Zilengezo
◼ Mabuku ogawira mu April ndi May: Tidzagawira magazini a Nsanja ya Olonda ndi Galamukani! Mukamachita maulendo obwereza kwa anthu achidwi, ngakhalenso amene anafika pa Chikumbutso kapenanso pamisonkhano ina koma safika pa misonkhano ya mpingo nthawi zonse, yesetsani kuwagawira buku la Baibulo Limaphunzitsa Chiyani, ndi cholinga choyambitsa phunziro la Baibulo. June: Mungathe kugawira buku la Creator kapena la Chimwemwe cha Banja. July: Gwiritsani ntchito kalikonse ka timabuku tamasamba 32 totsatirati: Dikirani!, Mizimu ya Akufa—Kodi Ingakuthandizeni Kapena Kukuvulazani? Kodi Iyo Ilikodi?, Njira ya ku Moyo Wosatha—Kodi Mwaipeza? ndi Pamene Munthu Amene Mumakonda Amwalira.
◼ Kuyambira mu April, tizitumiza mabaji a msonkhano wachigawo wa 2007 tikamatumiza mabuku. Simukufunika kuitanitsa mabajiwa. Ngati mpingo ukufuna mabaji ena, itanitsani pa Fomu Yofunsira Mabuku (S-14). Muitanitse mapulasitiki oikamo baji a aliyense amene alibe mumpingo wanu.
◼ Alembi a mipingo azisunga mafomu okwanira a Chofunsirapo Utumiki wa Upainiya Wokhazikika (S-205) ndi Chofunsirapo Utumiki wa Upainiya Wothandiza (S-205b). Angaitanitse mafomuwa pa Fomu Yofunsira Mabuku (S-14). Muzikhala ndi mafomu okwanira chaka chimodzi. Musanatumize ku nthambi mafomu a anthu amene afunsira upainiya wokhazikika, onetsetsani kuti mafunso onse ayankhidwa.
◼ Ofesi ya nthambi imayenera kukhala ndi maadiresi ndi manambala a foni amene akugwira ntchito panopo a oyang’anira otsogolera ndi alembi onse. Zimenezi zikangosintha nthawi ina iliyonse, Komiti ya Utumiki ya Mpingo izilemba ndi kusaina fomu ya Kusintha Adiresi ya Woyang’anira Wotsogolera/Mlembi (S-29) ndi kuitumiza mwamsanga kuofesi ya nthambi. Zimenezi zikuphatikizapo kusintha kulikonse kwa manambala a foni.
◼ Ena afunsapo ngati kuli kololeka kukopera ena mumpingo CD ya Watchtower Library—CD-ROM, kapena kungowabwereka kuti akailowetse mu kompyuta mwawo. Pangano limene mumavomereza mukamalowetsa Watchtower Library—CD-ROM mu kompyuta limaletsa zimenezi. Choncho, tikulimbikitsa abale ndi alongo kuitanitsa CD yawoyawo ya Watchtower Library—CD-ROM kudzera ku mpingo.
◼ Tidakali ndi buku lakuti Live With Jehovah’s Day in Mind m’Chingelezi. Buku limeneli linatuluka chaka chatha pamsonkhano wachigawo wakuti “Chipulumutso Chayandikira.” Ofalitsa amene amawerenga ndi kumva Chingelezi akulimbikitsidwa kuitanitsa buku limeneli kudzera ku mipingo yawo pa Fomu Yofunsira Mabuku (S-14).