Kalata Yochokera ku Bungwe Lolamulira
POTSATIRA chitsanzo cha Yesu, timapemphera zolimba kwa Mulungu kuti: “Dzina lanu liyeretsedwe.” Umboni wakuti tikufunitsitsa kukhala mogwirizana ndi pemphero limeneli umaonekera mwa khalidwe lathu pokhala Mboni za Yehova. N’zoona kuti kungodziwa dzina la Mulungu kokha sikokwanira ayi. Tikufunika kugwiritsa ntchito mpata uliwonse womwe wapezeka kulemekeza dzina limenelo. Kunena zoona, kudziwika ndi dzina loti wa Mboni za Yehova ndi ulemu waukulu kuposa wina uliwonse womwe tingalandire.—Mat. 6:9; Yes. 43:10.
Mogwirizana ndi lemba la Salmo 110:3, anthu a Yehova akugwira ndi mtima wonse ntchito imene Yehova walamula kuti ichitike. Kodi n’chifukwa chiyani anthu amisinkhu yonse ndiponso amitundu yonse akudzipereka okha pantchito yolalikira? Kwenikweni n’chifukwa chokonda Mulungu komanso chifukwa choti ndi odzipereka kwa iye. Lemba la Deuteronomo 6:5, 6 limatilamula kuti tizikonda Yehova ndi ‘mtima wathu wonse, moyo wathu wonse, ndi mphamvu zathu zonse.’ Chikondi chochokera pansi pa mtima chimenechi chimatilimbikitsa kugwiritsa ntchito nthawi yathu, mphamvu zathu, ndiponso chuma chathu kupititsa patsogolo zinthu za Ufumu wa Mulungu. Izi zikuphatikizapo kuyesetsa kuchita zimene tingathe mu utumiki.
Chifukwa chokonda anthu, Yehova walamula kuti uthenga wabwino wa Ufumu wake ulalikidwe padziko lonse lapansi. Sakufuna kuti wina aliyense adzawonongedwe koma kuti anthu onse alape, n’kusiya zochita zawo zoipa ndi kuyamba kuchita zimene Mlengi wawo amafuna. Akatero angayembekezere kudzakhala ndi moyo. (2 Pet. 3:9) Yehova anati: “Sindikondwera nayo imfa ya woipa, koma kuti woipa aleke njira yake, nakhale ndi moyo.” (Ezek. 33:11) Tikakhala mu utumiki wa kumunda, timapereka umboni wooneka ndi maso woti Yehova amakonda anthu anzathu. Mosakayikira, ichi ndi chimodzi mwa zifukwa zimene timakhalira osangalala tikamagwira ntchito yofunikayi.
Timasonyezanso kuti timam’konda kwambiri Yehova malinga ndi mmene timaonera Mawu ake ouziridwa, omwe ndi Malemba Oyera. Pakadapanda Baibulo, sitikanadziwa Mulungu ndi kukhala naye paubwenzi, monga momwe lemba la Yakobe 4:8 limatilangizira. Ndiponso sitikanadziwa chifukwa chake tili ndi moyo komanso zimene zidzachitikire anthu m’tsogolo. Sitikanathanso kudziwa kuti Adamu, yemwe ndi kholo la anthu onse, ndiye anayambitsa mavuto omwe timakumana nawowa. (Aroma 5:12) Komanso sitikanadziwa za chikondi chachikulu cha Mulungu chomwe anasonyeza popereka Mwana wake wobadwa yekha kuti akhale dipo lotiwombola. Yehova akutithandiza kuti nafenso pang’ono chabe tikhale ozindikira ndi omvetsa zinthu ndiponso anzeru monga mmene iye alili. Ndipo akuchita zimenezi m’njira zinanso zambiri. Timayamikira kwambiri mphatso imene anatipatsa, yomwe ndi Mawu ake ouziridwa ndi mzimu. Popeza timayamikira mphatso yamtengo wapataliyi, timalimbikitsidwa ‘kuwombola nthawi’ kuti tiwerenge, tiphunzire, ndi kusinkhasinkha zonena zake. (Aef. 5:15, 16; Sal. 1:1-3) Tisamanyinyirike m’pang’ono pomwe ndi nthawi yomwe timafunika kuti tiwerenge Mawu a Mulungu tsiku ndi tsiku. M’malo mwake, kukonda Mulungu kuyenera kutithandiza kukonda Mawu ake. Zimenezi zingatithandize kuti tim’dziwe bwino ndiponso kuti tikulitse chikondi chathucho.
Taphunzira kuchokera m’Baibulo kuti Adamu atachimwira Yehova, anachititsa kuti ana ake omwe anadzabadwa m’tsogolo, kuphatikizapo tonsefe, akhale m’mavuto aakulu ndiponso opanda chiyembekezo. Komabe, Mulungu akanatha kupeza njira yopulumutsira anthu, ndipo anaterodi. Anachita zinthu zothandiza kuti cholinga chake cha dziko lapansili chisalephereke.—Gen. 3:15.
N’zosachita kufunsa kuti aliyense wa ife akufunitsitsa kuyeretsa dzina lolemekezeka la Mulungu wathu. Tikamadziwa zambiri zokhudza Yehova yemwe ndi Mulungu wabwino kwambiri, timalimbikitsidwa kugwirizana naye ndiponso kugwirizana ndi gulu lake pantchito yodziwitsa anthu za dzina lake lolemekezeka komanso cholinga chake chachikulu. Timakhala ndi chikhulupiriro chakuti panopa amatikonda ndi kutidalitsa komanso tidzakhala kwamuyaya m’dziko lapansi latsopano.
Abale amene tili m’Bungwe Lolamulira tikufuna kukutsimikizirani kuti timakukondani kwambiri abale ndi alongo. Tikufunanso kukuyamikirani kwambiri chifukwa chakuti mukuyesetsa kugwiritsa ntchito nthawi yatsalayi kuti mufikire munthu aliyense ndi uthenga wabwino, “chisautso chachikulu” chisanayambe. (Chiv. 7:14) Pochita zimenezi, mumapatsa anthuwo mwayi womwe inunso munapatsidwa, wodziwa Mulungu ndi Khristu, zomwe zimathandiza anthu kupeza moyo wosatha.—Yoh. 17:3.
Ndife abale anu,
Bungwe Lolamulira la Mboni za Yehova