Ndandanda ya Misonkhano ya Utumiki
Mlungu Woyambira October 8
Mph.10: Zilengezo za pampingo. Chitani zitsanzo za mmene tingagawirire Nsanja ya Olonda ya October 15 ndi Galamukani! ya October pogwiritsa ntchito mfundo zimene zili pa tsamba 8 kapena mfundo zina zothandiza m’gawo lanu. M’zitsanzo zonse, gawirani magazini onse awiri ngakhale kuti mwachita chitsanzo cha magazini imodzi yokha. (Ngati mpingo wanu sunalandire magazini tatchulawa gwiritsirani ntchito zitsanzo za mu Utumiki Wathu wa Ufumu wa mwezi watha.)
Mph.20: Musalekane Nalo Gulu la Yehova. Nkhani ndi kukambirana ndi omvera kuchokera m’buku la Gulu Lochita Chifuniro cha Yehova, mutu 17.
Mph.15: “Tidzagawira Magazini Yapadera ya Galamukani! mu November.”a Fotokozani mwachidule zomwe zili m’magaziniyi. Ndiyeno kambiranani nkhaniyi mwa mafunso ndi mayankho. Pokambirana ndime yachitatu, chitani chitsanzo cha mmene tingagawirire magaziniyi pogwiritsa ntchito mfundo za patsamba 8 kapena mfundo zina zothandiza m’gawo lanu. Chitsanzochi chisanathe wofalitsayo amusiyire mwininyumba nkhani yodzakambirana pa ulendo wobwereza.
Mlungu Woyambira October 15
Mph.10: Zilengezo za pampingo. Musankhe zilengezo zina mu Utumiki Wathu wa Ufumu uno.
Mph.20: Kodi Choonadi Chikubala Zipatso mwa Anthu Amene Mumawaphunzitsa? Nkhani ndi kukambirana ndi omvera kuchokera mu Nsanja ya Olonda ya February 1, 2005, patsamba 28 mpaka 30. Phatikizanipo ndemanga za momwe mafunso a m’buku la Baibulo Limaphunzitsa Chiyani akonzedwera kutithandiza kudziwa zimene zili mu mtima wa ophunzira. Kambiranani zitsanzo zingapo, monga mutu 1, ndime 19; mutu 2, ndime 4; mutu 3, ndime 24; ndi mutu 4, ndime 18. Limbikitsani ofalitsa kugwiritsa ntchito bwino zinthu zothandiza kuphunzitsa zimene zili m’bukuli monga mafanizo, zinthuzi, mafunso ndi zina zotero.
Mph.15: Kodi Mukukumbukira? Nkhani yokambirana ndi omvera yochokera mu Nsanja ya Olonda ya August 15, 2007, patsamba 19.
Mlungu Woyambira October 22
Mph.10: Zilengezo za pampingo. Werengani lipoti la maakaunti ndi mawu oyamikira zopereka olembedwa pa sitetimenti. Chitani zitsanzo za mmene tingagawirire Nsanja ya Olonda ya November 1 ndi Galamukani! ya November pogwiritsa ntchito mfundo zimene zili pa tsamba 8 kapena mfundo zina zothandiza m’gawo lanu. (Ngati mpingo wanu sunalandire magazini tatchulawa gwiritsirani ntchito zitsanzo za mu Utumiki Wathu wa Ufumu wa mwezi watha.)
Mph.15: Zosowa za pampingo.
Mph.20: Yendanibe Ngati Ana a Kuwala. Nkhani ndi kufunsa anthu ena mafunso. Tinachoka mu mdima wa dzikoli ndipo tinasankha kutsogozedwa ndi kuunika kwa Yehova. (Aef. 5:8, 9) Izi zapangitsa moyo wathu kukhala wabwinopo ndiponso kukhala ndi cholinga. (1 Tim. 4:8) Kuwala kumeneku kumatipatsanso chiyembekezo. (Aroma 15:4) Funsani ofalitsa awiri kapena atatu amene anakumana ndi mavuto aakulu chifukwa chofuna kukhala paubwenzi wabwino ndi Yehova ndipo anathana nawo bwino. Kodi anakumana ndi mavuto otani pamene anali kuphunzira choonadi? Kodi anathana nawo bwanji? Kodi apindula motani pamoyo wawo chifukwa choti aphunzira choonadi? Kodi n’chiyani chimawathandiza kukhalabe olimba m’choonadi? Malizani mwa kulimbikitsa onse kupitiriza kulimbitsa ubwenzi wawo ndi Yehova ndi kupitiriza kusonyeza kuyamikira choonadi chimene watiphunzitsa.—2 Pet. 1:5-8.
Mlungu Woyambira October 29
Mph.10: Zilengezo za pampingo. Kumbutsani ofalitsa kuti apereke malipoti awo a utumiki wa kumunda a mwezi wa October. Tchulani buku logawira mu November, ndipo chitani chitsanzo cha momwe tingagawirire bukuli.
Mph.15: Khalani ndi Zolinga Zauzimu Kuti Mulemekeze Nazo Mlengi Wanu. Nkhani ndi kukambirana ndi omvera kuchokera mu Nsanja ya Olonda ya July 15, 2004, patsamba 21 mpaka 23. Pemphani omvera kunena zolinga zauzimu zimene ali nazo ndiponso zimene akuchita kuti azikwaniritse. Mungauziretu wofalitsa mmodzi kapena awiri kuti adzalankhulepo.
Mph.20: “Limbikitsani Osauka.”b Pokambirana ndime yachiwiri, phatikizanipo ndemanga za mu Galamukani! ya September 8, 2003, patsamba 28 ndi 29.
Mlungu Woyambira November 5
Mph.10: Zilengezo za pampingo.
Mph.15: Mmene Mungatetezere Ana Anu ndi Nzeru za Mulungu. Nkhani yochokera mu Nsanja ya Olonda ya January 1, 2005, patsamba 23 mpaka 27.
Mph.20: “Aliyense Amalimbikitsidwa.”c Pemphani omvera kuti afotokoze mmene woyang’anira woyendayenda anawalimbikitsira panthawi imene anali pampingopo. Mungauziretu wofalitsa mmodzi kapena awiri kuti adzalankhulepo.
[Mawu a M’munsi]
a Mawu oyamba asapitirire mphindi imodzi, ndiyeno kambiranani mwa mafunso ndi mayankho.
b Mawu oyamba asapitirire mphindi imodzi, ndiyeno kambiranani mwa mafunso ndi mayankho.
c Mawu oyamba asapitirire mphindi imodzi, ndiyeno kambiranani mwa mafunso ndi mayankho.