Zilengezo
◼ Mabuku ogawira mu April ndi May: Gawirani magazini a Nsanja ya Olonda ndi Galamukani! Pochita maulendo obwereza kwa anthu achidwi, komanso anthu amene anafika pa Chikumbutso kapena zochitika zina zampingo, koma safika pa misonkhano ya mpingo nthawi zambiri, tidzayesetse kugawira buku la Kodi Baibulo Limaphunzitsa Chiyani Kwenikweni? Cholinga cha maulendowa chidzakhale kuyambitsa phunziro la Baibulo ndi buku limeneli. June: Gawirani buku la Kodi Baibulo Limaphunzitsa Chiyani Kwenikweni? Ngati eninyumba ali nalo kale bukuli, ofalitsa angagawire buku lililonse la masamba 192, lomwe pepala lake limasintha mtundu m’kupita kwa nthawi kapena lomwe linasindikizidwa chaka cha 1992 chisanafike.
◼ Tidzakhala ndi ntchito yaikulu yolengeza misonkhano ya chigawo ndi ya mayiko ya m’chaka cha 2009 yomwe idzachitike padziko lonse. Ofalitsa adzakhala ndi mwayi wogawira kapepala kapadera kwa anthu a m’gawo lawo. Ntchito imeneyi idzayamba kutatsala milungu itatu kuti msonkhano umene mpingo wanu udzapite uchitike.
◼ Mabaji a msonkhano adzatumizidwa kwa ofalitsa onse kudzera ku mipingo. Anthu amene adzapite ku msonkhano wa mayiko adzagwiritsanso ntchito baji yomweyo.