Ndandanda ya Mlungu wa February 23
MLUNGU WOYAMBIRA FEBRUARY 23
□ Phunziro la Baibulo la Mpingo:
cl-CN mutu 15 ndime 1-7
□ Sukulu ya Utumiki wa Mulungu:
Kuwerenga Baibulo: Genesis 32-35
Kubwereza za m’Sukulu ya Utumiki wa Mulungu
□ Msonkhano wa Utumiki:
Mph. 5: Zilengezo. Tchulani mabuku ogawira m’mwezi wa March.
Mph. 10: Konzekerani Kugawira Nsanja ya Olonda ya March 1 ndi Galamukani! ya March. Pambuyo pofotokoza mwachidule zimene zili m’magaziniwo, pemphani omvera kuti atchule nkhani zimene zingasangalatse anthu a m’gawo lanu ndiponso chifukwa chake. Pogwiritsa ntchito nkhani za m’magaziniwo, pemphani omvera kuti atchule funso limene angafunse kuti ayambitse makambirano komanso lemba limene angawerenge asanagawire magaziniwo. Malizani ndi chitsanzo chosonyeza mmene tingagawirire magazini iliyonse.
Mph. 10: Zosowa za pampingo.
Mph. 10: Kodi Mukugwiritsa Ntchito Kabuku ka Kusanthula Malemba Tsiku ndi Tsiku? Nkhani ndi kukambirana ndi omvera kuchokera pa mawu oyamba a m’kabuku ka Kusanthula Malemba Tsiku ndi Tsiku—2009. Kambiranani ubwino wokhala ndi nthawi yowerenga Lemba la tsiku ndi ndemanga yake tsiku lililonse. Pemphani omvera kuti afotokoze za nthawi imene amachita lemba latsiku, mmene amachitira ndiponso phindu limene apeza.