Zilengezo
◼ Mabuku ogawira mwezi wa November: Kodi Baibulo Limaphunzitsa Chiyani Kwenikweni? Ngati eninyumba ali nalo kale bukuli, ofalitsa angagawire buku lililonse la masamba 192, lomwe pepala lake limasintha mtundu m’kupita kwa nthawi kapena lomwe linasindikizidwa chaka cha 1995 chisanafike. December: Munthu Wamkulu Woposa Onse Amene Anakhalako. Ngati anthu anena kuti ali ndi ana, agawireni buku la Phunzirani kwa Mphunzitsi Waluso. January: Kodi Baibulo Limaphunzitsa Chiyani Kwenikweni? February: Gawirani buku la Chinsinsi cha Chimwemwe cha Banja.