Kubwereza za M’Sukulu ya Utumiki wa Mulungu
Mafunso otsatirawa mudzawakambirana pa Sukulu ya Utumiki wa Mulungu ya mlungu woyambira February 23, 2009. Woyang’anira sukulu adzatsogolera kubwereza nkhani zomwe zakambidwa m’kati mwa milungu ya January 5 mpaka February 23, 2009. Kubwerezaku kudzakhala kwa mphindi 20.
1. Popeza kuti Mulungu analenga zounikira tsiku lachinayi, kodi kuwala kumene iye analamula kuti kuchitike pa tsiku loyamba kunachokera kuti? (Gen. 1:3, 16) [w04-CN 1/1 tsa. 28 ndime 5]
2. Kodi n’chifukwa chiyani Yehova sanamuuze Nowa kuti agonjetse dziko lapansi ngati mmene anamuuzira Adamu? (Gen. 9:1) [it-2 tsa. 1095 ndime 6]
3. Kodi pangano la Abrahamu linayamba liti, ndipo linali loti ligwira ntchito kwa nthawi yaitali bwanji? (Gen. 12:1-4) [w04-CN 1/15 tsa. 26 ndime 4; w01-CN 8/15 tsa. 17 ndime 13]
4. Kodi n’chiyani chikusonyeza kuti Nimrode ndiponso anthu amene ankamutsatira analephera ‘kudzipangira okha dzina.’? (Gen. 11:4) [w98-CN 3/15 tsa. 25]
5. Popeza kuti lemba la 2 Petulo 2:7, limanena kuti Loti ndi munthu “wolungama,” n’chifukwa chiyani iye ankafuna kupereka ana ake akazi kwa anthu achiwawa? (Gen. 19:8) [w05-CN 2/1 tsa. 25 ndime 15-16; w04-CN 1/15 tsa. 27 ndime 3]
6. Popeza kuti amuna oopa Mulungu ayenera kusamalira banja lawo, n’chifukwa chiyani Abulahamu anachotsa Hagara ndi Isimaeli pakhomo pake n’kuwalola kupita ku chipululu? (Gen. 21:10-21; 1 Tim. 5:8) [w88-CN 2/15 tsa. 31]
7. Kodi tikuphunzira chiyani pa zimene Eliezere anachita popezera Isake mkazi wokonda Yehova? (Gen. 24:14, 15, 17-19, 26, 27) [w97-CN 1/1 tsa. 31 ndime 2]
8. Kodi maloto amene Yakobo analota, pamene anaona angelo ‘akukwera ndi kutsika’ makwerero ankatanthauza chiyani? (Gen. 28:10-13) [w03-CN 10/15 tsa. 29 ndime 1; it-2 p. 189]
9. Kodi n’chifukwa chiyani Rakele ankafuna kwambiri kutenga zipatso za mankhwala a chikondi a mwana wa Leya? (Gen. 30:14, 15) [w04-CN 1/15 tsa. 28 ndime 6]
10. Kodi zimene Yakobo anachita pothetsa chidani ndi Esau, zingatithandize bwanji? (Gen. 33:3, 4) [g82-E 2/22 tsa. 19 ndime 8-10]