Ndandanda ya Mlungu wa June 1
MLUNGU WOYAMBIRA JUNE 1
□ Phunziro la Baibulo la Mpingo:
cl-CN mutu 20 ndime 1-12
□ Sukulu ya Utumiki wa Mulungu:
Kuwerenga Baibulo: Eksodo 38-40
Na. 1: Eksodo 40:1-19
Na. 2: Kodi Nthawi Zonse Mumafuna Kukhala Woyamba? (lr-CN mutu 20)
Na. 3: Kodi Anthu Onse Adzachiritsidwa? (rs-CN tsa. 169 ndime 5 mpaka tsa. 170 ndime 2)
□ Msonkhano wa Utumiki:
Mph.5: Zilengezo.
Mph.10: Thandizani Ena Kupita Patsogolo. Nkhani yokambirana ndi omvera yochokera m’buku la Sukulu ya Utumiki, pakamutu koyambira pa tsamba 187. Mwachidule funsani mpainiya kapena wofalitsa amene wathandiza atsopano kupita patsogolo.
Mph.10: Zosowa za pampingo.
Mph.10: Kodi Tinachita Zotani? Nkhani yokambirana ndi omvera. Yamikirani mpingo chifukwa cha kuwonjezera utumiki panyengo ya Chikumbutso, ndipo tchulani zimene mpingo unachita. Pemphani omvera kufotokoza zimene anakumana nazo pogawira timapepala toitanira anthu ku Chikumbutso kapena potumikira monga mpainiya wothandiza.