Ndandanda ya Mlungu wa October 12
MLUNGU WOYAMBIRA OCTOBER 12
□ Phunziro la Baibulo la Mpingo:
cl-CN mutu 27, ndime 8 mpaka 15
□ Sukulu ya Utumiki wa Mulungu:
Kuwerenga Baibulo: Deuteronomo 4-6
Na. 1: Deuteronomo 4:15-28
Na. 2: Kukumbukira Yehova ndi Mwana Wake (lr-CN mutu 37)
Na. 3: Kodi Ndi Nthawi Iti Pamene Tinganene Kuti Zapang’ono Zipambana Zambiri? (Miy. 15:16)
□ Msonkhano wa Utumiki:
Mph. 5: Zilengezo.
Mph. 10: Kuchititsa Maphunziro a Baibulo a Panyumba. Nkhani yochokera m’buku la Gulu, tsamba 98, ndime 1 mpaka tsamba 99, ndime 1. Pemphani ofalitsa kuti afotokoze mwachidule chisangalalo chimene akhala nacho pophunzitsa wina choonadi.
Mph. 10: Buku Logawira mu October. Chitani zitsanzo ziwiri. Pa chitsanzo chimodzi mufunse funso limene lidzayankhidwe pa ulendo wobwereza. M’chitsanzo chinacho sonyezani mmene tingayambitsire phunziro la Baibulo pa ulendo woyamba. Pambuyo pa chitsanzo chilichonse kambiranani mwachidule zimene tikuphunzira pa chitsanzocho.
Mph. 10: “Kodi Ndinu Wokonzeka Kuchita Ulaliki Wamwamwayi?” Kambiranani mwa mafunso ndi mayankho.