Ndandanda ya Mlungu wa October 19
MLUNGU WOYAMBIRA OCTOBER 19
□ Phunziro la Baibulo la Mpingo:
cl-CN mutu 27, ndime 16 mpaka 22, ndi bokosi patsamba 279
□ Sukulu ya Utumiki wa Mulungu:
Kuwerenga Baibulo: Deuteronomo 7-10
Na. 1: Deuteronomo 9:1-14
Na. 2: Chifukwa Chake Tiyenera Kukonda Yesu (lr-CN mutu 38)
Na. 3: Kodi Ndi Angati Amene Baibulo Limati Adzapita Kumwamba? (rs-CN tsa. 208 ndime 2 ndi 3)
□ Msonkhano wa Utumiki:
Mph. 5: Zilengezo.
Mph. 15: Kufufuza Kungatithandize Kumvetsa Zinthu. Nkhani yochokera m’buku la Sukulu ya Utumiki pa mfundo za patsamba 33 mpaka pakamutu komwe kali patsamba 34. Fotokozani m’njira yosonyeza kuti wofalitsa akulimbikitsa wophunzira Baibulo mwa kum’sonyeza mmene angafufuzire zinthu kuti alimbitse chikhulupiriro chake ndiponso kuti akonzekere utumiki. Kenako chitani chitsanzo chosonyeza mmene wofalitsa angathandizire wophunzira Baibulo kumvetsa phindu la kufufuza.
Mph. 15: “Khalanibe M’chikondi cha Mulungu.” Nkhani yokambirana mwa mafunso ndi mayankho. Tchulani mbali zapadera za bukuli. Limbikitsani onse kuti azidzapezeka pamisonkhano nthawi zonse ndi kutenga nawo mbali mokwanira.