nthawi yokwanira, pemphani omvetsera kuti apereke ndemanga pa malemba amene ali m’nkhaniyi.
Nyimbo Na. 104 ndi pemphero lomaliza.
[Mawu a M’munsi]
a Mawu oyamba asapitirire mphindi imodzi, ndiyeno kambiranani mwa mafunso ndi mayankho.
b Mawu oyamba asapitirire mphindi imodzi, ndiyeno kambiranani mwa mafunso ndi mayankho.
c Mawu oyamba asapitirire mphindi imodzi, ndiyeno kambiranani mwa mafunso ndi mayankho.
d Mawu oyamba asapitirire mphindi imodzi, ndiyeno kambiranani mwa mafunso ndi mayankho.
e Mawu oyamba asapitirire mphindi imodzi, ndiyeno kambiranani mwa mafunso ndi mayankho.