Ndandanda ya Mlungu wa May 11
MLUNGU WOYAMBIRA MAY 11
□ Phunziro la Baibulo la Mpingo:
cl-CN mutu 19 ndime 1-8
□ Sukulu ya Utumiki wa Mulungu:
Kuwerenga Baibulo: Eksodo 27–29
Na. 1: Eksodo 29:1-18
Na. 2: Mmene Tingakhalire Osangalala (lr-CN mutu 17)
Na. 3: Kukhulupirika Kolakwika Ndiponso Kuopsa Kwake
□ Msonkhano wa Utumiki:
Mph.5: Zilengezo.
Mph.10: Kodi Mungachite Upainiya Wothandiza M’miyezi Ikubwerayi? Nkhani yokambirana ndi omvera yochokera m’buku la Gulu, masamba 112-113. Fotokozani zinthu zofunika kuti munthu ayenerere kuchita upainiya wothandiza ndipo pemphani amene anachitapo upainiya wothandiza m’mbuyomu kuti afotokoze madalitso amene anapeza.
Mph.10: Konzekerani ndi Banja Lanu Kuchita Nawo Utumiki. Mwachidule, funsani abale awiri omwe ndi mitu ya mabanja amene amapatula nthawi pamene akuchita Kulambira kwa Pabanja kuti akonzekere utumiki. Kodi amakonzekera bwanji, ndipo zimenezi zawathandiza motani? Banja limodzi lichite chitsanzo chosonyeza mmene amachitira pokonzekera kugawira magazini.
Mph.10: “Phunzitsani M’njira Yosavuta.” Kambiranani mwa mafunso ndi mayankho.