Ndandanda ya Mlungu wa October 5
MLUNGU WOYAMBIRA OCTOBER 5
□ Phunziro la Baibulo la Mpingo:
cl-CN mutu 27 ndime 1-7
□ Sukulu ya Utumiki wa Mulungu:
Kuwerenga Baibulo: Deuteronomo 1-3
Na. 1: Deuteronomo 2:1-15
Na. 2: Kodi Malemba a “M’Chipangano Chatsopano” Amasonyeza Kuti Anthu Adzalandira Moyo Wosatha Padziko Lapansi? (rs-CN tsa. 207 ndime 1–tsa. 208 ndime 1)
Na. 3: Kodi Ndani Adzauka kwa Akufa? Nanga Adzakhala Kuti? (lr-CN mutu 36)
□ Msonkhano wa Utumiki:
Mph. 5: Zilengezo.
Mph. 10: Kodi Mukufuna Kudziwa Choonadi? Nkhani yokambirana ndi omvera. Funsani omvera kuti afotokoze mafunso a m’kapepalaka amene anthu ambiri m’gawo lanu akufuna kudziwa mayankho ake. Chitani chitsanzo chosonyeza mmene tingagwiritsirire ntchito kapepalaka kuti tiyambitse phunziro la Baibulo.
Mph. 10: Zosowa za pampingo.
Mph. 10: Lalikirani Anthu Achinenero China. Nkhani yokambirana ndi omvera. Kambiranani mfundo zitatu zimene zili patsamba 2 m’kabuku kakuti Uthenga Wabwino wa Anthu a Mitundu Yonse. Ndipo pemphani wofalitsa kuti achite chitsanzo chosonyeza mmene mungagwiritsire ntchito kabukuka m’gawo lanu.