Ndandanda ya Misonkhano ya Utumiki
Mlungu Woyambira February 11
Mph.10: Zilengezo za pampingo. Pogwiritsa ntchito mfundo zimene zili pa tsamba 8, kapena ulaliki wina uliwonse umene ungakhale wothandiza m’gawo lanu, khalani ndi chitsanzo cha mmene tingagawirire Nsanja ya Olonda ya February 1 ndi Galamukani! ya February.
Mph.15: Kodi Mungakatumikire Kumene Kukufunika Antchito Ambiri? Nkhani ndi kukambirana ndi omvetsera yotengedwa mu Nsanja ya Olonda ya July 15, 2003, tsamba 20. Onjezanipo ndemanga za m’buku la Gulu, tsamba 111, ndime 1 mpaka tsamba 112 ndime 1. Mwachidule funsani mafunso aliyense amene akutumikira kudera kumene kulibe ofalitsa okwanira. Kodi anakumana ndi mavuto otani, ndipo anathana nawo bwanji? Kodi ndi madalitso otani amene anapeza?
Mph.20: Thandizani Atumiki Atsopano Kupita Patsogolo. Pambuyo pokamba mawu oyamba osapitirira mphindi imodzi, kambiranani mwa mafunso ndi mayankho nkhani ya mu Nsanja ya Olonda ya December 1, 2005, tsamba 31 pogwiritsa ntchito mafunso amene aperekedwa. Mukamaliza kukambirana ndime 18, khalani ndi chitsanzo chosonyeza mwininyumba akutsutsa wofalitsa watsopano yemwe akuyenda ndi wofalitsa wodziwa bwino utumiki wake. Wofalitsa watsopanoyo sakuyankha mogwira mtima ndipo mwininyumbayo akuthetsa kukambitsiranako. Pochoka panyumbapo, wofalitsa walusoyo akuyamikira wofalitsa watsopano uja pa zimene wachita, ndipo kenako akumuonetsa mmene angadzagwiritsirire ntchito buku la Kukambitsirana poyankha anthu amene sakufuna kuwalalikira.
Mlungu Woyambira February 18
Mph.10: Zilengezo za pampingo. Zilengezo zina musankhe mu Utumiki Wathu wa Ufumu uno. Kambiranani “Pulogalamu Yatsopano ya Msonkhano Wadera.” Lengezani deti la msonkhano wadera wotsatira ngati mukulidziwa.
Mph.10: Zosowa za pampingo.
Mph.25: “Umboni wa Chikhulupiriro.”a Yoti ikambidwe ndi woyang’anira utumiki. Malizani pofotokoza mwachidule zimene mpingo wachita chaka cha utumiki chathachi ndipo uyamikireni.
Mlungu Woyambira February 25
Mph.10: Zilengezo za pampingo. Kumbutsani ofalitsa kupereka malipoti awo a utumiki wa kumunda a mwezi wa February. Werengani lipoti la maakaunti ndi kuyamikira zopereka zolembedwa pa sitetimenti. Chitani chitsanzo chosonyeza mmene mungagawirire timapepala toitanira anthu ku Chikumbutso kwa wachibale wathu kapena kwa mnzathu woyandikana naye nyumba.
Mph.20: “Kumbukirani Dipo ndi Mtima Woyamikira.”b Ngati nthawi ingalole, pemphani omvetsera kupereka ndemanga pa malemba osagwidwa mawu.
Mph.15: Konzekerani Kugawira Magazini Atsopano. Kukambirana ndi omvetsera. Pambuyo pofotokoza mwachidule zimene zili mu Nsanja ya Olonda ya March 1 ndi Galamukani! ya March, pemphani omvetsera kuti atchule nkhani zimene zingasangalatse anthu a m’gawo lanu ndipo afotokoze chifukwa chake. Pemphani omvetsera kuti atchule mfundo zimene akufuna kukatchula m’nkhani zimene akufuna kukagwiritsa ntchito pogawira magaziniwa. Ndi mafunso ati amene angafunsidwe kuti muyambitse makambirano? Ndi malemba ati m’nkhanizo amene mungakagwiritse ntchito? Pogwiritsa ntchito mfundo zimene zafotokozedwa, chitani chitsanzo cha mmene mungagawirire Nsanja ya Olonda ya March 1 ndi Galamukani! ya March.
Mlungu Woyambira March 3
Mph.10: Zilengezo za pampingo. Kambiranani mfundo zazikulu za m’bokosi lakuti “Zofunika Kukumbukira pa Chikumbutso.”
Mph.20: Kodi Mungayambitse Phunziro la Baibulo M’mwezi wa March? Kukambirana ndi omvetsera. M’mwezi wa March, tidzagawira buku la Baibulo Limaphunzitsa Chiyani n’cholinga choyambitsa maphunziro a Baibulo. Nenanipo za mbali zothandiza kwambiri za buku limeneli. Kambiranani zimene tinganene pogawira bukuli tikabwerera kwa munthu yemwe anasonyeza chidwi panthawi imene tinamusiyira kapepala koitanira anthu ku Chikumbutso, tikamabwerera kwa munthu amene tinamusiyira magazini, ndiponso tikamagawira bukuli mu utumiki wa khomo ndi khomo pambuyo pa March 22. (Onani km-CN 8/07 tsa. 3, ndime 3; km-CN 3/06 tsa. 1; km-CN 1/06 mas. 3-6.) Chitani chitsanzo chimodzi kapena ziwiri za zimenezi.
Mph.15: Gwiritsani Ntchito Baibulo Poyankha Mafunso. Nkhani ndi kukambirana ndi omvetsera kuchokera m’buku la Sukulu ya Utumiki, masamba 143-144. Khalani ndi chitsanzo chachidule chosonyeza wofalitsa akufunsidwa funso limene anthu a m’gawo lanu amakonda kufunsa ndiyeno wofalitsayo agwiritse ntchito Baibulo poyankha funsolo.
[Mawu a M’munsi]
a Mawu oyamba asapitirire mphindi imodzi, ndiyeno kambiranani mwa mafunso ndi mayankho.
b Mawu oyamba asapitirire mphindi imodzi, ndiyeno kambiranani mwa mafunso ndi mayankho.