Zilengezo
◼ Mabuku ogawira mu May: Magazini a Nsanja ya Olonda ndi Galamukani! Mukamachita maulendo obwereza kwa anthu achidwi, ngakhalenso amene anafika pa Chikumbutso kapenanso pa misonkhano ina koma safika pa misonkhano ya mpingo nthawi zonse, yesetsani kuwagawira buku Kodi Baibulo Limaphunzitsa Chiyani Kwenikweni? ndi cholinga choyambitsa phunziro la Baibulo. June: Kodi Baibulo Limaphunzitsa Chiyani Kwenikweni? July ndi August: Mungagwiritse ntchito kabuku kalikonse ka masamba 32 komwe muli nako pa timabuku totsatirati: Kodi Mulungu Amatisamaliradi?, Pamene Munthu Amene Mumakonda Amwalira ndi Mizimu ya Akufa—Kodi Ingakuthandizeni Kapena Kukuvulazani? Kodi Iyo Ilikodi?
◼ Ngati mukuganiza zokapezeka pa misonkhano ya mpingo, ya dera kapena ya chigawo ku dziko lina, mafunso anu okhudza masiku, nthawi ndi malo a misonkhanoyi, muyenera kuwatumiza ku ofesi ya nthambi imene imayang’anira ntchito m’dzikolo. Maadiresi a maofesi anthambi mungawapeze patsamba lomaliza la Yearbook ya chaka chino.
◼ Tili ndi mabaundi voliyumu a Nsanja ya Olonda a 2008 a chinenero cholankhula ndi manja cha ku America. Motero, tikulimbikitsa mipingo ndiponso timagulu ta Chinenero Cholankhula ndi Manja kuitanitsa zinthu zimenezi.