Umboni wa Chikhulupiriro
1. Kodi ndi zinthu zosautsa zotani zimene Yesu ananeneratu?
1 Mtumwi Paulo anamvetsera mwachidwi pamene Yesu amafotokoza za kukhalapo kwake ndi mapeto a dongosolo lino la zinthu. Yesu ananeneratu za zinthu zosautsa zimene zidzachitikire anthu, monga nkhondo, njala, zivomezi ndi miliri. Kenako Yesu anati otsatira ake adzadedwa, adzaperekedwa ku chisautso ndi kuphedwa. Anatinso kudzauka aneneri onyenga omwe adzasocheretse anthu ambiri ndiponso kuti chikondi cha anthu ambiri chidzazirala.
2. Kodi n’chifukwa chiyani zili zochititsa chidwi kuti uthenga wabwino ukulalikidwa padziko lonse?
2 Pambuyo ponena zinthu zonsezi, atumwiwo ayenera kuti anadabwa kwambiri Yesu atawauza kuti uthenga wabwino wa Ufumu wa Mulungu udzalalikidwa padziko lonse, konse kumene kuli anthu. (Mat. 24:3-14) N’zochititsa chidwi kuona kuti ulosi umenewu ukukwaniritsidwa masiku ano. Ngakhale kuti tikukhala m’nthawi yoopsa kwambiri, Mboni za Yehova zikulalikira uthenga wabwino modzipereka. Pamene chikondi cha anthu ambiri chikuzirala, chikondi chathu chikukulirakulira. Ngakhalenso kuti tikudedwa ndi “mitundu yonse,” tikulalikirabe pafupifupi kwa anthu a mitundu yonse.
3. Kodi ndi ziwerengero zolimbikitsa zotani zimene mukuona pa lipoti la padziko lonse?
3 N’zolimbikitsa kwambiri kuonanso zimene Mboni za Yehova zachita m’chaka cha utumiki chathachi, monga mmene tchati cha patsamba 3 mpaka 6 chikusonyezera. Kwa zaka 16 zotsatizana, Mboni za Yehova zakhala zikuthera maola opitirira 1 biliyoni pachaka m’ntchito yolalikira ndi kupanga ophunzira. Umenewu ndi umboni wa chikhulupiriro chimene Mboni za Yehova zili nacho. Apainiya anawonjezeka ndi 8 peresenti, ofalitsa ndi 3.1 ndipo maphunziro a Baibulo ndi 4.4 peresenti. Chiwerengero cha obatizidwa chinawonjezereka ndi 20.1 peresenti kuposa chaka cha utumiki chathachi. N’zosangalatsa kwabasi kuona kuti anthu pafupifupi 7 miliyoni akutumikira Yehova mokhulupirika. Sitinakhalepo ndi chiwerengero chachikulu chonchi m’mbuyo monsemu. Mukamaona tchatichi, n’chiyani chimene chikukulimbikitsani kwambiri?
4. Kodi munthu wina analimbana ndi vuto lotani akufuna kubatizidwa?
4 Ngakhale kuti ziwerengerozi pazokha n’zosangalatsa, tisaiwale kuti zapezeka chifukwa cha anthu amene asonyeza chikhulupiriro. Taganizirani za chitsanzo chimodzi. Guillermo anabadwa m’chaka cha 1935 ndipo anakulira ku Bolivia. Ali ndi zaka 9, anayamba kugwira ntchito m’minda ya mbewu za koka, zomwe amapangira mankhwala osokoneza bongo. Kuyambira ali wamng’ono ankatafuna masamba a koka kuti asamamve kutopa akamagwira ntchito yake ya kalavulagaga. Kenako anayamba mowa ndi fodya. Atayamba kuphunzira za zimene Yehova amafuna kuti iye azichita, Guillermo analeka kusuta ndi kuledzera. Koma vuto lake lalikulu linali kuleka chizolowezi cham’gonagona chotafuna masamba a koka. Ankapemphera mosatopa mpaka anasiya chizolowezi chimenechi. Anasiya zinthu zonse zoipa n’kubatizidwa. Guillermo anati: “Pakali pano ndine munthu wosangalala ndipo ndimaona kuti ndine woyera.”
5. Kodi inuyo muli ndi cholinga chotani?
5 Yehova amakonda anthu. Cholinga chake n’chakuti anthu onse alape. (2 Pet. 3:9) Ifenso tili ndi cholinga chimenechi. Tiyeni tipitirize kuchita zonse zimene tingathe kuti tithandize anthu a mtima wabwino kudziwa ndi kukonda Yehova monga mmene ife tikuchitira.