Watchtower LAIBULALE YA PA INTANETI
Watchtower
LAIBULALE YA PA INTANETI
Chichewa
  • BAIBULO
  • MABUKU
  • MISONKHANO
  • km 9/09 tsamba 4
  • Zilengezo

Palibe Vidiyo.

Pepani vidiyoyi ikukanika kutsegula.

  • Zilengezo
  • Utumiki Wathu wa Ufumu—2009
Utumiki Wathu wa Ufumu—2009
km 9/09 tsamba 4

Zilengezo

◼ Mabuku ogawira mu September: Gawirani buku lakuti Kodi Baibulo Limaphunzitsa Chiyani Kwenikweni? Ngati n’kotheka, ofalitsa ayenera kuyesetsa kuyambitsa phunziro la Baibulo paulendo woyamba. October: Gawirani magazini a Nsanja ya Olonda ndi Galamukani! Anthu amene asonyeza chidwi agawireni ndi kukambirana nawo kapepala kakuti Kodi Mukufuna Kudziwa Choonadi? November: Gawirani buku lakuti Kodi Baibulo Limaphunzitsa Chiyani Kwenikweni? December: Gawirani buku lakuti Munthu Wamkulu Woposa Onse Amene Anakhalako. Ngati mwapeza ana panyumba gawirani buku lakuti Phunzirani kwa Mphunzitsi Waluso.

◼ Nkhani yapadera ya panyengo ya Chikumbutso cha 2010 idzaperekedwa mlungu woyambira April 12, 2010. Mutu wa nkhaniyi udzalengezedwa m’tsogolo. Mipingo imene idzakhale ndi woyang’anira dera kapena msonkhano wapadera mlungu umenewo adzakhala ndi nkhaniyi mlungu wotsatira. Mpingo uliwonse usadzakhale ndi nkhaniyi pasanafike pa April 12.

◼ Nthawi zambiri mpingo watsopano umapangidwa kuchokera ku mpingo wakale. Komabe mwina zinthu zimene ofesi ya nthambi imatumiza (monga timapepala toitanira anthu ku Chikumbutso, Kusanthula Malemba Tsiku ndi Tsiku, timapepala toitanira anthu ku msonkhano wachigawo kapena zinthu zina) zingakhale zitatumizidwa kale ku mpingo wakalewo, mpingo watsopanowo usanagawidwe kapena utangogawidwa kumene. Pofuna kutsimikizira kuti mpingo watsopanowo uli ndi zinthu zofunikirazo, uyenera kukatenga zinthuzo ku mpingo wakalewo. Mpingo wakalewo uyeneranso kuonetsetsa kuti wapereka zinthuzo ku mpingo watsopanowo.

    Mabuku a Chichewa (1974-2025)
    Tulukani
    Lowani
    • Chichewa
    • Tumizirani Ena
    • Zimene Mumakonda
    • Copyright © 2025 Watch Tower Bible and Tract Society of Pennsylvania
    • Zoyenera Kutsatira
    • Nkhani Yosunga Chinsinsi
    • Privacy Settings
    • JW.ORG
    • Lowani
    Tumizirani Ena