Watchtower LAIBULALE YA PA INTANETI
Watchtower
LAIBULALE YA PA INTANETI
Chichewa
  • BAIBULO
  • MABUKU
  • MISONKHANO
  • km 9/09 tsamba 1
  • Kodi Mungayankhe Bwanji?

Palibe Vidiyo.

Pepani vidiyoyi ikukanika kutsegula.

  • Kodi Mungayankhe Bwanji?
  • Utumiki Wathu wa Ufumu—2009
  • Nkhani Yofanana
  • Kuwongolera Mayankho Anu
    Buku Lolangiza la Sukulu ya Utumiki Wateokalase
  • Dziŵani Mayankhidwe Oyenera
    Pindulani ndi Sukulu ya Utumiki wa Mulungu
  • Tsanzirani Wopanga Ophunzira Waluso
    Nsanja ya Olonda—2007
  • Kugwiritsa Ntchito Mafunso Mwaluso
    Pindulani ndi Sukulu ya Utumiki wa Mulungu
Onani Zambiri
Utumiki Wathu wa Ufumu—2009
km 9/09 tsamba 1

Kodi Mungayankhe Bwanji?

1. N’chifukwa chiyani tiyenera kutengera chitsanzo cha Yesu tikafunsidwa mafunso?

1 Yesu ankadziwa kwambiri kuyankha mafunso ndipo ngakhale masiku ano anthu amachita chidwi ndi mmene Yesu ankayankhira mafunso. Ifenso tingatengere chitsanzo chake anthu akatifunsa mafunso osiyanasiyana mu utumiki.—1 Pet. 2:21.

2. Kodi n’chiyani chingatithandize kuti tiziyankha anthu mogwira mtima?

2 Muzimvetsera Kaye: Yesu akafunsidwa funso, ankamvetsera kuti adziwe cholinga cha funsolo. Nthawi zina tingafunike kufunsa mafunso kuti tidziwe zimene munthu amene watifunsa funsoyo akuganiza. Mwachitsanzo, mwina chifukwa choona kuti sitichita nawo Khirisimasi anthu angatifunse kuti, “Kodi mumakhulupirira Yesu?” Ngati titadziwa chifukwa chimene afunsira funsolo, tingawayankhe mogwira mtima.—Luka 10:25-37.

3. Kodi ndi zinthu ziti zimene zingatithandize kupeza mayankho ogwira mtima a m’Malemba?

3 Muzigwiritsa Ntchito Baibulo: Zimathandiza kwambiri kugwiritsa ntchito Baibulo poyankha mafunso. (2 Tim. 3:16, 17; Aheb. 4:12) Buku la Kukambitsirana ndiponso “Nkhani za m’Baibulo Zokambirana” zimene zili mu Baibulo la Dziko Latsopano Lomasulira Malemba Achigiriki Achikhristu zimathandiza kwambiri kuti tiziyankha molondola. Ngakhale ngati munthuyo sakhulupirira Baibulo, tingathebe kumufotokozera mwaluso zimene Malemba amaphunzitsa. Tiyenera kulimbikitsa munthuyo kuganizira mozama mfundo zothandiza zopezeka m’Baibulo. Tikatengera chitsanzo cha Yesu, mayankho athu adzakhala aulemu, ochititsa chidwi ndiponso opindulitsa ngati “zipatso zagolidi m’nsengwa zasiliva.”—Miy. 25:11.

4. Kodi ndi nthawi iti yomwe sitiyenera kuyankha mafunso onse?

4 Kodi Tiyenera Kuyankha Funso Lililonse? Ngati sitikudziwa yankho la funso limene tafunsidwa, tisachite manyazi kunena kuti: “Sindikudziwa, koma ndikhoza kukafufuza n’kudzakuyankhani.” Zimenezi zingasonyeze kuti ndife odzichepetsa ndiponso tikumuganizira munthuyo, ndipo angatiuze kuti tidzabwerenso. Tikazindikira kuti munthuyo ndi wotsutsa ndipo akungofuna kuti tizikangana naye, tiyenera kutengera chitsanzo cha Yesu mwa kungosiya kulankhula naye. (Luka 20:1-8) Tikazindikiranso kuti munthu amene tikukambirana naye alibe chidwi chofuna kudziwa choonadi, mwaulemu tiyenera kusiya kukambirana naye kuti tisataye nthawi yomwe tingaigwiritse ntchito kufufuza anthu oyenerera.—Mat. 7:6.

5. Kodi Yesu asonyeza chitsanzo chotani pankhani yoyankha mafunso?

5 Yesu ankadziwa kuti kudalira Yehova n’kofunika kwambiri kuti akwaniritse ntchito yake ‘yochitira umboni choonadi,’ imene inaphatikizapo kuyankha mafunso a anthu amene amafuna kudziwadi choonadi. (Yoh. 18:37) Nafenso tingathe kutengera chitsanzo cha Yesu poyankha mafunso a anthu amene ali ndi “maganizo oyenerera moyo wosatha.”—Mac. 13:48.

    Mabuku a Chichewa (1974-2025)
    Tulukani
    Lowani
    • Chichewa
    • Tumizirani Ena
    • Zimene Mumakonda
    • Copyright © 2025 Watch Tower Bible and Tract Society of Pennsylvania
    • Zoyenera Kutsatira
    • Nkhani Yosunga Chinsinsi
    • Privacy Settings
    • JW.ORG
    • Lowani
    Tumizirani Ena