Ndandanda ya Misonkhano ya Utumiki
Mlungu Woyambira August 13
Mph.15: Zilengezo za pampingo. Gwiritsani ntchito mfundo zimene zili pa tsamba 8 kapena mfundo zina zothandiza m’gawo lanu, posonyeza zitsanzo za mmene tingagawirire Nsanja ya Olonda ya August 15 ndi Galamukani! ya August. M’chitsanzo chimodzi, wofalitsa agwiritse ntchito ulaliki womwe uli pa tsamba 3, ndime 3 mu Utumiki Wathu wa Ufumu uno kufunsa funso lomwe adzayankhe paulendo wobwereza. (Ngati mpingo wanu sunalandire magazini tatchulawa gwiritsirani ntchito zitsanzo za mu Utumiki Wathu wa Ufumu wa mwezi watha.)
Mph.15: Mmene Tingapindulire Pogonjera Dongosolo la Mulungu Lolemekeza Mutu. Nkhani yokambirana ndi omvetsera yochokera mu buku la Gulu Lochita Chifuniro cha Yehova mutu 15.
Mph.15: “Kulambira Yehova Pamodzi Monga Banja.”a Pemphani omvetsera kuti afotokoze mmene apindulira chifukwa chochita utumiki monga banja. Mungakonzeretu zoti wofalitsa mmodzi kapena awiri adzapereke ndemanga zawo.
Nyimbo Na. 48 ndi pemphero lomaliza.
Mlungu Woyambira August 20
Mph.10: Zilengezo za pampingo. Kambiranani “Pulogalamu Yatsopano ya Tsiku la Msonkhano Wapadera,” ndipo lengezani tsiku la msonkhano wapadera ngati mukulidziwa.
Mph.15: Yambitsani Phunziro la Baibulo Paulendo Woyamba mu September. Kukambirana ndi omvetsera. M’mwezi wa September tidzagawira buku la Baibulo Limaphunzitsa Chiyani ndipo yesetsani kukambirana ndi mwininyumba ndime zingapo paulendo woyamba. Kambiranani malingaliro omwe ali mu mphatika ya Utumiki Wathu wa Ufumu wa January 2006, ndipo chitani chitsanzo chimodzi kapena ziwiri za mmene tingayambitsire phunziro la Baibulo paulendo woyamba.
Mph.20: “Mmene Phunziro la Buku la Mpingo Limatithandizira.”b Pokambirana ndime 5, phatikizanipo ndemanga zochokera mu buku la Gulu, tsamba 41 ndime 3.
Nyimbo Na. 6 ndi pemphero lomaliza.
Mlungu Woyambira August 27
Mph.10: Zilengezo za pampingo. Werengani lipoti la maakaunti ndi mawu oyamikira zopereka olembedwa pa sitetimenti. Gwiritsani ntchito mfundo zimene zili pa tsamba 8 kapena mfundo zina zothandiza m’gawo lanu, posonyeza zitsanzo za mmene tingagawirire Nsanja ya Olonda ya September 1 ndi Galamukani! ya September. (Ngati mpingo wanu sunalandire magazini tatchulawa gwiritsirani ntchito zitsanzo za mu Utumiki Wathu wa Ufumu wa mwezi watha.)
Mph.10: ‘Pezani Mabwenzi ndi Chuma Chosalungama.’ Nkhani yokambidwa ndi mkulu yochokera mu Nsanja ya Olonda ya December 1, 1994, masamba 13 mpaka 18.
Mph.25: “Cholinga Chabwino Kwambiri M’chaka Chautumiki Chatsopano.”c Funsani wofalitsa mmodzi kapena awiri omwe achitapo upainiya wothandiza posachedwapa. Kodi n’chiyani chimene anasintha pa zochita zawo zatsiku ndi tsiku? Kodi anapindula motani? Mmodzi mwa ofunsidwawo akhale munthu yemwe anatha kuchita upainiya wothandiza chifukwa chothandizidwa ndi anthu ena a pabanja lake. Pokambirana ndime 9, tchulani masiku omwe mudzakhalanso ndi woyang’anira dera ngati mukuwadziwa.
Nyimbo Na. 196 ndi pemphero lomaliza.
Mlungu Woyambira September 3
Mph.10: Zilengezo za pampingo ndipo zilengezo zina musankhe mu Utumiki Wathu wa Ufumu uno. Kumbutsani ofalitsa kuti apereke malipoti awo a utumiki wa kumunda a mwezi wa August.
Mph.15: “Timayamikira Kwambiri Mwayi Umene Tili Nawo.”d Ngati nthawi ilola, pemphani omvetsera kuti afotokoze malemba omwe ali m’nkhaniyi.
Mph.20: “Mmene Tingayambitsire Maphunziro a Baibulo ndi Anthu Omwe Timawagawira Magazini.”e Chitani chitsanzo chachidule cha mmene tingagwiritsire ntchito maulaliki omwe ali m’ndime 2. Kumbutsani ofalitsa kuti angayambe kulemba lipoti la phunziro la Baibulo akachititsa phunzirolo kawiri kuchokera nthawi imene anasonyeza munthuyo mmene azichitira naye phunzirolo ndiponso ngati iwo akuona kuti apitiriza kuchita phunziro ndi munthuyo.
Nyimbo Na. 2 ndi pemphero lomaliza.
[Mawu a M’munsi]
a Mawu oyamba asapitirire mphindi imodzi, ndiyeno kambiranani mwa mafunso ndi mayankho.
b Mawu oyamba asapitirire mphindi imodzi, ndiyeno kambiranani mwa mafunso ndi mayankho.
c Mawu oyamba asapitirire mphindi imodzi, ndiyeno kambiranani mwa mafunso ndi mayankho.
d Mawu oyamba asapitirire mphindi imodzi, ndiyeno kambiranani mwa mafunso ndi mayankho.
e Mawu oyamba asapitirire mphindi imodzi, ndiyeno kambiranani mwa mafunso ndi mayankho.