Kubwereza za M’sukulu ya Utumiki wa Mulungu
Mafunso otsatirawa mudzawakambirana pa Sukulu ya Utumiki wa Mulungu ya mlungu woyambira June 25, 2007. Woyang’anira sukulu adzatsogolera kubwereza nkhani zomwe zakambidwa m’kati mwa milungu ya May 7 mpaka June 25, 2007. Kubwerezaku kudzakhala kwa mphindi 30. [Dziwani izi: Pa funso lomwe kumapeto kwake silikusonyeza buku lililonse lomwe mwatengedwa nkhaniyo, ndiye kuti muyenera mufufuze nokha kuti mupeze mayankho ake.—Onani buku la Sukulu ya Utumiki, mas. 36-7.]
LUSO LA KULANKHULA
1. Kodi tingamasuke bwanji polankhula kuti mawu athu amveke bwino? [be-CN tsa. 184 ndime 2 mpaka tsa. 185 ndime 2 mpaka 3]
2. Kodi tingakhale “zinthu zonse kwa anthu osiyanasiyana” mu utumiki wathu m’njira ziti? (1 Akor. 9:20-23) [be-CN tsa. 186 ndime 2 mpaka 4]
3. Kodi tingatengere motani chitsanzo cha Yehova chomvetsera ena akamalankhula? (Gen. 18:23-33; 1 Maf. 22:19-22) [be-CN tsa. 186 ndime 5 mpaka tsa. 187 ndime 1 ndi ndime 5]
4. Tingathandize ena kupita patsogolo mwauzimu m’njira ziti? [be-CN tsa. 187 ndime 5 mpaka tsa. 188 ndime 3]
5. N’chifukwa chiyani tiyenera kusonyeza ulemu kwa ena? [be-CN tsa. 190 ndime 3, ndi bokosi]
NKHANI NA. 1
6. N’chifukwa chiyani tiyenera kuyesetsa kuwafika pa mtima anthu amene timawaphunzitsa? [be-CN tsa. 59 ndime 1]
7. Kodi chitsanzo chathu chimakhudza bwanji anthu amene timawaphunzitsa? [be-CN tsa. 61 ndime 1]
8. Kodi tingakulitse bwanji luso lathu locheza ndi anthu a m’banja mwathu? [be-CN tsa. 62 ndime 3]
9. Kodi atumiki othandiza ayenera kuona bwanji udindo wawo mumpingo? [od-CN tsa. 58 ndime 1]
10. Kodi aliyense angachite chiyani kuti apindule mokwanira ndi chakudya chauzimu cha Phunziro la Nsanja ya Olonda? [od-CN tsa. 62 ndime 1]
KUWERENGA BAIBULO KWA MLUNGU NDI MLUNGU
11. Kodi zimene Yeremiya anakumana nazo zofotokozedwa pa Yeremiya 37:21, zimatilimbikitsa bwanji?
12. N’chifukwa chiyani Baruki anati ‘Yehova waonjezera chisoni pa zowawa zake,’ n’kumuchititsa ‘kulema,’ ndipo Baruki anachita chiyani ndi vutoli poyamba? (Yer. 45:1-5)
13. Kodi ndi liti pamene Babulo ‘anakhala bwinja’ ndiponso pamene anthu anasiyiratu kukhalako? (Yer. 50:13)
14. Kodi lemba la Maliro 3:8, 9, 42-45 limasonyeza bwino mfundo iti yokhudza pemphero?
15. Kodi galeta lofotokozedwa m’mutu woyamba wa Ezekieli limaimira chiyani?