Kubwereza za M’sukulu ya Utumiki wa Mulungu
Mafunso otsatirawa mudzawakambirana pa Sukulu ya Utumiki wa Mulungu ya mlungu woyambira October 29, 2007. Woyang’anira sukulu adzatsogolera kubwereza nkhani zomwe zakambidwa m’kati mwa milungu ya September 3 mpaka October 29, 2007. Kubwerezaku kudzakhala kwa mphindi 30.
LUSO LA KULANKHULA
1. Kodi ndi chifukwa chiyani kubwereza ndi luso lofunika pophunzitsa? [be-CN tsa. 206 ndime 1 ndi 2, bokosi]
2. Kodi mutu wa nkhani tingautsindike bwanji? [be-CN tsa. 210, bokosi]
3. Kodi mfundo zazikulu za nkhani ndiye chiyani, ndipo n’chiyani chingatithandize kusankha mfundozo? [be-CN tsa. 212 ndime 1 mpaka 3]
4. N’chifukwa chiyani sitiyenera kuchulukitsa mfundo zazikulu m’nkhani? [be-CN tsa. 213 ndime 2 mpaka 4]
5. Kodi ndi chifukwa chiyani mawu athu oyamba afunika kukopa chidwi, ndipo tingachite motani zimenezi? [be-CN tsa. 215 ndime 1; tsa. 216 ndime 1 mpaka 3, bokosi]
NKHANI NA. 1
6. Kodi lemba la Salmo 119:89, 90 limatithandiza bwanji kuzindikira kuti titha kudalira mawu a Mulungu? [w05-CN 4/15 tsa. 15 ndime 3]
7. Kodi ndi liti pamene tiyenera kubwereza mfundo ndi cholinga chozimveketsa? [be-CN tsa. 207, bokosi]
8. Kodi “mawu a Yehova” angateteze bwanji mtima wathu? (Sal. 18:30) [w05-CN 9/1 tsa. 30 ndime 2]
9. Kodi njira yofunika kwambiri younikira mfundo zazikulu ndi yotani? [be-CN tsa. 214 ndime 2]
10. Kodi ndi chifukwa chiyani mawu oyamba okopa chidwi ali ofunika? [be-CN tsa. 215, bokosi]
KUWERENGA BAIBULO KWA MLUNGU NDI MLUNGU
11. Kodi kuyesa kachisi kwa m’masomphenya a Ezekieli kunatanthauza chiyani, ndipo zimenezi zimatitsimikizira za chiyani masiku ano? (Ezek. 40:2-5) [w99-CN 3/1 tsa. 9 ndime 6; tsa. 14 ndime 7]
12. Pamene masomphenya a Ezekieli akukwaniritsidwa komaliza, kodi “kalonga” ndani? (Ezek. 48:21) [w99-CN 3/1 tsa. 16 ndime 13 mpaka 15; mas. 22 ndi 23 ndime 19 ndi 20]
13. Kodi lemba la Danieli 2:21 limatanthauza chiyani? [w98-CN 9/15 tsa. 12 ndime 9]
14. Kodi ndi chifukwa chiyani Danieli anali ‘wokondedwa kwambiri’ pamaso pa Yehova? (Dan. 9:23) [dp-CN tsa. 185 ndime 12; w04-CN 8/1 tsa. 12 ndime 17]
15. Kodi zinatheka bwanji kuti musakhale “kudziwa Mulungu m’dziko” la Isiraeli, ndipo ifeyo tiyenera kuwaona motani mawu amenewo? (Hos. 4:1, 2, 6) [w05-CN 11/15 tsa. 21 ndime 21; jd mas. 57 ndi 58 ndime 5; tsa. 61 ndime 10]