Zilengezo
◼ Mabuku ogawira mwezi wa June: Gawirani Chimwemwe cha Banja. July ndi August: Mungagwiritse ntchito kalikonse ka timabuku ta masamba 32 iti: Dikirani!, Mizimu ya Akufa Ingakuthandizeni Kapena Kukuvulazani? Kodi Iyo Ilikodi?, Njira ya ku Moyo Wosatha—Kodi Mwaipeza?, ndi Pamene Munthu Amene Mumakonda Amwalira. September: Gawirani buku la Kodi Baibulo Limaphunzitsa Chiyani Kwenikweni? Yesetsani kwambiri kuyambitsa phunziro la Baibulo paulendo wanu woyamba. Ngati mwininyumba ali nalo kale bukuli, mum’sonyeze mmene angapindulire nalo mwa kupanga naye mwachidule phunziro la Baibulo.
◼ Woyang’anira wotsogolera kapena wina amene iye wam’sankha awerengere maakaunti a mpingo a miyezi ya March, April, ndi May. Mukatha kuwerengerako, lengezani kumpingo pamodzi ndi lipoti lotsatira la maakaunti.—Onani Malangizo Oyendetsera Maakaunti a Mpingo (S-27).
◼ Mipingo iitanitse mafomu okwanira a Chaka Chautumiki cha 2008 pafomu yawo yotsatira yofunsira mabuku. Simudzafunikira kuitanitsa mafomu otsatirawa chifukwa adzatumizidwa pamodzi ndi mafomu amene timatumiza chaka ndi chaka: Maemvulopu a khadi la lipoti (rce), Lipoti la Mpingo (S-1), Fomu Yofunsira Mabuku (S-14), Fomu Yotumizira Zopereka (S-20), Lipoti la Kuwerengera Maakaunti a Mpingo (S-25), Pepala la Maakaunti (S-26), ndi Lipoti la Maakaunti a Mpingo la Pamwezi (S-30). Muzigwiritsa ntchito mafomuwa mogwirizana ndi ntchito yake basi.
◼ Posachedwapa mpingo uliwonse udzalandira mafomu a Chaka Chautumiki cha 2008 amene amatumizidwa chaka chilichonse mu emvulopu yaikulu.
◼ Nyimbo zotsatirazi zidzaimbidwa pa msonkhano wachigawo wa chaka chino: 4, 11, 31, 34, 38, 42, 91, 105, 150, 160, 168, 181, 191, 200, 205, 207, 209, ndi 224. Kuti anthu adzathe kuimba bwinobwino nyimbozi, tikulimbikitsa mipingo yonse kuphunzira nyimbo imodzi kapena ziwiri pambuyo pa msonkhano uliwonse.
◼ Ma CD Atsopano Amene Alipo:
Kingdom Melodies—MP3 (mpmel)—Chingelezi