Kubwereza za M’sukulu ya Utumiki wa Mulungu
Mafunso otsatirawa mudzawakambirana pa Sukulu ya Utumiki wa Mulungu ya mlungu woyambira February 25, 2008. Woyang’anira sukulu adzatsogolera kubwereza nkhani zomwe zakambidwa m’kati mwa milungu ya January 7 mpaka February 25, 2008. Kubwerezaku kudzakhala kwa mphindi 30. [Dziwani izi: Pa funso lomwe kumapeto kwake silikusonyeza buku lililonse lomwe mwatengedwa nkhaniyo, ndiye kuti muyenera mufufuze nokha kuti mupeze mayankho ake.—Onani buku la Sukulu ya Utumiki, mas. 36-7.]
LUSO LA KULANKHULA
1. Kodi tiyenera kuchita chiyani kuti tithandize omvera athu kumvetsa malemba, ndipo n’chifukwa chiyani tifunika kuchita zimenezi? [be-CN tsa. 228 ndime 2 ndi 3]
2. Chifukwa chiyani n’kofunika kuti nkhani zathu zizikhala zophunzitsadi kanthu omvera, ndipo tingachite bwanji zimenezi? [be-CN tsa. 230 ndime 3 mpaka 5 ndi bokosi]
3. Kodi kufufuza kungathandize bwanji nkhani yathu kukhala yophunzitsadi kanthu omvera? [be-CN tsa. 231 ndime 1 mpaka 3]
4. Kodi tingatani kuti omvera athu aphunzirepo kanthu tikamawerenga malemba omwe akuwadziwa kale? [be-CN tsa. 231 ndime 4 mpaka 5]
5. N’chifukwa chiyani n’kofunika kufotokoza mokambirana malemba amene tawerenga? [be-CN tsa. 232 ndime 3 mpaka 4]
NKHANI NA. 1
6. N’chifukwa chiyani masiku ano ulaliki wa nyumba ndi nyumba ndi wofunika kwambiri kuposa kale? [od-CN tsa. 93 ndime 2]
7. Kodi tingakonzekeretse motani mitima yathu kuti tilandire malangizo operekedwa pa misonkhano yachikhristu? (2 Mbiri 20:33) [be-CN tsa. 13 ndime 4 mpaka tsa. 14 ndime 5]
8. Kodi makolo angatani kuti aphunzitse ana awo ‘nzeru za mmene angapezere chipulumutso’? (2 Tim. 3:15) [be-CN tsa. 16 ndime 3 ndi 4]
9. Pofufuza anthu oyenerera, kodi tingachite bwanji kuti tilalikire anthu amene sapezekapezeka panyumba? [od-CN tsa. 96 ndime 2 ndi 3]
10. Kodi n’chifukwa chiyani tiyenera kutsogolera anthu achidwi ku gulu la Yehova, ndipo tingachite bwanji zimenezi? [od-CN tsa. 99 ndime 2 mpaka tsa. 100 ndime 1]
KUWERENGA BAIBULO KWA MLUNGU NDI MLUNGU
11. Kodi kunena mawu achipongwe kwa anzathu posonyeza kukwiya n’koopsa kuposa kusunga chakukhosi? (Mat. 5:21, 22) [w08-CN 1/15 “Mawu a Yehova Ndi Amoyo, Mfundo Zazikulu za M’buku la Mateyo”]
12. Kodi Akhristu amakhala bwanji ndi ‘diso la kumodzi’? (Mat. 6:22, 23) [w06-CN 10/1 tsa. 29]
13. Kodi mfundo ya Yesu inali yotani pamene anafunsa ophunzira ake kuti: “Kodi mukuzindikira tanthauzo la zinthu zonsezi?” (Mat. 13:51, 52) [w08-CN 1/15 “Mawu a Yehova Ndi Amoyo, Mfundo Zazikulu za M’buku la Mateyo”]
14. N’chifukwa chiyani nthawi zambiri Yesu akachiritsa munthu ankamulamula kuti “asamuulule”? (Mat. 12:16) [w87 5/15 tsa. 9; cl-CN tsa. 93 ndi 94]
15. Kodi mfundo ya Yesu inali yotani pankhani ya “muyeso” umene munthu ‘akupimira’ anzake? (Maliko 4:24, 25) [w80 6/15 tsa. 12; gt-CN mutu 43]