Zimene Mungachite Kuti Utumiki Wanu Waupainiya Uyende Bwino
1, 2. Kodi n’chiyani chimafunika kuti utumiki waupainiya umuyendere bwino munthu?
1 Kodi ntchito yanu ndi yaupainiya? Ngati ndinu mpainiya, kapena kuti wolengeza Ufumu wa nthawi zonse, mosakayikira mukufuna kuti zinthu zikuyendereni bwino. Koma kuti zinthu ziyende bwino, munthu amafunika kuchita zambiri, osati kungothera nthawi pa ntchito yakeyo. Munthu amene akufuna kuti zinthu zimuyendere bwino afunika kuvomera kuphunzitsidwa ndi kuyesetsa kukulitsa luso lake.
2 Choncho, kodi mungatani kuti mupitirize kuchita upainiya komanso mupite patsogolo pa ntchito yanuyi? Pali mafunso angapo ofunika kwambiri amene muyenera kuwaganizira.
3, 4. Kodi tingaphunzire chiyani kwa Mfumu Davide?
3 Kodi Ubwenzi Wanga ndi Mulungu Ndi Wolimba?: Chinthu chimodzi chofunika kwambiri kuti upainiya ukuyendereni bwino ndicho kukhala ndi ubwenzi wabwino komanso wolimba ndi Yehova Mulungu. Pankhani imeneyi, tingaphunzire kwa wamasalmo Davide. Iye anachonderera Mulungu kuti: “Mundidziwitse njira zanu, Yehova; mundiphunzitse mayendedwe anu. Munditsogolere m’choonadi chanu, ndipo mundiphunzitse; pakuti Inu ndinu Mulungu wa chipulumutso changa; Inu ndikuyembekezerani tsiku lonseli.”—Sal. 25:4, 5.
4 Davide anadalira kotheratu ‘Mulungu wa chipulumutso chake.’ Anafuna kuti Yehova am’phunzitse ndi ‘kumudziwitsa njira Zake.’ Kodi simukuona kuti Davide ankalakalaka kwambiri kusangalatsa Mulungu? Kumeneku sikunali kulakalaka kwa kanthawi kochepa, chifukwa Davide anati: “Inu ndikuyembekezerani tsiku lonseli.”
5. Kodi n’chiyani chimene chili chofunika kwambiri kuti tikhalebe paubwenzi wabwino ndi Mulungu?
5 Koma kodi mungatani kuti mukhalebe paubwenzi wabwino choncho ndi Yehova? Onani kuti mawu amene ali m’ndime yapitayi ndi amene Davide ananena m’pemphero. Zoonadi, kulankhula ndi Mulungu m’pemphero ndiko maziko okhalira paubwenzi wabwino ndi iye. Ndipo timasangalala podziwa kuti sitifunikira kuyamba tapempha kaye kuti tilankhulane ndi Atate wathu wakumwamba. Tikhoza kulankhula naye nthawi iliyonse. Tingachite ngati Davide, amene ananena kuti: “Tsiku lonse ndiitana Inu.” (Sal. 86:3) Ngakhale Mwana wa Mulungu amene, yemwe anakhala padziko lapansi monga munthu wangwiro, anadziwa kuti zinthu sizingamuyendere bwino popanda kuthandizidwa ndi Atate wake. Yesu ankalankhula ndi atate wake m’pemphero nthawi iliyonse, kaya m’mamawa, masana, ngakhalenso usiku.—Maliko 1:35; Luka 11:1; 6:12.
6, 7. Kodi mpainiya wina wodziwa bwino ntchito yake anati chiyani, ndipo kodi mukugwirizana ndi maganizo amenewo?
6 Ife Akhristu, tiyenera kutsatira chitsanzo cha Yesu kuti zinthu zitiyendere bwino pa utumiki wathu. (Aheb. 5:7) Ponena za pemphero, mayi wina wachikhristu amene upainiya wake wamuyendera bwino kwa zaka 30 anati: “Ndimaona kuti pemphero limandithandiza kwambiri kuti upainiya wanga uyende bwino. Landithandiza kudalira Yehova kotheratu, pozindikira kuti sindingakwanitse ntchitoyi pandekha. Nthawi zonse ndimapempha Yehova kuti andithandize kupitiriza kuchita upainiya.”
