Kodi Achinyamata Mukufuna Kuchita Chiyani Pamoyo Wanu?—Gawo 2 Utumiki wa Nthawi Zonse
1 Upainiya. Mpainiya ndi wofalitsa wobatizidwa wachitsanzo chabwino amene amalalikira uthenga wabwino kwa maola 70 kapena kuposerapo pamwezi. Mukamathera nthawi yochuluka muutumiki wa kumunda, zidzakuthandizani kukhala ndi luso kwambiri polalikira ndi pophunzitsa. Apainiya ambiri amasangalala kuona anthu amene awathandiza kuphunzira Baibulo akukhala Mboni zobatizidwa. Kodi ndi ntchito inanso iti imene ingakhale yosangalatsa kuposa pamenepa?
2 Kuti azidzipezera zofunika pamoyo, apainiya ambiri amagwira ntchito yaganyu. Ambiri amakonzekera udindo umenewu mwa kuphunzira ntchito zaluso kusukulu kapena kwa makolo awo. Kodi inuyo ndi makolo anu mukuona kuti ndi bwino kuphunzira ntchito ina mutamaliza sukulu yasekondale? Onetsetsani kuti cholinga chochitira zimenezi sikufuna ndalama zambiri, koma kuti mudzathandizike pa utumiki wanu ndiponso kuti kapena mudzayambe utumiki wa nthawi zonse.
3 Koma chachikulu pamoyo wa mpainiya si ntchito yake yolembedwa ayi, koma utumiki wake wothandiza ena kupeza moyo. Bwanji osaganiza zochita upainiya pamoyo wanu? Munthu akamachita upainiya, amakhala ndi mwayi wochita zina zambiri. Mwachitsanzo, apainiya ena amasamukira ku madera kumene kulibe ofalitsa Ufumu ambiri. Ena amaphunzira chinenero china ndi kukatumikira ku mpingo wa chinenerocho kwawo komweko kapena kudziko lina. Upainiya ndi ntchito yopindulitsadi!
4 Sukulu Yophunzitsa Utumiki inakhazikitsidwa kuti iziphunzitsa ena a akulu ndi atumiki othandiza osakwatira. Zina zimene amaphunzira ku sukulu ya milungu 8 imeneyi ndi udindo wa akulu ndi atumiki othandiza, kayendetsedwe ka gulu, ndiponso luso lolankhula ndi anthu. Akamaliza maphunzirowa, ena amatumikira m’dziko mwawo ndipo ena amatumizidwa mayiko ena.
5 Munthu amene amachita utumiki wa pa Beteli amagwira ntchito yongodzipereka pa nthambi ya Mboni za Yehova. Ena pa Betelipo amagwira ntchito yopanga mabuku ofotokoza Baibulo. Ena amagwira ntchito zina, monga kusamalira nyumba, zida, makina komanso kusamalira banja la Beteli. Ntchito zonsezi ndi utumiki wopatulika kwa Yehova. Onse ogwira ntchito pa Beteli amasangalala podziwa kuti ntchito yawo imathandiza abale awo ambirimbiri padziko lonse.
6 Nthawi zina abale amene ali ndi luso lapadera amaitanidwa ku Beteli. Koma ambiri amakaphunzitsidwa ntchito komweko. Anthu ku Beteliko sagwira ntchito kuti apeze ndalama koma amakhutira ndi zimene amapatsidwa monga chakudya, malo ogona, ndi ndalama pang’ono zogulira zosowa zawo. Pofotokoza utumiki wake, mnyamata wina wogwira ntchito pa Beteli anati: “Umenewu ndi utumiki wabwino kwambiri. Moyo wake ndi wopanikiza inde, koma ndapeza madalitso ankhaninkhani.”
7 Tumikirani Yehova ndi Moyo Wonse: Munthu ukamatumikira Yehova, umakhala ndi moyo wabwino kwambiri. Bwanji osaganiza zotumikira Mulungu muutumiki wa nthawi zonse? Kambiranani ndi makolo anu, akulu, ndi woyang’anira dera za utumiki umenewu. Ngati mukufuna kupita ku Beteli, ku Gileadi, kapena ku Sukulu Yophunzitsa Utumiki, kapezekeni pa misonkhano ya amene akufuna kulembetsa zimenezi pamsonkhano wadera ndi wachigawo.
8 Si onse amene angayenerere kapena angachite utumiki wa nthawi zonse. Nthawi zina anthu amalephera kuchita utumiki umenewu chifukwa cha matenda, mavuto a zachuma, ndi udindo umene angakhale nawo pabanja. Ngakhale zili choncho, Akhristu onse odzipereka amamvera lamulo la m’Baibulo lakuti: “Uzikonda Yehova Mulungu wako ndi mtima wako wonse, ndi moyo wako wonse, ndi maganizo ako onse.” (Mat. 22:37) Yehova amafuna kuti muchite zimene mungathe malinga ndi mmene zinthu zilili pa moyo wanu. Ndiye kaya zinthu zili bwanji, onetsetsani kuti chachikulu pamoyo wanu ndi kutumikira Yehova. Khalani ndi zolinga zauzimu zoti mutha kuzikwaniritsa. Zoonadi, ‘mukakumbukira Mlengi wanu masiku a unyamata wanu,’ mudzapeza madalitso osatha.