Ndandanda ya Mlungu wa May 10
MLUNGU WOYAMBIRA MAY 10
□ Phunziro la Baibulo la Mpingo:
□ Sukulu ya Utumiki wa Mulungu:
Kuwerenga Baibulo: 2 Samueli 4-8
Na. 1: 2 Samueli 6:1-13
Na. 2: Kodi Timadziwa Chiyani pa Nkhani ya Tsiku la Valentaini, Tsiku la Anakubala Ndiponso Zikondwerero Zosonyeza Kukonda Dziko Lako? (rs tsa. 245 ndime 3–tsa. 246 ndime 2)
Na. 3: N’chifukwa Chiyani Umbombo Uli Kupembedza Mafano? (Aef. 5:5)
□ Msonkhano wa Utumiki:
Mph. 5: Zilengezo.
Mph. 10: Athandizeni Anthu a M’gawo Lanu pa Zosowa Zawo. Nkhani yokambirana ndi omvetsera yochokera m’buku la Sukulu ya Utumiki, tsamba 188, ndime 4, mpaka kumapeto kwa tsamba 189. Funsani mwachidule wofalitsa wina amene anapita patsogolo chifukwa choti abale kapena alongo ena anam’sonyeza chidwi.
Mph. 10: Nyumba ya Ufumu Yosamalidwa Bwino Imalemekeza Yehova. Nkhani yoti ikambidwe ndi mkulu. Yehova ndi Mulungu woyera, choncho anthu akenso ayenera kuona kuti ukhondo ndi wofunika kwambiri. (Eks. 30:17-21; 40:30-32) Tikamaonetsetsa kuti malo athu olambirira ndi aukhondo komanso osamalidwa bwino, timalemekeza Yehova. (1 Pet. 2:12) Funsani m’bale amene amatsogolera ntchito yosamalira ndi kukonza zinthu zowonongeka pa Nyumba ya Ufumu yanu kuti afotokoze dongosolo limene lilipo pampingopo. Fotokozani chitsanzo cha kwanuko kapena chitsanzo chopezeka m’mabuku athu chosonyeza kuti anthu a m’deralo anakopeka ndi uthenga wathu chifukwa choti Nyumba ya Ufumu imaoneka bwino. Limbikitsani onse kuti azithandiza pa ntchito yosamalira Nyumba ya Ufumu.
Mph. 10: “Uthenga Wabwino Uwu Udzalalikidwa.” Nkhani ya mafunso ndi mayankho.