7 Zoonadi, kuti utumiki wanu waupainiya uyende bwino, mufunika kukhala paubwenzi wolimba ndi Yehova, ndipo muzimudalira kotheratu polankhula naye m’pemphero. Komabe, funso lotsatirali n’lofunikanso kuti muzidzifunsa.
8. N’chifukwa chiyani tinganene kuti kuchita upainiya kumasonyeza chikondi?
8 Kodi Anthu Ndimawakonda Kwambiri?: Kuchita upainiya kumasonyeza chikondi. Chifukwa chiyani? Chifukwa choti utumiki wa nthawi zonse umafuna mtima wodzimana. Pa upainiya wanu, nthawi zonse mumakhala mukugwiritsa ntchito nthawi yanu ndi mphamvu zanu pothandiza ena. Koma kuti mupitirize kuchita zimenezi, muyenera kukhaladi ndi mtima wofuna kuthandiza ena pa zosowa zawo. Yesu ali padziko lapansi anasonyeza chikondi choterocho kwa anthu. Mwachitsanzo, panthawi ina iye ndi ophunzira ake anakwera ngalawa kupita kumalo kopanda anthu kuti ‘akapumule pang’ono.’ Komabe, anthu anafika kumaloko iwo asanafike. “Tsopano potsika, anaona khamu lalikulu la anthu, koma anawamvera chifundo, chifukwa anali ngati nkhosa zopanda m’busa. Ndipo anayamba kuwaphunzitsa zinthu zambiri.”—Maliko 6:30-34.
9.N’chifukwa chiyani m’pofunika kukhala ndi cholinga chabwino chochitira utumiki waupainiya?
9 Mofanana ndi Yesu, ife apainiya tiyenera kukonda anthu kuchokera pansi pa mtima. Chikondi choterocho chimatithandiza kuti tidzipereke powathandiza. Monga mmene mlembi wina ananenera kwa Yesu: “Kum’konda [Mulungu] ndi mtima wonse, ndi kumvetsa konse, ndi mphamvu zonse, komanso kukonda mnansi wako mmene umadzikondera wekha, n’zofunika kwambiri kuposa nsembe zonse zopsereza zathunthu ndi nsembe zina.” (Maliko 12:33) Mawu amenewa akutithandiza kuona kuti zofunika si zinthu zokha zimene timachita mu utumiki wathu, komanso chifukwa chimene timazichitira.
10, 11. Kodi kukonda anthu ngati mmene Khristu ankawakondera kumathandiza bwanji apainiya kupirira mu utumiki?
10 Popeza ndinu mpainiya, mumathera nthawi yochuluka kuposa anthu ambiri pa ntchito yolalikira ndi kupanga ophunzira. Koma mumakumananso ndi anthu ambiri. Kodi mumawaona bwanji anthu amenewa? Mpainiya wina anati: “Ndikudziwa kuti chikondi ndi chipatso cha mzimu wa Mulungu. Choncho popanda chikondi, sindikanakhala n’komwe m’choonadi, ndipo sizikanatheka kuti upainiya wanga uyende bwino. Chikondi chimandithandiza kuchita chidwi ndi anthu, inde, kuzindikira zosowa zawo, ndipo ndaona kuti anthu amakopeka ndi chikondi. N’zoona kuti nthawi zina chikondi chanu chimayesedwa chifukwa cha maganizo a anthu kapena khalidwe lawo. Panthawi imeneyi m’pamene ndimayesetsa kwambiri kumvetsera ndi kuleza mtima.”
11 Kodi inunso mumawaona choncho anthu a m’gawo lanu? Kuti upainiya wanu uyende bwino, muyenera kukonda anthu. (1 Ates. 2:6-8) Koma kuti mukhale wogwira mtima pa ntchito yanu yaupainiya, mufunikanso kukhala ndi ndandanda yabwino. Choncho, dzifunseni kuti:
12. Kodi n’chiyani chimafunika kuti mpainiya achite mokwanira utumiki wake?
12 Kodi Ndili ndi Ndandanda Yabwino?: Kuti mpainiya apitirizebe kuchita upainiya ndipo uzimuyendera bwino, ayenera kulinganiza bwino zinthu. Ngati mulibe ndandanda yabwino, mukhoza kuumva kuwawa upainiya. Komabe, pamafunika zambiri kuwonjezera pa kungokhala ndi ndandanda imene imakuthandizani kuthera nthawi yokwanira mu utumiki wa kumunda.
