Zilengezo
◼ Mabuku ogawira mu October: Magazini ya Nsanja ya Olonda ndi ya Galamukani! Anthu akasonyeza chidwi, agawireni ndi kukambirana nawo za m’kapepala ka Kodi Mukufuna Kudziŵa Zambiri za Baibulo? Chitani zimenezi ndi cholinga choyambitsa phunziro la Baibulo. November: Phunzirani kwa Mphunzitsi Waluso. Ngati anthu anena kuti alibe ana, agawireni kabuku kakuti Dikirani! December: Munthu Wamkulu Woposa Onse Amene Anakhalako. Ngati mulibe buku limeneli, mungagawire buku la Yandikirani kwa Yehova kapena la Chinsinsi cha Chimwemwe cha Banja. January: Gawirani kabuku ka Dikirani!
◼ Mwezi wa December ndi mwezi wabwino kwambiri kuchita upainiya wothandiza chifukwa choti uli ndi masiku asanu a Loweruka ndi Lamlungu.
◼ Mphatika imene ili mu Utumiki Wathu wa Ufumu uno ndi “Ndandanda ya Sukulu ya Utumiki wa Mulungu ya 2008.” Isungeni kuti mudzaigwiritse ntchito chaka chonse cha 2008.
◼ Dziwani kuti m’bale yemwe akukamba nkhani yomaliza mu Msonkhano wa Utumiki ndi amene ayenera kutchula nyimbo yomaliza akatha kukamba nkhaniyo. Ndiyeno, iyeyo kapena m’bale wina woyenerera yemwe anauzidwiratu atseke msonkhanowo ndi pemphero.
◼ Mabuku Atsopano Amene Alipo:
Watch Tower Publications Index 1992-2005 (dx92-05)—Chinenero cha Manja cha ku America
Moyo m’Dziko Latsopano la Mtendere (Kapepala Na. 15)—Chitonga
Sangalalani ndi Moyo Wabanja (Kapepala Na. 21)—Chitonga
Yehova—Kodi Iye Ndani? (Kapepala Na. 23)—Chitonga
Yesu Khristu—Kodi Iye Ndani? (Kapepala Na. 24)—Chitonga
◼ Mabuku Amene Adakalipobe:
Watch Tower Publications Index 2002 (dx02)—Chingelezi