Zilengezo
◼ Mabuku ogawira mu February: Chinsinsi cha Chimwemwe cha Banja. March: Kodi Baibulo Limaphunzitsa Chiyani Kwenikweni? Yesetsani kuyambitsa maphunziro a Baibulo. April ndi May: Tidzagawira magazini a Nsanja ya Olonda ndi Galamukani! Tidzayesetse kuyendera anthu atsopano achidwi amene anafika pa Chikumbutso ndiponso pankhani ya onse yapadera koma safika pa misonkhano ya mpingo nthawi zonse. Cholinga cha maulendo amenewa ndi kuyambitsa maphunziro a Baibulo ndi anthu amene sanayambe kuphunzira.
◼ Mwezi wa March ndi mwezi wabwino kwambiri kuchita upainiya wothandiza chifukwa choti uli ndi masiku asanu a Loweruka ndi Lamlungu.
◼ Mlembi ndi woyang’anira utumiki ayenera kuonanso ntchito ya apainiya okhazikika. Ngati ena zikuwavuta kukwanitsa maola awo, akulu ayenera kukonza zokumana nawo kuti awathandize.
◼ Nkhani ya onse yapadera ya nyengo ya Chikumbutso ya 2008 ili ndi mutu wakuti “Kodi Ndani Ali Woyenerera Kulamulira Anthu?” Onani zilengezo zofanana ndi zimenezi mu Utumiki Wathu wa Ufumu wa October 2007.
◼ Ziwerengero za lipoti la utumiki la October n’zotsika chifukwa chakuti mipingo 140 sinatumize malipoti awo. Chonde muziyesetsa kutumiza malipoti anu mwezi uliwonse kuti tizitumiza lipoti lolondola ku Bungwe Lolamulira.
◼ Oyang’anira Otsogolera Adziwe Izi: Nthawi zina makalata amene amatumizidwa ku mabungwe a akulu kuchokera ku nthambi amakhala ndi malangizo ofunika okhudza ntchito ya atumiki a mabuku kapena a magazini. Oyang’anira otsogolera afunika kuonetsetsa kuti malangizo amenewa aperekedwa kwa abalewa kalatayo ikangowerengedwa.