13. Kodi pali kusiyana kotani pakati pa ndandanda, ndi ndandanda yabwino?
13 Mpainiya amafunika ndandanda yabwino. Kodi inu muli nayo? Mwina mungadzifunse kuti: Kodi ndikuthera nthawi yokwanira m’mbali zosiyanasiyana za utumiki? Kodi ndinganene kuti ndikuchita zonse zomwe ndingathe kuti ndiwafikire anthu a m’gawo langa? Kodi ndimasintha ndandanda yanga kuti ndizilalikira nthawi imene anthuwo ali panyumba? Kodi ndimachita maulendo obwereza ogwira mtima? Yesu anati: “Pitani mukapange ophunzira . . . kuwaphunzitsa.” (Mat. 28:19, 20) Zonse ziwiri, kulalikira ndi kuphunzitsa, ndi mbali zofunika kwambiri za utumiki wathu. Kodi mumangokhutira ndi kugawira mabuku, kapena mumabwereranso kwa onse amene asonyeza chidwi, kaya analandira mabuku ofotokoza za m’Baibulo kapena ayi? Mwachidule, kodi mukugwiritsa ntchito bwino nthawi yanu?
14, 15. Kodi nthawi zonse apainiya amaganizira zokulitsa luso lotani, ndipo pali thandizo lotani lomwe laperekedwa kuti liwathandize kuchita zimenezi?
14 Kodi Ndine Mphunzitsi Wopita Patsogolo?: Limeneli ndi funso linanso lofunika. Pa 2 Timoteyo 4:2, Paulo analemba kuti: “Lalika mawu, chita nawo mwachangu, m’nyengo yabwino ndi m’nyengo yovuta . . . ndi kuleza mtima konse, ndi luso la kuphunzitsa.” Kuti athe kulalikira mawu, kaya ndi mumpingo kapena kunja kwa mpingo, apainiya abwino amayesetsa kupeza luso la kuphunzitsa ndi kulikulitsa. N’chifukwa chiyani Paulo anati kuphunzitsa ndi luso? Chifukwa choti, kuti munthu aphunzitse bwino, amafunika kukhala ndi luso n’kumayesezera kuphunzitsako nthawi ndi nthawi.
15 Kodi mungakulitse bwanji luso lanu lophunzitsa? Mtumwi Paulo anayankha kuti: “Sinkhasinkha zinthu zimenezi mozama. Kangalika nazo, kuti kupita kwako patsogolo kuonekere kwa anthu onse.” (1 Tim. 4:15) Inde, apainiya ayenera kupatula nthawi yophunzirira Baibulo paokha, kuganizira zimene aphunzirazo, ndi kusinkhasinkha. Zimenezi zimaphatikizapo kugwiritsira ntchito malangizo othandiza amene amapezeka m’zofalitsa ngati Kukambitsirana za m’Malemba, Utumiki Wathu wa Ufumu, ndi Pindulani ndi Sukulu ya Utumiki wa Mulungu.
16. Fotokozani mwachidule njira zimene zingakuthandizeni kuti utumiki wanu waupainiya uyende bwino.
16 Choncho, kuti upainiya wanu uyende bwino, khalanibe paubwenzi wolimba ndi Yehova Mulungu. Zimenezi zidzakuthandizani kukonda anthu kuchokera pansi pa mtima ndi kuwasonyeza chikondi chimenecho. Komabe, kuti musonyeze chikondi chimenechi, muyenera kuganizira osati chabe nthawi imene mumathera mu utumiki, komanso muziigwiritsa ntchito bwino. Kodi mungachite bwanji zimenezo? Mwa kuyesetsa kufikira anthu ambiri amene mungathe ndi uthenga wa Ufumu. Pomaliza, pitirizani kupita patsogolo monga mphunzitsi mwa kuphunzira njira zosiyanasiyana zolankhulira ndi anthu mu utumiki ndi kuphunzira Baibulo mwakhama n’cholinga chokulitsa luso lanu la kuphunzitsa.